KODI MUNTHU AKAFA CHIMATSATIRAPO
NDI CHIYANI

Timazemba kuyankha funso limene mwana amafunsa kuti. "Kodi kufa ndi chiyani? "Timaganiza kuti ndizovuta kunena kapena kuganiza za munthu amene timamukonda kuti afe. Imfa ndi mdani wodziwika wa munthu kulikonse. Kodi nanga yankho la funso lovutali la imfa ndi chiyani? Kodi munthu akafa pamadzakhalanso moyo wina kwa iye? Kodi tidzathanso kuwaona okondedwa athu amene adafa kale?

1. KUKUMANA NDI IMFA MOPANDA MANTHA

Tonse, nthawi ina yake, mwina pakufa pa mbale kapena bwenzi lathu lapamtima, timaganizirapo za njala yomwe timamva ngati sitinadye kanthu, komanso kuganizirapo za mmene umasowera bwenzi poona za mapeto a moyo wa munthu.

Mwa mfundo zofunika kwambiri, zodzala ndi maganizo osiyana-siyana, tingaphunzire kuti za choonadi chake cha zomwe zimachitika munthu akafa? Mwa mwayi, mbali ya cholinga cha Yesu padziko lapansi inalinso "Kumasula onse iwo amene m'moyo wawo wonse adali mu ukapolo wa mantha a imfa" (Ahebri 2:15). Ndipo mu Baibulo, Yesu akupereka uthenga wolimbikitsa ndi kuyankha momveka bwino mafunso onse athu okhudza imfa ndi moyo ulinkudza.

2. MMENE MULUNGU ADATIPANGIRA IFE

Kuti timvetsetse kuchokera m'Baibulo zoonadi zeni-zeni za imfa, tiyeni tiyambe kuyambira pachiyambi ndi kuona mmene Mlengi wathu adatipangira ife.

"Ndipo Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi (Adamu mu chi Hebri) nauzira mpweya wa moyo m'phuno mwace, munthuyo nakhala wa moyo (Mzimu)." - Genesis 2:7.

Pa chilengedwe Mulungu adampanga Adamu "kuchokera ku fumbu la nthaka" adali ndi uwongo mutu mwace, wokonzekera kuganiza; mwazi mnjira zake, zokonzetsedwera kuti ukuyenda mthupi lonse. Ndipo Mulungu adauzira mphuno mwa munthuyo "mpweya wa moyo" ndipo Adamu adakhala "Munthu wa moyo" (mu chi Hebri, Mzimu wa moyo). Taonetsetsani apa mosamala kuti Baibulo silimunena kuti Adamu adalandira Mzimu ayi; koma likuti "munthu adakhala Mzimu wa moyo."

Pamene Mulungu adauzira mwa Adamu mpweya wa moyo, moyo udayambika kuyenda mwa anthu kuchokera kwa Mulungu. Kulumikizana kwa umodzi wa thupi ndi "mpweya wa moyo" kunapanga Adamu, "munthu wamoyo" choncho tingathe kulemba ndondomeko ya samu yake ya kupanga mwa umunthu motere:
"Fumbi la dothi lanthaka" + "Mpweya wamoyo" = "munthu kapena Mzimu wa moyo.
"Thupi lopanda moyo + mpweya wa Mulungu = munthu wa moyo" ali yense wa ife amaganiza. Pamene tiri otha kupuma, tidzakhala amoyo ndithu, mzimu wa moyo.

3. CHIMACHITIKA NDI CHIYANI MUNTHU AKAFA?

Pakufa, zimachitika ndi zosiyana ndi zija, zapachilengedwe za pa Genesis 2:7 ndizo zimachitika: "pfumbi ndi kubwerera pansi pomwe tinali kale, mzimu ndi kubwerera kwa Mulungu amene anaupereka." - Mlaliki 12:7.

Baibulo nthawi zambiri limagwiritsa ntchito mawu a chi Hebri pa liwu la "mpweya" ndi "Mzimu" mosinthana - sinthana pamene anthu afa, matupi awo amasandulika "fumbi" ndipo "mzimu" (mpweya wa moyo) umabwerera kwa Mulungu, kumene udachokera. Nanga kodi chinachitika ku munthu (mzimu wopangidwa) ndi chiyani?

