CHINSINSI CHA KUKULA KUPYOLERA MU CHIYANJANO

Kumayambiriro a zaka za 1960, mbale Andrew, mwamuna wochokera ku Holland, m'dziko la Romania kudutsa oyang'anira a chi "Communist" pa chipatapo. Adakapeza malo okhala ku Hotela nayamba kupemphera kuti Mulungu amutsogolere iye ku gulu loyenera la Chikhristu-limene lingathe kugwiritsa bwino ntchito ma Baibulo omwe adabweretsawo.

Kumapeto a Sabata imeneyo, Andrew adapita kwa kalaliki wa mu Hotelayo namufunsa za komwe angathe kukapeza Kachisi.

Kalalikiyo adamuyang'ana iye mwachilendo namuyakha kuti, "Tiribe anthu ambiri otero kuno, iwenso ukudziwa. Pambali pa izi, iwenso siutha chiyankhulidwe chakuno".

"Kodi sudadziwe eti?" adayankha Andrew,

"Akhristu amayankhula chiyankhulo chimodzi."

"Ooh! Ndiye chiti chimenecho?" "Chimatchedwa Agape"(chikondi chopanda malire).

Kalalikiyu adali asadamvepo za izi, koma Andrew adamutsimikizira iye nati "Ndicho chiyankhulo chabwino koposa padziko lonse lapansi.

Andrew adatha kupeza mipingo ingapo m,deralo natha kukumana ndi wamkulu ndi mlembi wa mpingo wina wake, Mwatsoka, ngakhale Andrew ndi amunawa adatha kuyankhula ndi kumva ziyankhulo zingapo za ku Ulaya, adapeza kuti mwa ziyankhulo zonsezo, padalibe chomwe amatha kumvana. Ndiye adangokhala nkumangoyang'anana wina ndi m'nzache. Andrew adali atayenda mitunda yambiri yoopsa ndi katundu wake wamtengo wapataliyu, koma sadatha kupeza ngati amuna awa omwe adakumana nawo adalidi akhristu eni eni abale kapena akazitape (azondi) a Boma. Pamapeto pake adapeza Baibulo lachiyankhulo cha chi Romania chakumeneko. Ndipo Andrew adatulutsa Baibulo lachiyankhulo cha chi Dutch nthumba lake. Adavundukula pa 1 Akorinto 16:20. Nalisiya chomwecho, naloza pa dzina la bukhulo lomwe adatha kulizindikira. Nthawi yomweyo nkhope za anthuwo zidawala. Mwachangu anapeza mutu womwewo ndi vesi lake mu ma Baibulo awo achiyankhulo cha Chi Romania nawerenga: "Abale onse kuno akupereka moni. Mupatsane moni ndi kupsopsona koyera."

Anthuwo adawalira pa Andrew, ndipo wina wa iwo adapeza mu Baibulo lake pa Miyambo 25:25 ndipo Andrew adalipeza vesili nawerenga: "Monga madzi ku moyo wothodwa ndiwo Mau a Uthenga Wabwino kudziko lachilendo."

Anthuwa adakhala theka la ora kukambirana ndi kugawana za m' Mawu a M'Baibulo basi, Adali okondwa kwambiri mukugawanaku mwakuti padalibenso kusankhana ziyankhulo ndi zikhulupiriro ndipo adafika poseka chikhakhaza kufikira misozi idaturuka m'maso mwawo.

Andrew adadziwa kuti wapeza abale ake. Pamene adawaonetsa iwo katundu wa ma Baibulo aja, anthu a ku Romania awa adakondwera koposa namukumbatira mobwereza bwereza.

Usiku umenewo, ku Hotelayi, kalaliki uja adapita kwa Andrew nati, Nena, ndayang'ana tanthauzo la liwo loti "Agape" mu bukhu lamatanthauzo a mawu. Palibe chilankhulo cha mtundu umenewo. Ili, koma, ndi liwu la mu chi Herene lotanthauza Chikondi."

Andrew adamuyankha nati, "Ndi choncho ndithu. Ndinayankhula m'chomwechi masana onse."

Kodi mwapeza chilankhulo chabwinochi? Mu phunziro iri, muphunzira za m'mene Mulungu angatibweretsere tonse pa bwalo lake limodzi lalikuklu la chikondi.

