KODI NDINGAPEZE MPINGO WA
MULUNGU LERO

Mulungu, nthawi zambiri, wapereka uthenga wapadera kuti akathetse zosowa zosiyana-siyana za mibadwo yosiyana-siyana: Uthenga wothandiza Adamu ndi Hava, pamene tchimo lidaononga dziko lawo, uthenga ku dziko lapansi chisanadze chigumula, uthenga kwa ana a Israyeli. Pamene Asiliya ndi a ku Babulo adawaopseza iwo Yesu adabwera ndi uthenga wapadera wa mbadwo wake, ndi Mulungu wapereka uthenga wa padera wa nthawi yathu ino. Mutu wakhumi ndi chiwiri ndi wa khumi ndi chinayi wa Chibvumbulutso ukunena mwachidule uthenga wa Mulungu wapadera kwa ife lero. Mu phunziro lotsogolera ndi lina lotsatiralo, tiona za uthenga umenewu.

1. MPINGO WOKHAZIKITSIDWA NDI YESU

Moyo ndi ziphunzitso za Yesu zidakhazikitsa umodzi wa chikhulupiriro ndi kupembedzera pamodzi mu mpingo wa atumwi womwe iye adayambitsa. Atumwiwo adayambitsa ubale ndi Khristu, weni-weni. Paulo akuuyerekeza ubalewo, pouwona, ndi chiyanjano cha ukwati.

"Pakuti ndinapalitsana ubwenzi mwamuna modzi, kuti ndikalangiza inu ngati namwali woyera mtima mwa Kristu." - 2 Akorinto 11:2.

Monga mwa kulongosola kwa Paulo, mpingo wa Mulungu uli ngati namwali wangwiro, woyera, mkwatibwi wa Khristu, choimirira cha mpingo wake wokondedwa wa Khristu. Mu chipangano chakale, chizindikiro chomwechonso chikugwiritsidwa ntchito kusonyeza za Israyeli, mtundu wa anthu wosankhidwa wa Mulungu. Mulungu anati kwa Israyelo "monga mkwatibwi udandikonda Ine" (Yeremiya 2:2) "ndiri mwamuna wako" (Yeremiya 3:14). Bukhu la Chibvumbulutso likunenanso za mpingo monga ngati mkazi.

"Ndipo chizindikiro chachikuru chinaoneka m'mwamba; mkazi wovekedwa dzuwa, ndi mwezi kumapazi ace, ndi pamutu pace korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri." - Chibvumbulutso 12:1.

(1) Mkaziyu wavekedwa "ndi dzuwa." Izi zikutiganiziritsa mpingo wowala monga dzuwa chifukwa chovala Khristu ndi ulemerero wake. Yesu, "kuwala kwa dziko lapansi" (Yohane 8:12), akuwalira mwa wokhulupira aliyense mu mpingo wake, ndi wonse amakhala "kuwala kwa pa dziko lapansi" (Mateyu 5:14).

(2) Mkaziyu wavekedwanso "mwezi kumapazi kwake." Mwezi umasonyezera kuwala kotengedwa kuchokera kwina kwake, kwa uthenga mu nsembe ndi ziphunzitso za anthu ake a Mulungu mu nthawi ya chipangano chakale mwezi wokhala "pamapazi pake" ukuganiziritsa za kuwala kotengedwa kwina kwa uthenga wabwino kumene kuimirira utumiki wa Yesu Khristu.

(3) Mkaziyu alinso ndi "korona wa nyenyezi khumi ndi ziwiri pamutu pake." Nyenyezi zimaimira mwachinduji atumwi khumi ndi awiri, amuna omvera omwe umboni wawo wapa Yesu umawala kwakukuru mpaka lero. Momveka bwino, maonekedwe a mkaziyo akulongosoledwa ndiYohane a kusonyezera kuti Yohane uyu adali ndi maganizo a kusinthika kuchokera ku kukhala anthu a Mulungu, Israyeli, wa mu chipangano chakale, kunka ku mpingo wa Khristu wa chipangano chatsopano umene Yesu Khristu adaukhazikitsa. Dzuwa, mwezi, ndi nyenyezi zikutsimikizira uthenga
wa kupatsa moyo wa mpingo wa Mulungu mu utumiki wakugawana uthenga
wabwino.