"Pali Ine, ati Ambuye… Miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa Atate momwenso moyo wa mwana…moyo wochimwawo ndiwo udzafa." - Ezekieli 18:3-4.

Moyo umafa! Panopa siuli wosafa ayi - utha kuonongeka. Samu ya kapangidwe ija yochokera pa Genesis 2:27, pamene Mulungu adatipanga ife, imadzitembenuzanso yokha pamene tifa

"fumbi la kunthaka" - "mpweya wa moyo = "mzimu wakufa"
"thupi lopanda moyo" - "phweya wa Mulungu" = Munthu wakufa

Imfa ndi kutha kwa moyo. Thupi limaphwasuka kusandulika dothi, ndipo mpweya , kapena mzimu umabwerera kwa Mulungu. Ife ndife anthu chifukwa cha moyo, koma timakhala mitembo tikafa. Choncho akufa saganiza ayi, pamene Mulungu watenganso mpweya wake wa moyo womwe adaupereka, miyoyo yathu imatha, timafa. Koma m'mene tionere kutsogoloku, mu phunziroli, mwa Khristu tiri ndi chiyembekezo

4. KODI MUNTHU WAKUFA AMADZIWA ZINTHU ZOTANI?

Tikafa, uwongo umaphwasuka, suthanso kudziwa kapena kukumbukira chirichonse. Zonse zochitika mwa munthu zimaima munthuyo akafa.

"Chikondi cao ndi udano wao ndi dumbo lao lomwe zatha tsopano…" - Mlaliki 9:6.

Akufa sadziwa kanthu, choncho sathanso kuzindikira za zochitika ziri zonse. Iwo ali olekanitsidwa kwathunthu ndi a moyo.

"Pakuti amoyo adziwa kuti adzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi" - Mlaliki 9:5.

Imfa iri ngati tulo topanda maloto - ndiponso, Baibulo litchula imfa monga "tulo" kwa nthawi makumi asanu mphambu zinayi. Yesu adaphunzitsa kuti imfa ili ngati tulo. Adati Iye kwa ophunzira ake.

"Lazaro bwenzi lathu ali mtulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo tace, chifukwa chace akuphunzira ace anati kwa Iye, Ambuye, ngati ali m'tulo adzacira. Koma Yesu adanena za imfa yache, koma iwowa anayesa kuti ananena za mpumulo wa tulo. Pamenepo Yesu anati kwa iwo momveka, "Lazaro wamwalira." - Yohane 11:11-14.

Lazaro adafa nakhala masiku anayi Yesu asadatulukile koma pamene Yesu adapita kumanda kwake kwa Lazaro adatsimikizira poonetsa kuti ndi kwa pafupi kwa Mulungu kuukitsa akufa, monga momwenso ziri ndi ife kudzutsa nzathu amene ali mtulo. Ndichopatsa chitonthozo kudziwa kuti abale athu okondeka omwe tidalekana nawo mu imfa ali "mtulo" kupuma mwa mtendere mwa Yesu. Njira ya imfa imene ifenso tidzadutsanso tsiku lina, iri ngati tulo taufulu takachetechete.

5. KODI MULUNGU AMAWAIWALA OGONA MU IMFA?

Kufa simathero a mbiri pa mmunda wa manda, Yesu adati kwa Marita, mchemwali wake wa Lazaro;

"Ine Ndine Kuuka ndi Moyo: wokhulupirira Ine angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo." - Yohane 11:25.

Iwo amene afa "Mwa Kristu" amakhala ali m'tulo mmanda mwawo - koma tsogolo lawo limankhala lowala. Yemwe amatha kuwerenga ngakhalle tsitsi lapamutu pathu natigwira ife kutinyamula mmanja mwake sadzatiiwalanso ife.

Titha kubwerera kunthaka titafa, koma mbiri yathu imakhalabe yoonekera poyera m'maganizo a Mulungu ndipo pamene Yesu adzabwera, adzaukitsa akufa ali oyera mitima onse ku tulo tawo, monga mmene adachitira ndi Lazaro.