1. MPINGO WOKHAZIKITSIDWIRA KUKUMANIRA PAMODZI

Yesu adakhazikitsa mpingo ndi cholinga chokwaniritsa chofunika pa munthu kuti asamalidwe ndi kuthandizidwa. Tonse tiri ndi zosowa. Ndicho cholinga cha mpingo. Iwo ndi malo omwe timayanjana ndi kuthandizana wina ndi muzake. Mau opatulika akutivumbulutsira za mpingo waukulu wa atumwi omwe udaitana amuna ndi akazi kukapempedzera limodzi mokondwa kufikira mpaka kwa wamphamvu zonsezo.

"Chimene tidachiona, ndipo tidachimva, tikulalikirani inunso mukayanjane pamodzi ndi ife, ndipo chiyanjano chathu chirinso ndi Atate, ndipo ndi mwana wake Yesu Khristu; ndipo izi tilemba ife, kuti chimwemwe chathu chikakwaniridwe." - Yohane 1:3, 4.

Gulu la anthu lomangika pamodzi ndi mitima yawo kupyolera mukulumikizana ndi Yesu komanso ndi wina ndi m'nzake, limapeza "Chisangalalo" chathunthu! Onse amayankhula chiyankhulo chimodzi chiyankhulo cha chikondi.

Akhristu amakhala mbali imodzi ya banja losefukira. Amakhala abale ndi alongo mwa Khristu popeza onse amakhala ndi mzimu umodzi wapfuko limodzi. Pamene mgwirizano woterowu ukula niukhala ndi anthu ambiri, mphamvu za m'gwirizanowu zimakhalanso zolimba pakati pa a Khristu.

Ziwalo za mpingo wokhazikitsidwa atumwi, ndi atumwi a Yesu, udamangika pamodzi mwazikhulupiriro zofanana, chikondi chawo pa Mulungu, ndi kukhumba kwawo kumutumikira Iye ndi kugawira ena za Chisomo Chake ku dziko lapansi. Kulumikizana kwenikweni uku kwa kupembedzera pamodzi kudali chifukwa chimodzi chomwe chidapangitsa kuti mtundu uwu wa anthu ochepa, opanda mphamvu ndi ozunzidwa ndi kuphedwa ulitembenuze dziko chadodolido.

2. MPINGO WOMWE KHRISU ADAKHAZIKITSA

Kodi Khristu ali ndi mpingo? Kapena cholinga cha kukhala ndi gulu kapena bungwe lachipembedzo chidali chifuniro cha munthu? Yesu akuyankha:

"Ndipo pa thanthwe ili ndidzakhazikitsa mpingo wanga, ndipo makomo a dziko la a kufa sadzaulaka uwo." - Mateyu 16:18.

Yesu ndiye thanthwe lokhazikika, mwala wapangodya, wa Mpingo wake.

Kodi ndi gulu lotani lomwe linapanga mbali ya maziko?

Omangika pa maziko a a tumwi ndi aneneri, pali Khristu Yesu mwini, mwala wa pangodya." - Aefeso 2:20.

Yesu Ambuye adakwaniritsa chiyani pamene uthenga udalalikidwa?

"Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe." - Machitidwe 2:47.

Pamene Yesu adakhazikitsa mpingo, adalonjeza kuti" "Makomo a gehena sadzaulaka uwo" (Mateyu 16:18), ndipo mpingo wa Khristu upirirabe chipiririre. Wakhala uli ndi adani amphamvu - kuyambira maufumu a Roma kufikira ku olamuliro ankhanza wa komunisiti - koma mwazi wa iwo omwe adafera uthengawu udapangitsa mpingowu kukula ndi mphamvu. Pamene wopembedza m'modzi anatenthedwa kapena naponyedwa ku mikango, ena ambiri adauka kulowa m'malo mwake. Akaligwiritsa adayesetsa kuchinyonyosola chipembedzo cha chikhristu. Koma choonadi cha chikhristu chapikisana nawo bwino lomwe kuposa kale mu mbadwo wa sayansi ndi chikunja.

