KODI GEHENA NDI CHIYANI NANGA ALI KUTI

Kuombera mfuti mosaganiza kudachitika pamene m' phunzi wina adafika pa sukulu yake napha angapo a anzake mu kalasi. Munthu winanso wokhumudwa amene anachotsedwa ntchito anapita ku ntchito kwake kwa kaleko nakapha mkulu wa pa ntchitopo ndi mfuti. Mayi wina anakankhira galimoto yake m'nyanja atatsekeramo ana ake awiri, nafera m'madzimo.

Pafupifupi mu maiko akulu awiri a m'dziko lapansi, anthu zikwi-zikwi aphedwa pa kuyeretsa kwa m'chiweniweni, chifukwa cha kusemphana mawu kokhala zaka mazanamazana. Amuna, akazi, ana ngakhale makanda aphedwa ndi mfuti, kudulidwa nthulinthuli, kumenyedwa, ndi kugwiriridwa chigololo.

Kulanga uchigawenga woipitsitsawu popereka chilango cha imfa, ngakhale chifukwa chakupha mwankhanzaku, kumatsutsidwa ndi anthu ambiri magulu osagwirizana ndi chilangochi amatsutsa poyera ndi mokweza mawu, m'kumati chilango choterechi sichaumunthu koma "chachikunja ndi cha usatana." Iwo amafunsa, kodi anthu akuphawa sangathe kupulumutsidwa m'njira iliyonse?

Kodi njira yabwino yeniyeni ya umunthu yoti nkulangira zigawengazi ndiye iti? Mpando wopha ndi magetsi? Ena amaganizira zolasa jakisoni wa mankhwala aululu yemwe amapha munthu wolasidwayo mopanda kumva ululu. Enanso amanena kuti moyo ungachoke mwansanga pongompachika wopalamulayo.

Komatu mwa zonse zokambirana mokhudza mtimazi pa chilango cha imfachi, pali njira imodzi imene aliyense saiganizira. Palibe munthu yemwe amaganizira kuti zigawenga zakupha mwankhanzazi, zimene zimachotsa moyo wa anzawo mopanda chifundo, zimadzilanga zokha pomva kutsutsidwa mu ndingaliro (maganizo) zawo ndi kusautsika mu mtima pofikira kuzunzika mpaka imfa. Palibe, mwachitsanzo, yemwe wapereka ganizo loti zigandangazi zimapsa ndi moto wa mu mtima mwawo pang'onopang'ono mpaka kufa.

Koma a Khristu ambiri oona mtima amaganizira kuti Atate wathu wa Kumwamba adzachita choipa koposa apa. Oipa, iwo amatero, ayenera kuzunzidwa kuti alipire dipo la machimo awo. Kuonjezera apo, iwo amatenga zinthu za mabwalo olangira a Mulungu ngati malo akuzunza kosatha.

Makamakano kodi n'chiyani chimachitika kwa oipa? Kodi mapeto ao akulumikizika bwanji mu chikondi cha Mulungu ndi chilungamo chake? Tiyeni tiyang'ane m"Baibulo kuti tipeze yankho.

1. KUSWEKA MTIMA KOTSIRIZA KWA YESU

Kwa zikwi zisanu ndi chimodzi, Mulungu wakhala ali kudandaulira amuna ndi akazi:

"Uziti nao; Pali Ine; ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo." - Ezekiel 33:11.

Mtanda wa Yesu udaonetsera poyera mmene Mulungu akufunira kupulumutsa mtundu wa anthu wakugwawu. Pamene Yesu analira ndi mawu akulu pa mtanda, "Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita." Iye anaonetsera poyera mtima wake wosweka (Luka 23:34). Atangonena izi, Yesu anapereka moyo Wake ndipo, ena amakhulupirira, adafa Iye chifukwa cha mtima wosweka (Yohane 19:30, 34).

"Komabe ngakhale ndi chionetsero cha mphamvu choterechi cha chikondi cha Umulungu, anthu ambiri satembenukirabe kwa Yesu. Ndipo monga m'mene uchimo ukulamulirabe m'dziko muno, udzapitirizabe kuchulukitsa chisoni cha mtundu wa anthu. Chotero uchimo uyenera kuonongedwa. Kodi Mulungu akulinganiza motani pofuna kuuthetsa uchimowu?

