KODI GULU LINGAKHALE LOLAKWA

Mu phunziro lathu lakhumi ndi chisanu ndi chimodzi, tidapeza kuti kuchita nawo mpumulo wa Sabata ndi chinthu chofunika kwambiri ku moyo wathu wopsinjika wa masiku ano. Popeza Mulungu amatimvetsetsa ndi chosowa chathu chiri chonse, adakhazikitsa tsiku lachisanu ndi chiwiri lonse kuti tikapumule ku ntchito zathu zakuthupi ndi kutitsitsimutsa mu uzimu. Atatha kulenga dziko lathu lapansi lonse kwa masiku asanu ndi limodzi, Iye "adapumula" pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, "ndi" kuliyeretsa" tsikuli (Genesis 2:1-3).

Pamene Mulungu adapereka malamulo khumi kwa anthu ake, a Israyeli, Iye adaika lamulo losunga tsiku lachisanu ndi chiwiri monga Sabata ngati chirikati chenicheni cha Malamulo onse (Eksodo 20:8-11). Molingana ndi lamulo limeneli, Sabata ndi lokumbutsa mphamvu ya Mulungu yakulenga, tsiku lakukhala chete ndi kuganizira kukongola ndi zozizwitsa za ntchito ya chilengedwe chake, tsiku lotakasuka ndi kudza pafupi ndi Mlengi wathu, tsiku lofufuza mwakuya za mbale wathu ndi Iye wotilengayo.

M'moyo wa munthu wa Yesu padziko lapansi, Iyenso adasunga Sabata (Luka 4:16) nalitsimikizira kuti liri tsiku lakupindulitsa a Khristu (Marko 2:27, 29). Mavesi ambiri a m'bukhu la Machitidwe akuonetsera poyera molongosola bwino kuti ophunzira ake a Yesu adapembedza pa tsiku la Sabata Yesu atangouka kwa akufa (Machitidwe 13:14; 16:13; 17:2; 18:1-4, 11).

1. FUNSO LOSOKONEZA NDI LOBVUTA

Izi zikutibweretsa ife ku mutu umene anthu ambiri amaona ngati wovuta ndi wosokoneza. Akhristu padziko lonse lapansi akhala kwa nthawi yaitali akupembedza masiku awiri olekana. Mbali inayi, Akhristu ambiri akupempedza tsiku loyamba la pa Mulungu (Sunday), limene akulikhulupirira kuti likumbutsa kuukanso kwa akufa kwa Khristu. Kwinanso, gulu lina lalikulu, loona mtima ngati loyambadi, limakhulupirira kuti Bukhu Lopatulika limazindikira Sabata la pa tsiku lachisanu ndi chiwiri lokha basi ndipo palibe paliponse pamene pakuonetsa kupatulidwa kwa tsiku loyamba la pa Mulungu

Kodi pali kusiyana pakupembedza tsiku lirilonse lomwe munthu afuna ngati Sabata? Monga anthu oona ndi a chilungamo omwe afuna kudziwa choonadi, tiyenera kumadzifunsa nthawi zonse tokha: "Chofunika kwa Yesu ndi chiyani? Kodi Yesu akufuna kuti ine ndichite chiyani?"

Pofika pa chitsimikizo cha Funsoli, mfundo zambiri zofunika ziyenera kulongosoledwa momveka bwino: Adasintha tsiku la Sabata lenileni ndi ndani kulibweretsa ku tsiku loyamba la pa Mulungu? Kodi Baibulo likuvomereza kusinthaku? Ngati ndi choncho, Mulungu kapena Yesu, kapena atumwi ndiwo adapangitsa kusinthaku?,

Tipitirira pakuona za mafunso onsewa ngati ali otheka.

2. KODI MULUNGU ADALISINTHA TSIKULI?

Kodi palipo pamene Mulungu adalengeza kuti wasintha tsiku la Sabata kuchoka ku tsiku la chisanu ndi chiwiri kupita ku tsiku loyamba la pa mulungu?

Akhristu ambiri amavomereza za Malamulo khumi a Mulungu monga chowatsogolera choyenera kukhalira m'moyo, polemba ndi chala chake, kwa mtundu wa anthu. Ali ofunika kwambiri adawalemba iwo pa magome a miyala ndi chala chake (Eksodo 31:18).