Chobetchera chachikuru chimodzi cha Mpingo chidadza pamene udaloledwa ndi boma la Aroma kukhala chipembedzo chodziwika mu ufumuwu. Mpingo udakula mopambana - koma pamapeto pake udaipitsidwa. Udaoneka wakufa mu uzimu mu nthawi yochedwa ya mdima (Dark Ages). Koma Ambuye adasunga nthawi zonse Akhristu olimba mtima ndi okhulupirika omwe mu nthawi yamavuto ndi yowawitsa, adaonetserabe kuwala ngati nyenyezi mu usiku wopanda mwezi.

Paulo akuyerekezera ubale wa a Khristu ku Mpingo wake ndi chiyanjano cha mwamuna chakuteteza mosamalitsa mkazi wake (Aefeso 5:23-25). Mpingo ndi banja, ndipo chiwalo chiri chonse chiri kukhazikitsa ubale weni weni ndi chiwalo chinzake cha m;banjalo, ku chitapo kanthu mu zonse zothandiza pa banjalo (Aefeso 2:19).

Paulo akuyerekezeranso mpingo ngati thupi, ndi Khristu mwini wake ngati mutu wake (Akolose 1:18).

Pamene tabatizidwa, timaonetsera poyera ku chikhulupiriro chathu mwa Yesu ndi kukhala ziwalo za "thupi", mpingo.

"Pakutinso mwa Mzimu m'modzi, ife tonse tinabatizidwa kulowa m'thupi limodzi." - 1 Akorito 12:13.

Bukhu la Chibvumbulutso likutionetsera Khristu woukitsidwa akuyenda pakati pa mipingo, kuyionetsera chisamaliro chake (Chibvumbulutso1:20, 12, 13). Khristu sanawasiyepo anthu ake okha, ndipo sadzatero ayi.

3. MPINGO WA CHOLINGA

Kupita kukapembedza kumpingo m'chofunika kwa Mkhristu. Timasowa thandizo la ena kuti chikhulupiriro chathu chikhalebe chamoyo ndi kukula.

Mpingo uli ndi zofunika zitatu izi:
(1) Mpingo umasamalira choonadi.
Monga "Mwala wa maziko wa choonadi" (!Timoteo 3:15). Mpingo umagwiriziza ndi kuteteza choonadi cha Mulungu padziko lapansi: Tiyenera ife nzeru zamgwirizano za anthu opembedza kuti zitithandize ife kuona choonadi chenicheni chofunika cha m'malembo oyera.
(2) Mpingo uli chitsanzo cha zomwe chisomo cha Mulungu chimachitira munthu wochimwa.
Kusintha komwe Khristu amachititsa m'miyoyo ya anthu okhulupirira kumachitira umboni za Mulungu yemwe amatitchula ife kutiitanira"Mukuwala kwake kozizwitsa" (1 Petro 2:9).
(3) Anthu ake a Mulungu ali mboni zake ku dziko lonse ndi zosowa zake.
Yesu asanabwerere kunka kumwamba, Iye adawalonjeza akuphunzira ake:
"Koma mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: Ndipo mudzakhala mboni zanga M'Yerusalemu, ndi M'Yudeya lonse, ndi m'Samariya, ndi kufikira malekezero ace a dziko." - Machitidwe 1:8.

Ndi mwayi waukuru kuti Mpingo utengere uthenga wa chikondi chachikuru cha Mulungu kudziko lonse lapansi.

4. WOKHAZIKIDWA KUTI UKHALE NDI MPHAMVU

Mpingo womwe Khristu adakhazikitsa udali ndi dongosolo lolozeka. Munthu amatha kulowetsedwa, komanso kuchotsedwa monga Chiwalo cha Mpingo ( Matenyu 18:15-18). Mpingo wa Mulungu umasankha atsogoleri ndipo unali ndi likulu lake padziko lino komanso malo ang'onoan'gono okomanirako (Machitidwe 8:14; 14:23, 15:2; 1 Timoteo 3:1-13) Pamene adabatizidwa, okhulupirirawo amalowa gulu lokhazikitsidwa mwadongosolo (Machitidwe 2:41 ndi 47).

Mpingo uli ndi cholinga cha kulimbikitsana

"Ndipo tiganizirane wina ndi mzache kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku (lakudza Khristu) lirikuyandika." - Ahebri 10:24, 25.