"Koma tsiku la Ambuye lidzadza …; m'mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam'mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo DZIKO NDI NTCHITO ZIRI MOMWEMO ZIDZATENTHEDWA." - 2 Petro 3:10.

Mulungu pomalizira pake ayenera kuyeretsa dziko kulichotsera chivundi chonse ndi kuthetsa uchimo. Iwo amene apitiriza kuumirira uchimo adzaonongedwa ndi moto umenewu wokonzedwera kuononga mdierekezi, angelo ake ndi uchimo kuuchotsa mu dziko lathu lino. Nthawi yowawitsa nanga kwa Yesu pamene akuona moto ukunyeketsa iwo amene Iye adawafera pofuna kuwapulumutsa.

2. KODI GEHENA ALI KUTI NANAGA ADZAYAKA LITI?

Motsutsana ndi maganizo ena otchuka, Mulungutu alibe moto umene ulinkuyaka pakali pano kumalo wena otchedwa "Gehena" kumene anthu amapitako akafa. Gehena adzakhala pamene dziko lino liti lidzasandulike nkukhala nyanja yamoto. Mulungu akudikira kudzagumula mulandu wa oipa mu chiweruziro chotsiriza kumapeto a zaka chikwi (Chibvumbulutso 20:9-15).

"Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe." - 2 Petro 2:9.

Nthawi yokhayokhayinso Iye adzachotsa zonyansa zonse ndi moto woyeretsa.

"Miyamba ndi dziko la masiku ano ndi mau omwewo zaikika kumoto, zosungika kufikira TSIKU LACHIWERUZO ndi chionongeko cha anthu osapembedza." - 2 Petro 3:7.

Mulungu sanalinganizire mpang'ono ponse munthu wina aliyense kudzatsiriza moyo wake m'moto wa gehena. Koma pamene anthu akana kulekana naye satana ndi kuumirirabe kumachimo awo, ayenera potsiriza kulandira zotsatira za kusakha kwawo.

"Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a ku dzanja lamanzere, chokani kwa Ine otembereredwa inu, ku moto WOKOLEZEDWERA MDIEREKEZI NDI AMITHENGA AKE." - Mateyu 25:41.

Molingana ndi Yesu, ndi liti limene gehenayu adzayambe kuyaka?

"Ndipo monga namsongole asonkhanitsidwa pamodzi, natenthedwa pamoto, motero mudzakhala M"CHIMALIZIRO CHA NTHAWI YA PANSI PANO. Mwana wa munthu adzatuma ANGELO ake, ndipo iwo ADZASONKHANITSA PAMODZI, NDI KUCHOTSA ufumu wake ZOKHUMUDWITSA ZONSE, NDI ANTHU ONSE AKUCHITA KUSAYERUZIKA, NDIPO ADZAWATAYA IWO M'NG'ANJO YA MOTO; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano." - Mateyu 13:40-42.

Namsongole, yemwe ali anthu ochita zoipa, sakuotchedwa panopa ayi kufikira kumapeto ake a dziko lapansi. Chiweruziro chisanaperekedwe, dziko lonse la m'mwamba ndi lapansi liyenera kutsimikizira kuti Mulungu wachita naye munthu aliyense mwa chilungamo. Monga mudafotokozeredwa tsatanetsatane mu Phunziro 22, mu mkangano waukulu umene ukuchitika pakati pa Khristu ndi satana, satana wakhala akuyesetsa kulitsimikizira dziko lonse lapansi ndi m'mwamba momwe kuti njira ya uchimo ndiyo njira yopambana; Yesu wakhala akuonetsera kuti njira yakumvera ndiyo mfungulo (kiyi) ya moyo wokwanitsidwa.

Pakutha pa zaka chikwi, chionetsero chimenechi chidzatsirizira mu kuweruzidwa kwa satana, angelo ake, ndi oipa. Atatha kutsekulidwa mabukhu omwe adzasonyeze mbali imene munthu aliyense anaichita mu zochitika zazikuluzi, Mulungu adzaponya satana, imfa, ndi manda, pamodzi ndi wina aliyense amene dzina lake "silinapezedwe lolembedwa m'bukhu lamoyo, anaponyedwa m'nyanja ya moto, (Chibumbulutso 20:14, 15). Molingana ndi vesi lotsatiralo, Chibvumbulutso 21:1, Mulungu atatha kuliyeretsa dziko lapansi kuchotsa uchimo kudzera m'moto, Iye alenganso "M'mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano".