2. KUGONJETSEDWA KWA SATANA

Kudza kwa mkazi kukubweretsa zochitika zambiri:

"Ndipo anali ndi pakati; ndipoapfuula ali mkubala, ndi kumva zowawa za kubala. Ndipo chioneka chizindikiro cina m'mwamba, taonani chinjoka, chofiira, chachikuru, cakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri, ndi nyanga khumi, ndi pamutu pace nduwira zachifumu zisanu ndi ziwiri. Ndipo mchira wace uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi za m'mwamba, nuziponya padziko. Ndipo chinjoka chinaimirira pamaso pa mkazi akuti abale, kuti, akabala, icho chikalikwira mwana wace. Ndipo anabala mwana wamwamuna, amene adzaweruza mitundu yonse ndi ndodo yachitsulo; ndipo anakwatulidwa mwana wace amuke kwa Mulungu, ndi kumpando wachifumu wace." - Chibvumbulutso 12:2-5.

Anthu atatu ofunikira ndiwo ali muzochitikazi:
(i) Mkazi; yemwe waonetsedwa kale ngati mpingo wa Mulungu
(ii) Mwana wamwamuna, wobadwa mwa mkaziyu "watengedwe kupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wachifumu" ndipo tsiku lina "adzalamulira mitundu yonse" Yesu ndiye mwana yekhayo adabadwa mu dziko lino lapansi, natengedwa kunka ku mpando wachifumu wa Mulungu ndipo tsiku lina adzalamulira mitundu yonse.
(iii) Chinjoka chaimira mdirekezi, kapena satana, "ndipo munali nkhondo m'mwamba Mikayeli ndi angelo ace akucita nkhondo ndi chinjoka, chinjokanso ndi angelo ace chinacita nkhondo, ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo ao m'mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikuru, njoka yokalamba yo, iye wochedwa mdierekezi ndi satana, wonyenga wa dziko lonse, chinaponye-dwa pansi ku dziko, ndi angelo ace anaponyedwa naye pamodzi." -
Chibvumbulutso 12:7-9.

Izi zikuonekera bwino pamene timvetsetsa zizindikiro ndi matanthauzo ake, pamene mdierekeze ndi angelo ake "adasiya malo ao m'mwamba" adaponyedwa kudziko lapansi pamene Yesu anabadwira m'dziko lino lapansi, mdierekezi adafuna kuti amuphe Iye, mwana wa mwamunayo. Atangobadwa kumene, koma adalephera," ndipo Yesu adakwatulidwa" kupita kumpando wake wachifumu wa Mulungu. Ndipo tsopano satana ananka namaononga mpingo wa Khristu womwe Khristuyo adaukhazikitsa. Mtumwi Yohane, yemwe adalemba Chibvumbulutso, adaona za nkhondo yaikuru pakati pa Khristu ndi satana ikubwera ku dziko lapansi. Pamene nkhondoyi ikufika pachimake peni-peni pa kufa kwa Khristu Yesu kwa kupachikidwa, Yohane akumva mpfuu wa mawu ochokera kumwamba.

"Ndipo ndinamva mawu akuru m'mwamba, nanena, Tsopano cafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu wa Mulungu wathu ndi ulamuliro wa Khristu wace; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wa kuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku." - Chibvumbulutso 12:10.

Yesu adagonjetsa satana pa mtanda paja moonekeratu. Ndipo adatsimikizira kukhalako kwake kwa chikonzetsero cha "Chipulumutso" ndi kupereka "mphamvu" zakukanira machenjerero a satana kuwagonjetsa; "Ufumu wa Mulungu" udakhala wotetezedwa, ndipo "Udindo wa Mpulumutsiyo" kukhala wa nsembe wathu wamkuru ndi Mfumu yathu udatsimikiziridwa.

"Panopa tsono chafika chipulumutso" kuonetsera kuti mbiri yonse yakwaniritsidwa. Kubadwa kwa Yesu Mpulumutsi wadziko lapansi kwachitika (vesi 5) Ngakhale satana adayesera kuopseza, koma Yesu adakhala moyo wosachimwa, nafa ndi kuuka kugonjetsa tchimo ndi imfa (vesi 10) satana wagonjetsedwa kwa muyaya (vesi 7-9) Mtanda wakuzidwa m'mphamvu zake zonse.

Kulemekeza koti "Tsopano yafika nthawi ya chipulumutso" sikosangalatsa Yohane yekha ayi, komanso dziko lonse lapansi.

"Chifukwa cace, kondwerani, miyamba inu, ndi Inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nao udani waukuru, podziwa kuti kamtsalira kanthawi." - Chibvumbulutso 12:12.

