KODI MULUNGU NDI WACHILUNGAMO

M'nyamata wina waphedwa ndi mfuti akulemba ntchito yake yakusukulu pagome lakunyumba mkati mwa mzinda wina.

Mayi wachichepera mu dela la mzinda wina wapeza kuti mwana wake ali ndi matenda a Edzi chifukwa cha magazi oonongeka ndi matendawa omwe iye analandira kuchipatala atadwala.

Mavuto a matsokawa a kunka nachulukira-chulukirabe m'dziko lathu lapansili. Ndipo tikufuna yankho la zonsezi. Kodi Mulungu amakhala ali kuti m'dziko la mavuto ndi imfa? Wolemba Masalimo akutitsimikizira ife kuti "Dziko ladzala ndi chikondi chake cha Mulungu chosalephera" (Masalimo 33:5).

Koma ngati izi ziri zoona, ndi chifukwa chiyani Iye sathetsa kunzunzika ndi matsokawa? Mutu wamakumi awiri wa Chivumbulutso ukutionetsera m'mene Mulungu adzathetsere tchimo ndi mazunzo komanso nthawi yake ya zonsezi.

1. ZAKA CHIKWI ZIVUNDUKULIDWA M'KUSATHULA

Mutu wa Makumi awiri wa Chivumbulutso ukulongosola momaliziratu za zaka chikwi zotsatira pa kubweranso kwa Khristu. Zochitika za m'zaka zimenezi zidzakhala zomaliza mu mkangano wa Satana ndi Khristu womwe wakhalako kuyambira pamene tchimo linalowa m'dziko.

Zonsezi zinayambira kumwamba pamene Lusifara anachita nsanje ndi Khristu, nayamba nkhondo ndi angelo osagonjetsedwawo, naponyedwa kuchokera kumwamba kudza ku dziko lapansi. Izi zinapitirira pa dziko lapansi m'munda wa Edeni, mpaka pamene zinafika pa chimake choyamba pomwe Mdierekezi anakopa anthu kuti am'pachike Yesu. (Mutha kuwerenganso izi mu phunziro lathu la chitatu lija). Zochitikazi zidzafika pachimake chomaliza potha pa zaka chikwi zimenezi pamene dziko lathu lauchimoli lidzayeretsedwa ndi kuikidwa pansi pa ulamuliro wa Kristu. Chibvumbulutso 20 akutisonyezera ife kuti zaka chikwi zimenezi zagawidwa mu midzukiro iwiri ya akufa.

Kodi Mulungu adzaukitsa ndani kwa akufa mu mdzukiro woyamba omwe udzachitike ku mayambiriro a zaka chikwizo?

"Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yochiwiri iribe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, nadzacita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwizo." - Chibvumbulutso 20:6.

"Wodala ndi woyera" iwo amene anamulandira Yesu ngati Mpulumutsi wawo, akuturuka m'manda mu"Kuuka koyamba". Ngati wolungama "Adzalamulira pamodzi" ndi Khristu munthawi ya zaka chikwiyi, adzayeneradi kuuka kumayambiriro kwake kwa zakazi.

Nanga ndi ati omwe adzauke kwa akufa kachiwiri kumapeto kwake kwa zaka chikwizi?

"Otsala akufa sanakhalanso ndi moyo kufikira kudzatha zaka chikwi." - Chibvumbulutso 20:5.

"Otsalawo akufa akutanthauza akufa osalungamawa, chifukwa olungama," wodala ndi woyera" auka kale ku mdzukiro woyamba wa zaka chikwizi.

Choncho nthawi ya zaka chikwiyi ikusonyezedwa bwino ndi kuuka kwa akufa kwa mitundu iwiri: kuuka kwa anthu oyera mtima koyamba, ndi kuuka kwa anthu ochimwa kwa kumapeto kwa zakazi.

2. KUUKITSIDWA PAKUBWERANSO KWA KHRISTU

Kuuka koyambirira, kwa wolungama, kukuchitika pakubweranso kachiwiri kwa Yesu Kristu.