"Koma sitifuna , abale kuti mukhale osadziwa za iwo akugona, kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe Chiyembekezo… Pakuti Ambuye adzatsika kumwamba mwini Yekha ndi mpfuu, ndi mau a mngelo wamkuru, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Ambuye adzayamba kuuka; pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse. Chomweco, tonthozanani ndi mau awa." - 1 Atesalonika 4:13, 16-18.

Pa tsiku la m'dzukiro, njira ya imfa idzakhala ngati kupuma kwakamphindi. Akufa sakuona kudutsa kwa nthawi. Iwo amene alandira Khristu monga Mpulumutsi wawo, adzaukitsidwa ku tulo tawo ndi liu la Ambuye lozizizwitsa lobwera ku dziko lapansi. Chiyembekezo cha kuuka kwa akufa chiri ndi mnzake? Chiyembekezero cha kukhala kumwamba komwe Mulungu "adzapukuta misozi iri yonse m'maso a anthu. Sikudzakhalanso imfa, kulira kapena maliro ndi zowawa ziri zonse. (Chubvumbulutso 21:4). Onse okonda Mulungu sayenera kuopa imfa, kupitirira imfa pali moyo wa muyaya wokwanira ndi Mulungu. Yesu wagwiriza "Mfungulo wa imfa" (Chibvumbulutso 1:18 popanda Khristu, imfa ikadakhala njira ya chimaliziro cha zonse, koma ndi Khristu, pali tsogolo la chiyembekezo chodala chowala.

6. KODI NDIFE OSAFA TSOPANO LINO?

Pamene Mulungu adalenga Adamu ndi Hava, adawalenga iwo kuti adzafa, koma akadakhalabe omvera Mulungu sakadafa, koma atachimwa, adataya ufulu wawo wokhala ndi moyo. Posamvera Mulungu adasandulika kukhala oti atha kufa. Tchimo lawo lidakhudza mtundu wonse wa anthu, ndi pakuti ali yense adachimwa, tiri ife oti titha kufa, (Aroma 5:12). Ndipo Baibulo silikufotokoza pali ponse kuti munthu amadziwanso kanthu kali konse akafa ayi.

Palibe pomwe Baibulo lidafotokozapo kuti mzimu tsopano uli woti sungafe. Mawu onse a chi Hebri ndi chi Herene onena za "Mzimu" kapena "Mpweya wa moyo" akunenedwa mwa nthawi chikwi, mazana asanu ndi awiri. Koma palibe ngakhale pamodzi pomwe adanena kuti izi sizidzafa. Panopa Mulungu Yekha ndiye ali wosafa.

"Mulungu…amene Iye yekha ali nao moyo wosatha." - 1 Timoteo 6:15, 16.

Mawu a Mulungu akulongosola momveka bwino kuti anthu a moyo uno ndi akufa: adzayenera kufa, koma Yesu akadzabweranso, machitidwe athu adzasinthika kwakukuru "Taonani, ndi kuuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika, m'kamphindi, m'kuthwanima kwa diso, pa Lipenga lotsiriza, pakuti lipenga lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osabvunda, ndipo ife tidzasandulika. Pakuti chobvunda ichi ciyenera kubvala chisabvundi, ndi cha imfa ichi kubvala chosafa." - 1 Akorinto 15:51-53.

Monga anthu, sitiri ife osafa panopa; koma chilimbikitso cha Ukhristu ndicho chakuti tidzasandulika osafa pamene Yesu adzabwerenso kachiwiri. Panganoli liri loona ndipo lidatsimikiziridwa kuona kwake pamene Yesu adang'amba manda ake kuwatsegula, Iye naturukamo wamoyo ndipo; "anatha imfa ndipo… naonetsera poyera moyo ndi cosavunda mwa uthenga wabwino" - 2 Timoteo 1:10.

Kuona kwa Mulungu pa mapeto a munthu kuli komveka bwino lomwe imfa yamuyaya kwa iwo okana Khristu ndi kukamamatira ku machimo; kapena kusafa monga mphatso pamene Yesu adzabwerere iwo amene amulandira Iye monga Ambuye ndi Mpulumutsi wawo.