Izi, mwachidule, ndizo zomwe gulu la mpingo wathanzi umachita ziwalo zake zimakulitsana m'chikhulupiriro, ndi kulimbikitsana. Mulungu adalinganiza mpingo wake kuti ulimbikitse anthu a Mulunguyo ndi kutumikiranso dziko lapansi. Titha kuchita zambiri ndi zoposa m'chigulu kusiyana ndi pamene tichita mwatokha. Tangoonani inu chitsanzo chimodzi chokha.

Mpingo wosunga Sabata poyembekezera kudzanso kwachiwiri kwa Khristu (Seventh-Day Adventist): Timafalitsa uthenga wabwino kupyolera mu ntchito zachipatala padziko lonse lapansi -kugwiritsa ntchito zipatala zoyenda m'magalimoto m'mizinda ikuluikulu ndi m'midzi ndi zipatala zing'onozing'ono m'midzi yokhala kwaokha kapena zisumbu kumwera kwa Pacific. Masukulu athu abweretsera makumi azikwi za achinyamata ku chidziwitso cha moyo wabwino mwa Khristu - kuyambira ku sukulu yaukachenjede yaikulu ya Loma Linda, komwe amaphunzitsa ngakhale ntchito ya madotolo yakusintha chiwalo cha mtima mwa munthu; kufikira ku timasukulu ting'onoting'ono tachimishoni tomwe tawanda mkati monse mwa Afirika.

Koma timalimbana ndi ngozi ndi njala popereka chithandizo kupyolera mu bungwe la ADRA. Mipingo ing'onoing'ono ikudyetsa anthu ndi kuwapatsa zovala ovutika ndi opanda pokhala mu malo zikwi zikwi a chithandizowa. Ndipo magulu ambirimbiri osiyanasiyana a chi Adventist akugawira uthenga uwu wachipulumutso mu maiko osachepera mazana awiri. Ndigulu lokhalo lokhazikitsidwa mwa dongosolo lokhala ndi a Khristu odzipereka lomwe lingathe kukhala ndi chikoka chokhudza dziko lonse motere.

Khristu ndi atumwi adayerekezera mpingo ndi thupi, nalongosola kuti ziwalo zonse za thupi ndi zofunika (a Akorinto 12:21-28). Ziwalo zonse zathupi sizofanana ayi, koma zonse ziri zofunika kwambiri ndipo ziyenera kugwirira ntchito pamodzi mogwirizana.

Diso lomwe lachotsedwa pa thupi silingaone. Mkono wolekanitsidwa ndi thupi ulibe ntchito. Kaya ife ndife diso kapena mkono, kapena chala, sitingakhale otakataka mwa phindu pa za Khristu pa tokha ayi.

Kukhala chiwalo cha mpingo, kulumikizitsidwa ku ziwalo zina za thupi, kumatipatsa ife mphamvu monga a Khristu.

5. THE JOY OF WORSHIP

Chimwemwe cha kupembedza. Mkatikati mwa mitima yathu muli chikhumbo khumbo chopembedza Mulungu, ndipo chikhumbo khumbo ichi chitha kufota ngati sitichionetsera. Kodi wolemba Masalimo adamva bwanji poganizira za kupita ku malo opembedzera?

"Ndinakondwera m'mene ananena nane tiyeni ku nyumba ya Yehova." - Masalimo 122:1.

Kodi nyimbo ziri ndi mbali yanji pakupembedza pagulu?

"Tumikira Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kumyimbira mokondwera." - Masalimo 100:2.

Baibulo likutiuza ife kuti kupereka zopereka ndi mbali inanso yoyenera ya kupembedza koyera.

"Bwerani nacho chopereka, ndipo fikani ku mabwalo ace. Gwadirani Yehova woyera ndi mokometsetsa." - Masalmo 96:8-9.

Pemphero lirinso chofunikira chachikuru chakupembedza kwa pagulu.

"Tiyeni, tipembedze tiwerame, tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga." - Masalmo 95:6.