"Pakuti Ambuye adzatsika kumwamba mwini Yekha ndi lipenga la Mulungu, NDIPO AKUFA MWA AMBUYE ADZAYAMBA KUUKA; pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye m'mlengalenga. Ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse." - 1 Atesalonika 4:16, 17.

Podzabwera Yesu kachiwiri kudziko lapansi, akudzaukitsa" akufa mwa Khristu" ndi kuwatenga. Iwo pamodzi ndi olungama amoyo, kupita nawo kumwamba. Popeza wochimwa adzakhala ndi chikangamirire ku uchimo, sangaonekerenso pamaso pa Mulungu, ndipo adzaonongedwa pakudza kwa Khristu (Luka 17:26-30) (Mutha kukawerenganso phunziro lathu la chisanu ndi chitatu lija za zochitika pakubweranso kwa Khristu).

3. SATANA ADZAKHALA MMAUNYOLO A NDENDE KWA ZAKA CHIKWI

Pamene nthawi ya zaka chikwiyi idzayamba, wolungama adzakhala onse atapita kumwamba, ndipo ochimwa onse adzakhala atafa ali m'manda mwawo. Nanga chidzidzachitika ndi chiyani pa dziko lapansi?

"Ndipo ndinaona m'ngelo anatsika kumwamba, nakhala nacho chimfungulo cha phompho, ndi unyolo waukuru m'dzanja lace. Ndipo anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye mdierekezi ndi Satana, nam'manga iye zaka chikwi' namponya ku phompho, natsekapo, nasindikizapo cizindikiro pamwamba pache, kuti asanyengeso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi." - Chibvumbulotso 20:1-3.

Pakubwera kwa Yesu, Satana adzamangidwa nakhala muunyolo mu zaka chikwi. Nanga ndende yake ya Satanayo idzakhala kuti? Ku "phompho", liwu lachihelene lotanthauza "Kwakuya kwambiri" kapena "Kopanda malire kupita pansi" Mu Genesis 1-2, m'chiherene cha chipangano chakale, "phompho" likulongosoledwa ngati m'mene dziko lidaliri kusadalengedwe kanthu kali konse. Choncho dziko lapansi ndilo "phompho" la ndende ya Satana komwe Mulungu adzamutsekereko iye.

Mawu a Mulungu akunena zoti Satana adzamangidwa "unyolo waukuru" Kodi umenewu ndi unyolo weni-weni womwe tikuudziwawu? Ayi ukuimira unyolo wa zochitika satana akadakonda kupitiriza kunyenga anthu mu zaka chikwi zimenezi. Koma sangapeze aliyense wolungama chifukwa adzakhala atapita kumwamba. Komanso sangapeze ngakhale munthu mmodzi wochimwa chifukwa adzakhala onse atafa, ali mmanda, kugona mu fumbi la nthaka ya dziko lapansi.

Adzayenda-yenda uku ndi uko m'dziko lopanda kanthu kusowa woti amunamize, ndipo adzaumirizidwa kuganizira za mitima ya anthu yomwe iye adaswa ndi matsoka omwe iye adadza kuwachititsa.

4. OYERA ADZAWERUZA OCHIMWA

Munthawi ya zaka chikwi, idzakhalanso nyengo ya chiweruziro. Koma kumbukirani kuti chiweruziro chiri ndi makhwerero eni eni anayi monga:-
(i) Chiweruziro cha oyera Yesu asanabwerenso kachiwiri
(ii) Mphotho ya wolungama pa kubweranso kwachiwiri kwa Yesu
(iii) Chiweruziro cha wosalungama mu nthawi ya zaka chikwi
(iv) Mphotho ya satana ndi omutsatira ake kumapeto kwa zaka chikwi. Mutha kubwerezanso phunziro lathu lija la chikhumi ndi chitatu lomwe likulongosola bwino za khwerero loyamba ndi lachiwiri la chiweruziro, ndi (chiweruziro kufufuza ndi mphotho ya oyera mtima).

Panopa tiona khwerero lachitatu ndi lachinayi, kufufuza ndi mphotho la ochimwa. Taona kuti akufa ali woyera omwe aikitsidwa ndi iwo amoyo oyera akutengedwa onse pamodzi kunka kumwamba pakubweranso kwachiwiri kwa Yesu Kristu. Ali kwawo kumwamba m'nthawi iyi ya zaka chikwi. Kodi adzakhala akuchitako chiyani?

"Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi?… Kodi simudziwa kuti tidzaweruza angelo?" - 1 Akorinto 6:2-3.

"Ndipo ndinaona mipando ya chifumu, ndipo anakhala pamenepo, ndipo anawapatsa chiweruziro… ndipo anakhala ndi moyo, nachita ufumu pamodzi ndi Khristu zaka chikwi." - Chibvumbulutso 20:4.

M'nthawiyi ya zaka chikwi, oyera adzaonanso mobwereza milandu ya anthu ochimwa ndi angelo akugwa, kuphatikizapo mtsogoleriwawo, satana. Choyeneratu nanga kwa iwo adafera ntchito ya Mulungu, ogonjetsa ndi oima nji mu nkhondo yoopsa ya uthenga wabwino, kuti afufuze ndi kumvetsa chiweruzo cha Mulungu pa anthu ochimwa.

Mwachisomo, Mulungu wapereka mwayi uwu wa kufufuza ntchito zake pa anthu ochimwa, kwa anthu ake oyera. Titha kukhala ndi mafunso ambiri monga ili: "Kodi chifukwa chiyani adzakhali anga siali nafe kuno? Iwo amaoneka munthu wabwino". Tikadzaona m'mabukhu ndi kuweruza akufa; "molingana ndi zomwe adachita zolembedwa m'mabukhuwo" (1 vesi 12) tidzaona tokha kuti Mulungu ndi wachilungamo ndi aliyense mu zochitika zake zonse pa munthuyo. Tidzaona mmene Mzimu Woyera udzaperekera mwayi kwa anthu nthawi zosiyana-siyana kuti afikire kwa Mulungu, ndi chilungamo cha chilango chawo chidzaonekera poyera.

5. SATANA AMASULIDWA PATATHA ZAKA CHIKWI

Kumapeto kwake kwa zaka chikwi, Bukhu Lopatulika likunena kuti:

"Ndipo ndinaona mzinda woyerawo, Yerusalemu watsopano, ulikutsika kumwamba kwa Mulungu, woko nzeka ngati mkwatibwi wokometsedwera mwamuna wace." - Chibvumbulutso 21:2.

Mzinda wozizwitsawu wakhala ngati kwathu kwa zaka chikwi. Ndipo panopa Mzinda woyerawu - pamodzi ndi Khristu ndi opulumutsidwa ake onse ali mkatimo, akutsika kumwamba kudza kudziko lathu lapansi. Kodi satana adzatani pa kutsekedwa kwa nthawiyi ya zaka chikwi?

"Ndipo pamene zidzatha zaka chikwi, adzamasulidwa satana m'ndende yace; nadzaturuka kudzasokeretsa a mitundu ali mu ngodya zinai za dziko… kudzawasonkhanitsa achite nkhondo, chiwerengero cao ca iwo amene chidzakhala ngati mcenga wa kunyanja. Ndipo anakwera nafalikira m'dziko, nazinga tsasa la oyera mtima ndi mudzi wokondedwawo." - Chibvumbulutso 20:7-9.

Ochimwa akuukitsidwa mu kuuka kwachiwiri pamapeto pa zaka chikwi (vesi 5) Pamene oyera mtima akutsikira ku dziko lapansi ali mu mzinda woyera ndipo ochimwa akuukitsidwa, satana "adzamasulidwa kwa kanthawi kochepa (vesi 3). Iye adzakhalanso ndi anthu ochimwa awa ngati mtsogoleri wawo ndi oyera monga adani oti achite nawo nkhondo. Mosataya nthawi; iye adzayamba kusonkhanitsa ochimwawa ku gulu lalikuru lankhondo. Ndipo adzalamulira iwo kuchita nkhondo ndi anthu okhala mu Mzinda Woyerawu. Pamene ochimwa adzidzatenga mbali zawo kuzungulira Yerusalemu (vesi 9), adzaona kuopsa kwake kulephera kulowa mumzindawu chifukwa chotaika - tataika tsono kwamuyaya.