7. KUKUMANA NDI IMFA YA OKONDEDWA ATHU

Mantha amene timavutika nawo nthawi zambiri ndiwo a imfa ndipo amafika pachimake pamene wokondedwa wathu amwalira. Kusoweka kwathu kwa kutaika kwake kumakhala kowawitsa. Yankho lenileni la izi ndi kulimbikitsa ndi pa zoti timuona Khristu wotonthozayo, kumbukirani kuti wokondedwa wanuyo ali m'tulo, ndipo ngati agona mwa Khristu adzaukitsidwa mu "kuuka kwa moyo" pamene Yesu adzabwera.

Mulungu akukonza kukumana ndi kugwirizananso kozizwitsa ana adzabwezeredwa kwa makolo awo. Amuna nadzabwezeredwa kwa akazi awo nakumbatirana m'dzanja la wina ndi mnzake. Kulekanitsidwa kwa nkhanza kwa moyo uno kudzatha. "Imfa yamezedwa mu chigonjetso" (1 Akorinto 15:54). Ena amaona ngati angathe kulumikizana ndi okondedwa awo omwe adalekana nawo kupyolera mu za mizimu (ziwanda) kapena matsenga. Koma Baibulo likufotokoza mwa chindunji kutichenjeza ife kuti tisaletse vuto la imfa mwa njira imeneyi.

"Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, funa kwa olaula ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa ca moyo, kodi adzafuna kwa akufa? - Yesaya 8:19.

Nzoonadi, chifukwa chiyani? Baibulo likufotokoza momveka bwino kuti akufa sadziwa kanthu. Choncho yankho la zopweteka zonse zokhuzana ndi kulekanitsidwa kwathu ndi okondedwa athu ndi chitonthozo chokha cha kwa Kristu basi. Kukhala ndi nthawi yolumikizana ndi Kristu ndiyo njira yokhayo yabwino kukula m'mavuto. Kumbukirani nthawi zonse, atafa okhulupirira Khristu adzagona ndi kudzidzimuka kwa kutulo lawo kudzakhala mfuu ya kubweranso kwachiwiri kwa Khristu kudzawaukitsa iwo ku imfa.

8. KUKUMANA NDI IMFA MOPANDA MANTHA

Imfa inatichotsera pafupifupi chiri chonse. Koma chinthu chimodzi chomwe siingatenge ndicho Khristu; ndipo Khristu atha kubwezeretsa zonse zomwe imfa ingatenge kwa ife imfa sidzalamulira nthawi zonse padziko lapansi, mdierekezi, woipa, imfa ndi manda zidzathera mu "ng'anjo ya moto" imene iri "imfa yachiwiri" (Chibvumbulutso 20:14).

Dotolo wina wamphamvu wotchedwa Dr James Simpson yemwe adapanga mankhwala othetsa ululu, adakhuzidwa ndi chisoni chachikulu ndi imfa ya mwana wake woyamba. adalira kwakukuru monga momwe kholo liri lonse lichitira koma adapeza njira ya ku chiyembekezo. Ndipo pa munda wa manda a mwana wakeyu adamangapo chizindikiro nalembapo mau awa omwe Yesu adanena okhuzana ndi kuuka kwake kwa akufa; "Ngakhale ziri chonchi. Ndiri ndi moyo."

Izi zikunena zonse, matsoka a munthu ngoonetsa ngati afufuta miyamba, nthawi zina; komabe ngakhale zitero, Yesu ali wa moyo! Mitima yathu itha kusweka; komabe, Yesu aliwamoyo! Mwa Khristu, tiri ndi chiyembekezo cha moyo ngakhale titafa. Iye ali "kuuka ndi moyo" (Yohane 11:25), ndipo akulonjeza "Chifukwa chakuti ndiri wa moyo, inunso muli a moyo" (Yohane 14:19). Khristu ndiye chiyembekezo chathu chokha cha moyo ngakhale timwalira. Ndipo akadzabweranso adzatipanga ife osafa. Sitidzakhalanso m'chigwa cha mthunzi wa imfa, chifukwa tidzakhala tiri ndi moyo wosatha. Kodi inu mwapeza chiyembekezochi choti tidzikhala nacho munthawi zathu zowawitsa? Ngati simunamulandire Yesu monga Ambuye ndi Mpulumutsi wanu, simungatero tsopano lino?

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.