M'mwamba monse mukondwerera chigonjetso cha Yesu Kristu adaononga zonse zomwe satana amati ndi zake kumwamba, ndipo satana wogonjetsedwayo adalibenso kanthu kake ngakhale m'dziko lathu lino lapansi.

3. MPINGO WA KHRISTU ULI PAMKANGANO NDI SATANA

Yesu asadakwere kunka kumwamba, adakhazikitsa mpingo wake (chizindikiro cha mkazi). Imfa yake ya pa mtanda idapereka mphamvu zogonjetsera satana ku mpingo wake.

Ndipo iwo (Akhristu) anamlaka Iye chifukwa ca mwazi wa Mwana wa Nkhosa, ndi chifukwa ca mau a umboni wao kungakhale kufikira imfa." - Chibvumbulutso 12:11.

Kristu panopa akutha kupereka mphamvu zake, yomwe iri mphatso ya chigonjetso chake, kwa mpingo wake, Yesu mogonjetsa satana adaonekera pa mtanda paja ndipo akupitirira kuonekerabe ndi chigonjetsochi kupyolera mu Mpingo wake. Pali zizindikiro zoonetsera zitatu za mpingo wogonjetsa mu nthawi yakalelo ya Chikhristu:

(i) "Adamlaka Iye (satana) ndi mwazi wa Mwanawankhosa" Yesu adatengedwa kupita kumpando wa chifumu wa Mulungu kuti mwazi wake ukapangike kukhala ndi chikoka mu miyoyo ya omutsatira ake. Iye angathe kufufuta machimo athu onse, ndi kutipulumutsa mu mwazi wake wokhetsedwa (Yohane 1:7), ndikutipatsa ife mphamvu za kukhala moyo wabwino wachikristu tsiku ndi tsiku.

(ii) "Iwo sadakonde miyoyo yawo kuti akaope imfa" "Mwazi wa mwanawankhosa"udawapanga iwo kulola kufa chifukwa cha Khristu, ndipo iwo "sadaope imfa" Mulungu adazunzika kwambiri, ndipo awa ofera dzina la Khristu adaloleranso kuzunzika ndi kufa. Ngakhale ena adapanda nsembe yoyenerera. Nthano ikunenedwa ya Mayi wina wachikhristu yemwe adaponyedwa mu dzenje la mikango mu nthawi ya ulamuliro wa chi Roma chifukwa chakuti iye adatsimikizira kukhala ndi kuchita za Yesu osati za dziko. Mwana wake wamkazi wang'ono, mmalo moti achite mantha ndi kubwera m'mbuyo, adamva mumtima mwake chikakamizo cha kudzipereka. Pamene mikango inalimbana ndi a Mayi ake, iye adaima kuonerera akulira nati. "Inenso ndine mkhristu" Akulu akulu achi Roma adam'manga iye namuponyanso ku zilombo zolusazo.

(iii) "Iwo adamugonjetsa iye (satana)…ndi mau a maumboni awo" osati mawu okha, koma liwu la umboni wawo; umboni wa moyo wawo, kukhala moyo wa umboni ku mphamvu ya Yesu ndi uthenga wake. M'nthawi ya mdima woopsa wa nthawi ya chi Khristu, asilikari a gulu lankhondo - kuchokera mu mpingo likutsogolera iwo akuteteza mpingo wake wa Mulungu potsutsana ndi dziko. Iwowa adagonjetsa mdierekezi ndi choipa chake chonse pa iwo, pongochitira umboni ndi ntchito za miyoyo yawo.

Pa Chibvumulutso 12:11 akuonetsera mpingo wodzala ndi anthu ogonjetsa; atumwi, ofera ntchito ya Khristu, osungitsa choonadi, ndi ena onse okhulupirira, chifundo chawo, kukhulupirika kwawo, kulimba mtima kwawo ndi chigonjetso chawo chachita bingu mu nthawi zonse za dziko lapansi.

Popeza kuti satana analephera kuononga Yesu pamene anakhala pa dziko lapansi, panopa tsopano akufunitsitsa kuononga a Khristu amene ali mu mpingo wake.