6. CHIONETSERO CHA CHIWERUZIRO CHOTSIRIZA

Apa, kwa nthawi yoyamba, anthu a mtundu wake akukumana maso - ndi - maso pamodzi. Yesu akuwatsogolera ana a Mulungu opulumutsidwa omwe ali mkati mwa Mzindawo. Satana naye akutsogolera chigulu cha anthu ochimwa omwe ali kunja kwa mzindawo. Panthawi yoopsa iyi, Mulungu akupereka chiweruzo chake chomaliza ndipo ochimwa adzalandira zoyenera za mlandu wawo patsikuli.

"Ndipo ndinaona mpando wa chifumu waukuru woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pace… ndipo akufa anaweruzidwa mwa zolembedwa m'mabuku. Monga mwa nchito zao." - Chibvumbulutso 20:11, 12.

Pamene ochimwa adzaima pamaso pa chiweruziro cha chilungamo, moyo wao wonse udzatsegukira kuonekera poyera pamaso pawo, kuchokera m'mabukhu a kumwamba, Yesu, woweruza wachilungamo, adzatambasula mbiri yonse ya zochitika zake pa anthu akugwa, amuna, akazi ndi angelo. Dziko lonse lapansi lidzayang'ana ndi chidwi. Ataima pamaso pa mpando wa Mulungu, Yesu adzapereka umboni wonse womveka wa ntchito yake yakupulumutsa. Adzaulula kuti ndadza kufuna ndi kupulumutsa chotaikacho adadza m'dziko lathu lapansi mwa thupi la umunthu, nakhala moyo wosachimwa pakati pa mavuto ndi mayesero. Adapereka nsembe yokhayo ya pamtanda, natumikira monga wansembe wathu kumwamba. Pamapeto pake, pamene Khristu adzaima patsogolo, mwachisoni napereka chiweruzo cha iwo okhalabe ochimwa, kukana chisomo chake, ali yense m'dziko adzabvomereza chilungamo ndi kufunika kwake kwa chiweruzo chomalizachi cha Mulungu.

"Pakuti ife tonse tidzaimirira ku mpando wakuweruza wa Mulungu. Pakuti kwalembedwa, pali moyo wanga, ati Ambuye, mabondo onse adzagwadira Ine, ndipo malilime onse adzavomereza Mulungu." - Aroma 14:10-11.

"Yesu Khristu… anakhala womvera kufikira imfa ndiyo imfa ya pamtanda!… Mdzina la Yesu bondo lirilonse lipinde, la za m'mwamba ndi za padziko, ndi za pansi pa dziko… Ndi malilime onse avomere kuti Yesu Khristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate." - Afilipi 2:5-11.

Kuyambira nthawi yomwe chimo linayamba, Mdierekei wakhala akunyoza khalidwe lake la Mulungu, kumutsutsa Iye kuti ali wopanda chilungamo, koma tsopano mafunso onse adzayankhidwa, ndi zonse zosokonezeka zidzakhala mmalo mwake. Ndipo tsono, munthu aliyense m'dziko adzavomereza kuti Yesu, Mwana wa Nkhosa wa Mulungu, ndi woyenera chikondi ndi chitamando cholinga chonse cha Mulungu ndi ntchito yake tsopano zidzaululika kwathunthu, ndipo khalidwe la Mulungu lidzaima lopanda cholakwa.

Siopulumutsidwa okha ayi, komanso angelo oipawo ndi satana mwini wake adzavomereza kuti njira yake idali yolakwika ndi kuti njira za Mulungu ziri zachilungamo ndi zoona. Onse adzaona kuti choipa ndi kudzikonda zabweretsera iwo kusakondwa ndi kusakhutitsidwa ndipo siziri zoyenera kupitirira.