3. KODI GEHENA ADZAYAKA NTHAWI YAITALI BWANJI?

Okhulupirira ambiri amalilandira ganizo lakuti moto wa gehena udzayaka kwa muyaya, kusonyeza chilango chosatha. Tiyeni tione mosamalitsa ndime zimene zimafotokoza mmene Mulungu adzachitire nalo tchimo ndi ochimwa.

"Iye adzabwezera chilango kwa iwo osamdziwa Mulungu, ndi iwo osamvera uthenga Wabwino wa Ambuye Wathu Yesu, amene adzamva chilango, ndicho CHIONONGEKO CHOSATHA chowasiyanitsa ku nkhope ya Ambuye, ndi ku ulemerero wa mphamvu yake." - 2 Atesalonika 1:8, 9.

Chonde onani kuti "chionongeko chosatha" sizifanana ndi "chizunzo chosatha" ai, koma kuti zotsatira zake za chionongeko chimenechi zidzakhala zotsirikiziratu kwa muyaya. Sichidzabweranso chionongeko china ai. Zochitikazo ndizo imfa yosatha. Petro ananena za tsiku la chiweruziro ndi "chionongeko cha anthu osapembedza" (Petro 3:7).

Molingana ndi Yesu, "moyo ndi thupi" lomwe zidzaonongedwa m'gahena (Mateyu 10:28). Mu chiphunzitso chake cha paphiri, Yesu adanena za chipata chopapatiza yomwe ili njira "yakumuka nayo ku moyo" ndi njira yotakata yomwe ili "yakumuka nayo ku kuonongeka" (Mateyu 7:13, 14). Mu Yohane 3:16, Yesu akufotokoza kuti Mulungu "anapatsa Mwana Wake wobadwa yekha." Kuti iwo onse akukhulupirira Iye "asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha". Yesu akuyerekeza mapeto a zochitika ziwirizi: moyo wosatha kapena kutaika - osati kumangopsabe mpaka muyaya. Tiyenera tsono kumaliza mwakuti gehena ali ndi mapeto ake otsimikizika: mu imfa ndi m'kuonongeka kwa oipa.

Zolembera zomveka bwino m'malembo opatulika zimatiuza kuti oipa adzaonongedwa.

"Oipa adzadulidwa" (Masalmo 37:28) iwo "adzaonongeka" (2 Petro 2:12) "adzanyeka monga utsi, adzakanganuka" (Masalmo 37:20). Motowo udzawayatsa kuwanyeketsa ndi kuwatsiriza, nasanduka phulusa (Malaki 4:1-3). "Mphotho yake ya uchimo ndi imfa," osati moyo wosatha mu moto wa gehena ayi; "mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha" (Aroma 6:23).

Cholinga cha chilango chotsirizachi mu moto wa gehena ndi kuchotsa uchimo pa dziko lonse, osati k usunga kwa nthawi zosatha ayi. Ndi yovuta kwambiri kuganizira kuti Khristu yemwe adalirira Yesusalemu chifukwa cha kuuma mtima kwake ndi yemwe adakhululukira iwo amene anamupha Iye angakhoze kukhala nthawi zamuyaya akuyang'anira zowawa za iwo olangidwa.

Gehena ndithu ali ndi mapeto ake. Pakutha pa zaka chikwi, Mulungu adzavumbwitsa moto kuchokera ku mwamba ndipo adzachotsa kotheratu mdierekezi, angelo ake ndi wonse oipa amene aumirira ku machimo ao. "Moto" udzatsika "kuchokera kumwamba nuwanyeketsa iwo," (Chibvumbulutso 20:9).

Molingana ndi Yesu, moto umenewu ndi "moto wosazima" (mateyu 3:12). Palibe gulu lina lililonso la zimani moto lomwe lingadzathe kuuzimitsa motowu kufikira utadzachita ntchito yake yonse yakuononga kotheratu.

Mulungu akulonjeza kuti, kuchokera mu moto woyeretsawu, Iye adzalenga, "dziko latsopano," mmene "zovuta zakale zidzaiwalika; ndipo "mau akulira sadzamvekanso mwa iye, pena mau akufuula (Yesaya 65:16-19).

Tsiku lodabwitsa nanga! China chilichonse choyambitsa kusweka mtima kapena kukhumudwitsa chidzachoka. Mulungu adzapoletsa mabala a uchimo ndi kufafaniza zipsera zonse kuzichotsa mu mtima uliwonse, ndipo chimwemwe chathu chidzakhala chodzaza.