Mu lamulo lachinayi Mulungu akutilangiza kuti:
"Uzikumbukira tsiku la Sabata likhale lopatulika. Masiku asanu ndi limodzi uzigwira, ndi kumariza ntchito zako zonse; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la YEHOVA MULUNGU WAKO; usagwire ntchito iri yonse… chifukwa masiku asanu ndi limodzi Yehova adamariza zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zinthu zonse ziri m'menemo, napumula. Tsiku lachisanu ndi chiwiri; chifukwa chache Yehova ANALIDALITSA tsiku la Sabata kuti likhale LOPATULIKA." - Eksodo 20:8-11.

Pamene Mulungu adapereka Malamulo Khumi kwa anthu ake, adaonetseranso poyera kwa iwo kuti munthu ayenera abwereze ndi kulembanso Malamulowa ochokera ndi pakamwa pake Mulunguyo poyera.

'MUSAMAONJEZA pa mau amene ndikuuzani, kapena KUCHOTSAPO, kuti musunge Malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani." - Deuteronomo 4:2.

Mulungu mwini akulonjeza kuti sadzasintha Malamulo ake:
"Sindidzaipsa chipangano changa, kapena kusintha mau oturuka m'milomo yanga." - Masalimo 89:34.

Baibulo liri lomveka bwino kuti Mulungu sadasinthe Sabata kuchoka ku tsiku lachisanu ndi chiwiri kupita ku tsiku loyamba la pa mulungu.

3. NANGA KODI KAPENA YESU NDI YEMWE ADASINTHA SABATA?

Molingana ndi Yesu, Malamulo khumi sasintha:

"Musaganize kuti ndinadza Ine kudzapasula chilamulo kapena aneneri: Sindinadza kupasula, koma kukwaniritsa.
Pakuti indetu ndinena kwa inu, kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kake kamodzi sikadzachokera kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse." - Mateyu 5:17, 18.

Mu phunziro lachikhumi ndi chisanu ndi chimodzi, tidapeza kuti chidali chizolowezi cha Yesu kukapembedza ku sinagoge pa tsiku la Sabata (Luka 4:16). Tidapezanso kuti Yesu adafuna kuti ophunzira ake apitirize chisangalalo cha kusunga Sabata koona (Mateyu 24:20).

Zikuonetsera poyera kupyola mu ziphunzitso za Yesu ndi zitsanzo zake kuti ifebe tikufunika Sabata la kupuma, kutakasuka, ndi kukhala nayo nthawi ndi Mulungu wathu.

4. KODI NANGA ATUMWI NDIWO ADASINTHA SABATA?

Yakobo, mtsogoleri woyamba wa mpingo wa mpingo woyambirira wa a Khristu, adalemba zokhudzana ndi Malamulo khumi:

"Pakuti aliyense angasunge Malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wachimwira onse. Pakuti Iye wakuti 'Usachite chigololo', anatinso 'Usaphe'. Ndipo ukapanda kuchita chigololo, koma ukapha, wakhala wolakwira lamulo." - Yakobo 2:10, 11.

Luka, sing'anga ndi Mlaliki wa uthenga mu mpingo woyambirira, adati:

"Tsiku la Sabata tinaturuka ku mudzi kunka ku mbali ya mtsinje, kumene tinaganizira kuti amapempherako; ndipo tinakhala pansi ndi kulankhula ndi akazi amene adasokhana." - Machitidwe 16:13.

Chipangano Chatsopano, m'buku la Machitidwe mukunenedwa za kupembedza Sabata pafupifupi kwa nthawi makumi asanu ndi atatu mphambu zinayi. Akunenawo ndiwo otsatira ake a Khristu, onse pamodzi okhalako kuposera pa zaka khumi ndi zinayi, kuyambira pamene Yesu adauka kwa akufa: MASABATA awiri ku Antiokeya (Machitidwe 14:14, 42, 44); Sabata imodzi ku Afilipi (Machitidwe 15:13); Masabata atatu ku Atesalonika (machitidwe 17:2-3); Masabata makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi zitatu ku Akorinto (Machitidwe 18:11).

Yohane, womaliza kufa mwa atumwi khumi ndi awiri aja, adasunga Sabata. Ndipo adalemba kuti:

"Ndinagwidwa ndi Mzimu tsikula Ambuye." - Chibvumbulutso 1:10.

Malingana ndi Yesu, tsiku la Ambuye ndilo Sabata.

"Pakuti Mwana wa Munthu ali mwini tsiku la Sabata." - Mateyu 12:8.