7. TCHIMO LIKUMANA NDI MAPETO AKE

Ngakhale satana ndi gulu lake lalikulu la anthu ochimwa adzabvomereza kuti njira zake za Mulungu ziri zoyenera, mitima yao sidzasinthika, khalidwe lawo lidzakhalabe chiipire. Ndipo chitatha chiweruzochi, ndi chigamulo chitaperekedwa ochimwawa;

"Anakwera nafalikira m'dziko nazinga tsasa la Oyera mtima ndi mudzi wokondedwawo; ndipo unatsika moto wakumwamba nuwanyeketsa; ndipo mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m'nyanja ya moto ndi sulfure… Ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufawo anali m'menemo, ndipo imfa ndi Hade zinaponyedwa m'nyanja ya moto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja ya moto ndipo ngati munthu sanapezedwa wolembedwa m'bukhu la moyo, anaponyedwa m'nyanja ya moto." - Chibvumbulutso 20:9-15.

Mu chiweruzo chotsiriza moto wa Mulungu wosatha udzaononga tchimo ndi onse okangamira tchimolo. Satana ndi onse otaikawo adzathedwa ndi "imfa yachiwiriyi" imfa yosatha yomwe sadzaukanso. Njira yawo yakunkira idzawasiya iwo osayenera kukhala nawo pa chisangalalo cheni cheni, naonongedwa naye pamodzi mdierekezi ndi angelo ake. Moto wakumwamba udzayeretseratu dziko lonse lapansi ku tchimo lonse ladziko lonse lapansi; Mulungu adzakhala ndi dziko loyera tsopano, lomwe silingadzaipitsidwenso ndi tchimo kulimbana kwa chabwino ndi choipa, pakati pa Kristu ndi Satana kudzakhala kuthatha tsopano ndipo Khristu adzalamulira tchinga likugwa tsopano pa zochitika zonse za tchimo, ndipo kukudza ulemerero wa dziko latsopano lazotheka zambiri-mbiri.

8. DZIKO LIYERETSEDWA KUKHALA LATSOPANO

Kuchokera pa kuyeretsa komaliza uku, Mulungu adzalenga dziko lapansi latsopano.

"Ndipo ndinaona m'mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano, pakuti m'mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidacoka, ndipo kulibenso nyanja… Ndidaona Mzinda woyera, Yerusalemu watsopano, ulikutsika kumwamba kwa Mulungu…. Chihema ca Mulungu ciri mwa anthu, ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ace, ndi Mulungu Yekha adzakhala nao, Mulungu wao; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao, ndi sipadzakhalanso imfa, ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita… Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano." - Chibvumbulutso 21:1-5.

Dziko lapansi litabwezeretsedwa ku ubwino wake ndi kukongola kwake kwa pachiyambi, lidzakhala kwawo kwa muyaya kwa anthu opulumutsidwa. Atamasulidwa kukudzikonda, matenda ndi mazunzo, tidzakhala ndi dziko lonse lakuti tilifufuze kulikhala, mwaubale ndipo kwamuyaya tidzakhala pamapazi a Yesu Khristu, kumumvera, kuphunzira ndi kukonda. (Kuti timve bwino lomwe zambiri za dziko latsopanoli, titha kubwereranso ku phunziro lathu lija lachisanu ndi chinayi).

Kodi inu mukukonzekera kuti mudzakhale kuti pa tsikuli? Kodi mwatsimikiza kukakhala naye Yesu pamodzi mkati mwa mzindawo? Kapena mudzakhala kunja kwa mzindawo kopanda Khristu namukhala otaika mnyanja?

Ngati mwaika moyo wanu m'manja mwa Yesu Khristu, simuyenera kudzaona inu choopsa chosanenekachi cha kwa iwo akukhala kunja kwa mzindawo omwe azindikira kutaika kwawo kwamuyaya. Palibe kanthu kuti mwakumana ndi zotani m'moyo, mukaika moyo wanu m'manja mwa Yesu tsopano lino, mutha kukhala nawo pa gulu la awo okhala mu mzindawo pamodzi ndi Khristu ndi opulumutsidwa.

Ngati simunatero, perekani mitima yanu tsopano lino kwa Yesu, ndipo Iye adzakuzingani inu ndi chikondi ndi chikhululikiro chake. Uwu ndi mwayi wanu, ili ndilo tsiku lanu lachipulumutso lero.

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.