4."NTHAWI ZOSATHA" M'MALEMBA (M'BAIBULO)

Mu Mateyu 25:41 Yesu akunena za "moto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi amithenga ake" Kodi mawu akuti "nthawi zonse" apa akupereka ganizo lakuti gehena ndi wamuyaya? Yuda amatipatsa Sodomu ndi Gomora monga "chitsanzo… cha chilango cha moto wosatha." Moonekeratu mizinda imene ija siikuyakabe mpaka lero. Koma motowo unali wosatha muganizo lakuti zimene unachitazo zinali chionongeko chotsimikizika.

Mu 2 Petro 2:6 timawerenganso za moto wosatha. Komano lemba ili limaonetseratu momveka bwino kuti Mulungu "anaisandutsa makala midzi ya Sodomu ndi Gomora anaitsutsa poigwetsa, ataiika.
Chitsanzo cha kwa iwo akakhala osapembedza. Osapembedza a mu Sodomu ndi Gomora sali mu chisautsobe mpaka lero ayi; iwo anasandulitsidwa phulusa kalekale. Komabe moto udawanyeketsawo ndi "wosatha" mu zotsatira zimene udachitazo-chionongeko chotsimikizika. "Kusatha" kutanthauza chilango chotsimikizika ndi chosasinthika, osati kulangika komangopitirirabe.

Popeza bukhu la Chibvumbulutso limagwiritsa ntchito mawu amaphiphiritso komanso ooneka ngati zinthu zenizeni, zina za ndime zake zamvetsedwa molakwika. Mwa chitsanzo, Chibvumbulutso 14:11 amanena za otaika kuti, "utsi wa kuzunza kwawo ukwera ku nthawi za nthawi." Izitu zimaoneka ngati kuzunzika kopanda mapeto. Koma, mobwerezanso, tiyeni tilole malemba (Baibulo) azimasulire okha.

Eksondo 21:16 akunena za kapolo wobooledwa khutu monga chizindikiro chakuti ayenera kutumikira mbuye wake "kwa muyaya (kosatha). Apapatu "muyaya" akutanthauza nthawi yonse yomwe kapoloyo akali moyo. Yona, yemwe adakhala m'mimba mwa chinsomba masiku atatu okha ndi usiku wake (Mateyu 12:40) amanena kuti iyeyo adakhala mmenemo "kwa muyaya" (Yona 2:6). Nzosadabwitsaditu apa chifukwa kukhala mu mdima waukulu mkati mwa chinsomba kudaoneka ngati muyaya.

Chotero tiyenera kusamalitsa pofuna kumvetsetsa za mmene ndi nthawi imene Baibulo likugwiritsa ntchito ziphiphiritso kapena mau a chining'a ngati ndakatulo. Utsi wokwera nthawi za nthawi kuchokera ku nyanja ya moto ndi njira yeniyeni yomveka bwino pofotokoza kuononga komaliziratu, Chibvumbulutso 21:8 akutiuza poyera kuti nyanja yotentha ndi moto ndi sulfure ndiyo "imfa yachiwiri". Gehena ali ndi mapeto ake. Oipa anyeketsedwa; iwo aonongedwa.

5. KODI NDI CHIFUKWA CHIYANI KUYENERA KUKHALA GEHENA?

Pachiyambi Mulungu analenga dziko langwiro. Koma tchimo linadza ndi kubweretsa mavuto oopsa, chivundi ndi imfa. Inu mutafika ku nyumba kwanu madzulo ena ndikupeza kuti nyumbayo yafwanyulidwa fwanyulidwa ndi kuonongedwa, mungaisiye choncho kwa nthawi zonse? Ndithu ayi. Musesa zinyalala zonse ndi zinyasi zonse, kukonza malo onse, ndi kutaya mipando yonse yothyoledwa mosakaza. Mulungunso naye adzachita chimodzimodzi. Adzakonza zophwasuka ndi zoonongedwa ndi tchimozo kwa nthawi zonse, nkuyeretsa dziko ndi moto n'kuti akonzetsere njira ya dziko langwiro momwe mudzakhale anthu opulumutsidwa.