Kufufuza umboni m'malembo oyera kwavumbulutsa kuti atumwi sadayeserepo kusintha tsiku la Mulungu la kupuma kuchokera ku tsiku lachisanu ndi chiwiri kupita nalo ku tsiku loyamba la pa mulungu. Chipangano Chatsopano chikutchula tsiku loyamba la pa mulungu maulendo asanu ndi atatu basi. Monsemo sadaonetsemo kuti liri tsiku loyera kapena kuti liyenera kupatulidwa ngati tsiku lopembedza ayi. Kufufuza bwino bwino mwakuya ndi moganizira mosamalitsa za mavesi asanu ndi atatuwa anena za tsiku loyamba la pa mulungu tiona kuti tsikuli lidali ndi zochitika izi:

(1) Akazi adadza kumanda patsiku loyamba la pa mulungu (Mateyu 28:1).
(2) "Pamene Sabata linadutsa," akazi adapitiriza ntchito zawo pa tsiku loyamba lapa mulungu (Mariko 16:1, 2).
(3) Yesu adaonekera koyamba kwa Mariya wa Magadala mawa wa tsiku loyamba lapa mulungu (Marko 16:9).
(4) Otsatira a Yesu adapitiriza ntchito zawo pa tsiku loyamba lapa mulungu (Luka 24:1).
(5) Mariya adapita ku manda a Yesu napeza m'manda muli mbee! Patsiku loyamba la pamulungu (Yohane 20:1).
(6) Akuphunzira a Yesu adasonkhana pamodzi "poopa Ayuda" (osati kudzapembedza ayi) pa tsiku loyamba lopa mulungu (Yohane 20:19).
(7) Paulo adapempha ziwalo za mpingo kuwerengera chuma chawo patsiku loyamba lapa mulungu, ndi "Kupatula ndarama zina" za osanka ku Yerusalemu (1 Akorito16:1, 2). Sikunenapo zakukumanira kwa mpingo kupembedza ayi.
(8) Pa Machitidwe 20:7, Luka akunenapo za kulalikira kwa Paulo pa tsiku loyamba la pamulungu pa msonkhano wapadera wochitikira chifukwa cha kutsazikana ndi abale. Zoonadi Paulo adalalikira, koma iyeyu adali kulalikira tsiku ndi tsiku, ndipo atumwi anali kunyema mkate tsiku ndi tsiku (Machitidwe 2:45).

Palibe vesi lirilonse mwa awa likuonetsera kuti atumwi adaganizapo zoleka kusunga Sabata la tsiku lachisanu ndi chiwiri. Atumwi sadatchulepo zakusintha kuchokera ku tsiku lachisanu ndi chiwiri kupita ku tsiku loyamba lapamulungu. Palibiretu umboni uli wonse mu Chipangano Chatsopano chonse pa zakusinthaku. Kusintha kudadza atatha masiku a Yesu ndi atumwi, choncho tiyenera kubwerera ku mbiri kuti tione kuti zinasintha liti, ndipo zimasintha bwanji:

5. KODI (SUNDAY), TSIKU LOYAMBA LA PAMULUNGU LIDABWERA
BWANJI?

Aneneri akutichenjeza momveka bwino kuti Akhristu ena adzasiya zikhulupiriro zoona za ,"chipangangano Chatsopano cha Ukhristu: "Chotero, chenjerani!" (Machitidwe 20:29-31). Ndipo izi ndizomwe zidachitikadi oona za mbiri mwakuya adalemba za m'mene Akhristu adayambira kutayana ndi chiyero cha utumwi.

Zikhulupiriro zachikunja miyambo zikhulupiriro za uzimu zomwe Paulo, Petro ndi ena omwe adayamba ntchitoyi ya mpingo wa Mulungu sizidapeza njira ina iri yonse yolowera mu Mpingo.

Kusintha kwakusunga Sabata loona kupita ku kusunga tsiku loyamba lapamulungu kudachitika chitatha Chipangano Chatsopano, atumwi onse atafa. Mbiri ikufotokoza kuti a Khristu tsono adayamba pang'ono ndi pang'ono kuchoka ku chipembedzo choona ndi mpumulo wa Sabata wa pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la pamulungu ndi kuyamba kusunga tsiku loyamba lapamulungu.

Komabe sikuti okhulupirira adasiyiratu kusunga Sabata loona ayi ndikupitiratu ku Sabata la chilendoli monga tsiku la Ambuye. Chiyambi chenicheni cha kusiiratu chidali ku dziko la Italy, mkatikati mwa zaka za mazana awiri atafa Khristu. Kwa nthawi yaitali kuchokera pamenepa a Khristu akhala akusunga masiku onse awiri wa pamene enanso akupangabe Sabata loona basi.