Kuphunzira Baibulo ndi kulalikira ziri mbali za pa chilikati penipeni pa chipembedzo cha m'chipangano Chatsopano. Kuyambira pa ulaliki wa Petro pa tsiku la Pentekoste, wopezeka mu Machitidwe 2, komanso kuyambira munthawi ya otsutsa okonzanso kuti choonadi chisasokonezeke kufikira m;masiku athu ano, chitsitsimutso chirichonse cha uzimu cha chipembedzo chagonera pa kulalikira za mu Baibulo. Nanga ndi chifukwa chiyani? Ndichifukwa chakuti "Mawu a Mulungu ndi a moyo ndi akuchitachita. Akuthwa kuposa lupanga lakuthwa konsekonse" (Ahebri 4:12-13).

6. CHOYENERA NDI CHITI NDI MPINGO?

Ena amatsutsa zoti mpingo wadzala ndi anthu osalungama. Koma zomwe munthu wina wochedwa Henry Kland Beecher adanena ndi zoona zoti, "Mipingo simalo oonetsera anthu woyera okhaokha ayi, koma uli Sukulu yakuphunzitsa osayenerawo kukhala oyenera."

Popeza palibe m'modzi waife amene ali wangwiro, Mpingo sudzakhalanso wangwiro. Yesu, mmafanizo ake, limodzi la iwo likutikumbutsa kuti nansongole ndi tirigu zimakulira pamodzi (Mateyu 13:24-30). Tikawerenga m'Chipangano Chatsopano, m'makalata a Paulo, tipeza kuti mpingo wa atumwi udali ndi mabvuto oopsa. Ndiponso mpingo wa lero uli ndi zilema zake. Koma, chonde, kumbukirani kuti palibe mpingo wa zifukwa umene ungaononge kapena kujejemetsa mwala wa pangodya wa mpingo - Yesu Khristu mwini. Tsono, mu Mpingo wathu wosakhala ndi anthu angwirowo tiyenera kulunjika maso pa Mpulumutsi yemwe amatitumikira. Pambali pazovutozo, Mpingo uli wa mwini wake Yesu, ndiye yanga'nirani pa Khristu.

"Khristu anakonda Eklesia (Mpingo) nadzipereka yekha m'malo mwace kuti akampatule, atamyeretsa ndi kumsambitsa madzi ndi mawu; kuti iye akadziikire yekha Eklesia wa ulemerero, wopanda banga kapena khwinya, kapena kanthu kotere; komatu kuti akhale woyera, ndi wopanda chilema." - Aefeso 5:25-27.

Mpingo ndi wofunika kwambiri kwa Yesu kotero kuti "Adadzipereka yekha chifukwa cha Mpingo " pamene adafera munthu wina aliyense payekhapayekha ndi mpingo wonse pamodzi. Chotero kukhala ziwalo za mpingo zikhale zofunikiranso kwa inu. Kodi ndinu chiwalo cha thupi la Khristu?

7. KUPEZA MPINGO

Kodi ndi zipembedzo zoona zingati zomwe Yesu ali nazo pa dziko lapasi?

"Thupi limodzi ndi Mzimu umodzi,… Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi." - Aefeso 4:4, 5.

Popeza Khristu ali ndi "Chikhulupiriro chimodzi" chokha basi, nanga tingachidziwe bwanji? Yesu akutipatsa ife mfungulo wake wopezera:

"Ngati munthu ali yense afuna kuchita chifuniro chake (Mulungu), adzazindikira za chimphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa ine ndekha." - Yohane 7:17. (onaninso pa Yohane 8:31, 32).

Pamene tipanga chitsimikizo kuchita chifuniro cha Mulungu, Iye adzatithandiza kuona ngati chiphunzitsocho chiri chochokera kwa Iye kapena chiri chopangidwa ndi mwambo wa munthu,. Pofuna kupeza mpingo woyenera, tiyenera kuyesa kumvera kwake ku Mawu a Mulungu, chagonera pa Mawu a Mulungu, osati pa mtsogoleri wamphamvu wa mpingowo kapenanso kukula kwa mpingo ayi.

Pitirizani kufufuza mu maphunziro athuwa yendani m'kuunika pamene Mulungu akuvumbulutsira kwa inu kuchokera m'Bukhu Lopatulika, ndipo adzaonetsera momveka bwino cholinga chake pa inu

Mkhristu yemwe akukula ndi munthu amene atsegula mtima ndi maganizo ake kulandira choonadi monga m'mene Mulungu akuchivumbulutsira kuchokera Mawu ake.

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.