Komano Mulungu akukumana ndi vuto lalikulu popeza tchimo silinangosakaza dziko leni leni lokhalo ayi, komanso linaononga anthu okhala m'dzikomo. Tchimo linasokoneza ubale wathu ndi Mulungu, komanso ndi wina ndi mzake. Umunthu ukupitirirabe kuzunzika ndi vuto la kuzunza ana, kuopsezana pakuphana, kanema wa zaumaliseche, ndi matenda ambiri a khansala yosiyanasiyana ya moyo wauzimu. Chotero Mulungu ayeneradi tsiku lina kuliononga tchimo, chifukwa ilolo likusakaza anthu. Njakata ya Mulungu ili apa: Achotsa bwanji kachilombo koopsa koyambitsa utchimo m'dziko komano osaononga anthu onse omwe ali ndi tchimolo? Yankho lake linali kutenga kachilomboko kakhale m'thupi mwake; kulola kuti khansala ya uchimoyo iwononge thupi lake pamtanda. Zotsatira:

"Ngati tivomereza machimo anthu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo anthu, ndi KUTISAMBITSA KUTICHOTSERA CHOSALUNGAMA CHILI CHONSE." - 1 Yohane 1:9.

Mulungu apa akupereka yankho lake ku vuto la uchimo kwa aliyense kwaulere. Koma chomvetsa chisoni ndi chakuti anthu ena akukangamirabe ku nthenda ya uchimoyi. Ndipo Mulungu sadzawaumiriza iwo kutsata njira Yake ya moyo wosatha. Iwo amene akana yankho lakelo adzanyeketsedwa ndi nthendayi pamapeto pake, cholinga chenicheni cha Gehena ndi ichi:

"Pakuti pamene ndinaitana, inu simunayankhe; pamene ndinanena, simunamve; koma munachita choipa m'maso mwanga, ndi kusankha chimene Ine sindinakondwera nacho." - Yesaya 65:12.

Atalekanitsidwa ndi Yesu mwa chisankho chawo, oipa adzafika pozindikira kuti palibenso njira ina yowayenera koma imfa yamuyaya basi.

6. KODI KUTAIKA KUDZAPINDULANJI?

Ngakhale Baibulo siliphunzitsa kuti zotsatira za moto wa Gehena ndi chizunzo chosatha, linatipatsabe masomphenya a zowawa zoopsa zimene adzakumane nazo anthu otaika. Anthu oipa adzausowa moyo wosatha. Choopsatu nanga kuzindikira kuti chimwemwe cha moyo wosatha ndi Mulungu chapulumuka m'manja mwawo, kuti iwo sadzaonanso ukoma ndi kununkhira kwa chiyanjano chokonda ndi changwiro cha mibadwo mibadwo.

Pamene Yesu adapachikidwa pamtanda ndi machimo a dziko lapansi kumulekanitsa ndi Atate, ayenera kuti adamva kuwawa kwake kwakutaikiratu kosatha. Monga oipa akamaona chimdima cha phompho lopanda kanthu lili patsogolo pawo, iwo amangoona chionongeko chosatha chokha basi. Pa nthawi yokhayokhayo, iwo amaonanso m'mene adamkankhira Khristu kutali ndi iwo kawirikawiri pamene Iye adadza pafupi ndi zidandaulira za chikondi. Pa mapeto pake, iwo agwa pansi pa maondo awo navomereza chilungamo cha Mulungu ndi chikondi chake (Afilipi 2:10).

Nzosadabwitsa kuti anthu olemba Baibulo amakanikiza pa ife mwachangu kulemera kwake kwa zisankho zathu ndi za zomwe Khristu amanena za Iye Mwini.

"Tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu, (pakuti anena, m'nyengo yolandiridwa ndinamva iwe, ndipo m'tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza, taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la chipulumutso)" - 2 Akorinto 6:1, 2.

Ndikuganizira kuti palibenso tsoka lina lalikulu loposa la munthu amene wataya nsembe ya mtengo wapatali ya Yesu posankha kutaika. Zisankho zomwe tayang'anana nazo zaonetsedwa poyera ndi momveka bwino: chionongeko chamuyaya-kulekanitsidwa kwa nthawi zosatha kuchokera ku nkhope ya Mulungu, kapena ubwenzi wamuyaya ndi Khristu umene udzakhutitsa zolakalaka zathu zakuya. Inu mudzisankhira nokha chiti? bwanji osadzipezera nokha mapeto a moyo wanu mwa Khristu lero?

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.