Pa 7 Malichi, m'chaka cha A.D. 321, Konsitantini wamkuru adaika lamulo lakupembedza tsiku loyamba lapa mulungu kuti likhale Sabata, kuwakakamiza anthu onse, kupatulapo alimi, aku Roma, kuti azipuma pa tsiku loyambali lamuloli, kuphatikizapo ena asanu omwe Konsitantini adakhazikitsa okhudzana ndi tsiku loyamba lapa mulungu, udapangitsa tsikuli kukhala lokhazikika ndi lamulo kuyambira nthawi imeneyo mpakana lero.

Muzaka za mazana anayi, Bungwe la Lodikaya lidaletsa a Khristu kuti asamasiye kugwira ntchito zawo pa tsiku la Sabata loona, ndi kuwaumiriza kusunga tsiku loyambali lapamulungu posagwira ntchito iri yonse ngati kudali kotheka.

Mbiri ikutisonyezera kuti kupembedza pa tsiku loyamba ndi kutsatira lamulo la munthu. Bukhu Lopatulika silikuvomereza kupembeza pa tsiku loyamba la pa mulungu.

M'neneri Daniel adalosera kuti m'nthawi ya chi Khristu, kudzabwera mphamvu yakunyenga yoyesera kusintha Malamulo a Mulungu (Daniel 7:25).

6. ADASINTHA IZI NDANI?

Kodi ndi ndani adalichotsa Sabata ku tsiku lachisanu ndi chiwiri kupita ku tsiku loyamba lapamulungu? Mpingo wa Katolika umavomereza kuti ndiwo udasintha izi. Adachita izi pofuna kupumitsa ufumu wa Roma womwe munthawiyi unapasuka, kufikira kuti atsogoleri a mpingo adakambirana ndi kugwirizana kusintha tsiku lakupembedza kuchoka ku lachisanu ndi chiwiri kupita ku loyamba lapamulungu.

Katekisima wa mpingo wa katolika amati:
"FUNSO: Kodi tsiku la Sabata ndi liti?
"YANKHO: Tsiku lachisanu ndi chiwiri (Saturday).
"FUNSO: Nanga ndi chifukwa chiyani timapembedza pa tsiku loyamba la pa mulungu (Sunday)?
"YANKHO:Timasunga tsikuli m'malo mwa lachisanu ndi chiwiri chifukwa
Mpingo wa Katolika... udalisintha choncho." Wolemba, Peter Geirmann.
(Zopezeka mu Katekisima wa zikhulupiriro za a Katolika wa 1957, tsamba 50.)

Mpingo wa Katolika umalengeza monyadira kuti atsogoleri a mpingo wa anthu adasintha chotere.

"Tsiku loyera, Sabata, lidasinthidwa chotere- osati motsogozedwa ndi mawu a m'malembo opatulika ayi koma mwa mphamvu yomwe mpingo udaziona kuti uli nazo... Anthu omwe akuona kuti udindo wonse wa zinthu ngati izi wagonera pa mawu a Mulungu, malemba ake oyera, ayenera kukhala ziwalo za mpingo wa "Seventh-day Adventist", ndi kusunga Sabata loona, kukhala "Loyera" (Zonenedwa ndi Cardinal Maida Bishop
wamkuru wa ku mpingo wa Katolika wa Catherine woyera ku Detroit, Algonac, Michigani, May 21,1995).

7. NANGA MIPINGO INA YA MPATUKO IKUTIPO CHIYANI?

Zolembera zokhazikitsidwa zoonetsa zikhulupiriro za mipingo ingapo yamipatuko zikugwirizana ndi kunena kuti Baibulo silinapereke udindo wakusintha kuti anthu adzipembedza pa tsiku loyamba lapamlungu.

Martin Luther, yemwe adayambitsa mpingo wa chi "Lutheran", adalemba mkulapa kwake kuti:
"Iwo (mpingo wa Katoloka) akunena kuti Sabata lidasintha kuchokera kutsiku lachisano ndi chiwiri kupita ku tsiku loyamba lapamlungu, tsiku la Ambuye, kusemphana ndi (Malamulo Khumi)… ndipo palibe chomwe amachinyadira koposa ngati kusintha uku komwe adakupanga kukhala kotheka. Iwonso akunena modzikweza kuti, mphamvu yawo ndi yaikuru koposa ya utsogoleri wa mpingo wawo, chifukwa idatha kusintha limodzi la Malamulo Khumi a Mulungu." (Augsbury Compession, Arbele 28, paragraph 9.)