"Ndipo pamene chinjoka chinaona kuti chinaponyedwa pansi kudziko, chinazunza mkazi amene adabala mwana wa mwamuna. Ndipo anapatsa mkazi mapiko awiri a chiomba nkhanga chachikuru, kuti akaulukire ku chipululu, ku mbuto yace, kumene adyetsedwako nthawi, ndi nthawi, ndi nusu la nthawi, osapenya nkhope ya njoka. Ndipo inalabvulira m'kamwa mwace, potsata mkazi, madzi ngati m'tsinje, kuti akakokoloredwe mkazi nawo. Ndipo dziko linathandiza mkaziyo, ndi dziko linatsegula m'kamwa mwace, nilimeza madzi a mtsinje amene chinjoka chinalabvula m'kamwa mwace." - Chibvumbulutso 12:13-16.

Monga m'mene zinaloseredwa, mu nthawi ya mdima waukuru wa nyengo ya chi Khristu, satana adatuma "mtsinje" wa chizunzo chakupha "kuti uyeretse kusesa" mpingo "ndi madzi othamanga" satana akufuna kuononga chikoka cha Mulungu pochotsa mpingo wake ndi pogwiritsa nzeru za chining'a mmene angathere za kuipa kwake pochita izi. Njoka ikuimira satana kuyambirira, komanso kumbukirani kuti satana amagwiritsa ntchito mabungwe a anthu mu ntchito yake monga njoka kuti agonjetse anthu a Mulungu. Adagwiritsa ntchito mfumu ya chi Roma, Herode kuyesera kupha Yesu Khristu mwanayo atangobadwa kumene. Adagwiritsa ntchito adani a Yesu opembedza a kaduka kuzunza ndi kupachika Mpulumutsi; nafika pachimake popachikitsa Yesu pa mtanda. Koma chigonjetso cheni-cheni cha satana chidasandulika chigonjetso chachikuru cha Kristu.

Pokwiya ndi kugonjetsedwa kwake pamtanda, satana wautembenuzira mkwiyo wake ku mpingo umene Yesu adakhazikitsa. Muzaka makumi makumi zotsatira atafa Yesu mopachikidwa, zikwi za anthu adaphedwa mu ulamuliro wa chi Roma, m'mizinda, m'zipululu ndi m'malo ena onse.

Poyamba, maukulu a dziko adalimbikitsa chizunzo ndinenachi. Koma atafa atumwi, kusintha kudabwera mu mpingo. Mu zaka za mazana awiri; atatu ndi anayi; anthu ambiri adayamba kukweza choonadi chomwe Khristu ndi atumwi ake adachiphunzitsa. Atsogoleri ena otsutsana ndi izi adayambapo kupha okhulupirira omwe adaima nganganga pa chiyero cha m'chipangano cha tsopano ndi zikhulupiriro zake.

Aphunzi amayerekezera kuti pafupifupi zikwi zikwi makumi asanu za anthu okhulupirira adaonongedwa poyesera kuumiriza mpingo ndi kuuononga, mdierekezi adatuma "mtsinje" wa chizunzo kuti usese mpingo ndi madzi othamanga mwa liwiro, kuuchotsa:…"koma dziko lapansi lidathandiza mkaziyo,…. Pomeza mtsinjewo" wa masautso ndi umboni wabodza.

Munthawi ya mkatikati mwa chisautsochi, mpingo woona udachokamo mu utsogoleri wa mipingo yonama, naubisala mu "Chipululu, ku malo okonzetsedwa iwo ndi Mulungu, kumene ukasamalidwa bwino kwa masiku chikwi, mazana awiri ndi mphambu makumi asanu ndi limodzi (1260 days) (vesi 6) ulosi uwu udakwaniritsidwa m'zaka zimenezi za chikwi, mazana awiri ndi makumi asanu ndi limodzi za chisautso kuyambira m'chaka cha 1798 (tsiku loimira chaka mu zizindikiro wa ulosi wa Baibulo. Onani pa (Ezekieli 4:6).

Munthawi ya zaka zamdimayi, a Khristu okhulupirika adapeza mpumulo wawo pali ponse pamene iwo adakhala, monga ku chigwa cha Waldens ku zambwe kwa dziko la Italy, ndi kum'mawa kwa dziko la France, komanso mu mpingo wa ku Celt wa ku zilumba za ku Britain.

4. MPINGO WA MULUNGU M'MASIKU ATHU ANO

Apa tikudza ku nthawi yathu ino- ku mpingo woona wa Mulungu kuyambira m'chaka cha 1798. Monga zingayembekezedwe, mdierekezi adakalibe wokwiya ndi anthu ake a Mulungu, nkhondo yosaonekerayo ikupitirirabe. Ndipotu satana, cholinga chake chiri pakugonjetsa mpingo Khristu asanabwere.