Woona za chipembedzo m'maphunziro a chi "Methodist", Amos Binney ndi Daniel Steele adaona izi:
"Ndi zoona, palibe chochitira umboni ubatizo wa ana akhanda…. Kapena kusunga tsiku loyamba lapamlungu monga Sabata." (Theological Compend New York: Methodist Book Concern, 1902) tsamba 180, 181.

Dr, N Summerbell, woona za mbiri ya ophunzira a Yesu Khristu kapena mpingo wake, adalemba:
"Mpingo wachi Roma udapatutsa kwathunthu… udasintha lamulo lachinayi la Mulungu pochotsa Sabata la Mawu a Mulungu, ndi kuikapo Sabata lawo la patsiku loyamba lapamlungu kukhala loyera" - (A Time Ministry of the Christian and the Christain Church, tsamba 417, 418).

8. KODI NKHANI YAIKURU APA NDI ITI?

Mutu uwu ukutibweretsa maso ndi maso kuti: Ndichifukwa chiyani anthu ambiri achi Khristu akupembedza patsiku loyamba lapamlungu limene Baibulo silimavomereza? Chofunikiranso kuposa apa, ndi tsiku liti lomwe ndiyenera kulisunga? Kodi nditsatire awo akuti" palibe kusiyana pa tsiku lomwe munthu asankha kupembedza bola ngati ndikusunga limodzi pa mlungu"? kapena/ iwo amene akuti; Kodi ndisunge kukhala tsiku lomwe Yesu, Mlengi wathu, pamene a malenga dziko lathu lapansi , ndi tsiku lomwe Mulungu adalionetsera m'malamulo ake khumi: tsiku lachisanu ndi chiwiri kukhala Sabata?"

Apa tikulimbana ndi zoposa kusunga kuonetsera kunja koma nkhani ndi yoti, kodi tsiku lenileni loonekera kuti liri lenileni mu Baibulo ndi liti? Nkhani yaikuru apo ndi kumumvera Yesu. Mlengi wathu adapatula Sabata monga tsiku loyera", nthawi yathu ndi mabanja athu kuti tidze chifupi ndi Iye kupezako mphamvu ndi chitsitsimutso. Kodi ndimvere yani? Ndimvere Khristu, Mwana wa Mulungu, kapena miyambo ya munthu pa za tsiku loyenera kulisunga kukhala loyera? Chisankho ndichoonekeratu poyera: Ziphunzitso za anthu kapena lamulo la Mulungu. Mawu a munthu kapena Mawu a Mulungu. Munthu wolowa m'malo kapena lamulo loyera.
Mneneri Daniel akuchenjeza kolimba kwa iwo akuyesera "Kusintha nthawi zoikika ndi chilamulo" (Daniel 7:25) "Kapena ofuna kusintha nthawi ndi chilamulo" (Daniel 7:25).
Mulungu akuitanira anthu ake kuti abwere kwa Iye.. Akuwaitanira iwo ku kusunga Sabata ngati chizindikiro cha kumvera ndi chikondi chawo pa Iye.

Yesu anati, "Ngati mukonda Ine, sungani Malamulo anga" (Yohane 14:15). Ndipo akulonjeza chisangalalo chathunthu kwa iwo akumukonda, Iye ali nafe chidwi kuti tipeze chikondi chake chathunthu. Mtima wa munthu wofuna kumvera umatheka kutseguka mokwanira ku chikondi chimenechi.

M'munda wa Getsemane, Khristu adadzipereka kwathunthu ku chifuniro cha Atate wake - ngakhale adakomana nawo mtanda ndikuti machimo a dziko lonse adachotsa moyo wake. Pamene analirira kwa Mulungu, "Chikho ichi chindipitirire" adakhalabe wodzipereka mkudandaula kwake, ndi adatinso, "Koma osati monga mwa kufuna kwanga ayi, koma kufuna kwanu" (Marko 14:36).

Khristu akufuna ife tikapeze chikwaniritso chomwe moyo wodzipereka moona umabweretsa. Ndiponso Iye akufuna kuti ife tikapeze chisangalalo cha mpumulo wa Sabata. Iye akufuna ife kuti timukhulupirire ndi kumudalira Iye kwathunthu pomumvera mu zochitika zonse za m'moyo. Ngati mubvomereza kuitana kwa Mulungu uku ndi kumumvera pa Malamulo ake onse, mudzalandira lonjezo la Yesu loti mtendere wake udzakhala "wa inu" ndipo "chisangalalo chanu" chidzakhala "chathunthu" (Yohane 15:11).

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.