"Ndipo chinjoka chinakwiya ndi mkazi, nicinacoka kunka kucita nkhondo ndi otsala a mbeu yace, amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nao umboni wa Yesu." - Chibvumulutso 12:17.

Ulosiwu ukunena za nthawi ya masiku athu ano. Satana wakwiya; akuchita nkhondo pa "Otsala" a mbewu ya mkaziyo" - anthu ake a Mulungu a lero. Onani mosamala zizindikiro za anthu ake amenewa:

(i) Anthu okhulupirira a masiku otsirizawa "amamatira ku umboni wa Yesu" kumamatira mokhulupirika ku ziphunzitso zoyenera za mawu a Mulungu, kwapangitsa iwowa kuchitira umboni za Yesu pakukhala moyo wodabwitsa kwambiri.
(ii) Anthu okhulupirira a masiku otsiriza ndi anthu a ulosi. Kulandira "umboni wa Yesu Khristu" kudamupangitsa Yohane kutha kulemba bukhu la Chibvumbulutso (Chibvumbulutso 1:1-3) gulu lomaliza la anthu okhulupirira lidzalandiranso mphatso yomweyo: Maumboni ochokera kwa mwini wake Mulungu kudza mwachindunji kwa mtumiki wa dziko lapansi. Mphatso yawo ya ulosi idzatsimikizira pa za Chibvumbulutso cha Mulungu pa za cholinga chawo ndi mapeto awo.

Akhristu a masiku otsirizawa akudziwikanso monga "Iwo amene amvera Mulungu posunga Malamulo ake" Iwowatu sangoteteza kokha ukulu wa Malamulo Khumi a Mulungu ayi, komanso amamvera powasunga iwo. Chikondi cha Mulungu m'mitima yawo chimabweretsa chimwemwe cha kumvera (Aroma 5:5; 13:8-10).

Akhristu a masiku omalizawa amatsatira chitsanzo cha Yesu Khristu ndi mpingo woyambirira pakutsatira ndi kumvera Malamulo a Mulungu. Izi zimakwiyitsa chinjoka-mdierekezi. Ndipo akumema nkhondo ndi "Otsala" a "mbewu" ya mkaziyo chifukwa ali ndi umboni wakuti chikondi cha Mulungu chimabala akuphunzira ake omvera. Monga umene Yesu adalamulirira kuti:

'Ngati mukonda Ine, sungani Malamulo anga." - Yohane 14:15.

Miyoyo ya a Khristu a masiku omalizawa ikuonetsera kuti ndizotheka kumvera Mulungu ndi kumukonda ndi mtima wathu wonse, komanso kukonda nzathu monganso ife eni. Malinga ndi Yesu, zizindikiro izi, chikondi pa Mulungu ndi pa anthu ena, zikumanga malamulo onse khumi pamodzi kupanga lamulo lalikuru (Mateyu 22:35-40).

Lamulo lachinayi la iwo likutifunsa kusunga Sabata, tsiku lachisanu ndi chiwiri la pa Mulungu. Ndipo popeza chikondi cha pa Mulungu chagonera pa kukhazikika kwa Malamulo onse Khumi a Mulungu m'mitima yawo, a Khristu a masiku a kumapeto kwa nthawiwa ndi osunga Sabata.

Sabata ndilo mtima wa uthenga wace wa Mulungu wotsiriza kwa anthu ake m'Chibvumbulutso, mitu ya khumi ndi chiwiri, ndi khumi ndi chinayi (14:6-15) zonse zofunikara za kumwamba zaonetseredwa mwa okhulupirira a masiku otsirizawa polongoseledwa mu mitu imeneyi; Mpulumutsi wa moyo ndi yemwe ali ndi iwo monga bwenzi, ndipo Mzimu Woyera akugwira ntchito "kuwalimbikitsa mu mphamvu za mkati mwawo monga anthu". Lonjezo iri lokhazikika ndithu. Adzagonjetsa satana "ndi mwazi wa Mwana wa Nkhosa ndi mau a umboni wawo" (Chibvumbulutso 12:11).

Kodi inu mukufuna kukhala mmodzi wa a Khristu a mmasiku omaliza amene "omvera Malamulo a Mulungu" ndiponso "kukangamira pa umboni wa Yesu"? Bwanji kodi osapanga chitsimikizo choterechi tsopano lino?

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.