KULOWA MMOYO WACHIKHRISTU

Nayi kalata yopatsa chidwi yochokera kwa m'modzi wa ophunzira athu a Baibulo mu Afrika:

"Zaka zisanu zapitazo ndidalandira kalata ya pempho yochokera ku Mawu a Mzimu wa Chinenero kuti ndikayendere wa ndende wina yemwe amapanga nawo maphunziro a Baibulo pa makalata ndidaipereka kalata yopemphayo kwa akuluakulu oyan'ganira kundendeko omwe mwa chisomo adavomereza pempholo. Popeza kuti mphunziyu adali ndi chidwi kuphunzira Baibulo, ndinkamuchezera pafupi-pafupi.

"Patatha pafupi-fupi miyezi isanu ndi umodzi chiyambire kumuchezerera kuja, adafunsa kuti abatizidwe ndi kulowa mu mpingo. Oyang'anira ndende aja adapereka zipangizo za ubatizo kuti uchitikire mundende momwemo. Oyang'anira akaidi pamodzi ndi akaidi enanso adasonkhana kuchitira umboni umodzi mwa maubatizo opambana ndi osangalatsa omwe ndidabatizapo.

"Patangopita nthawi pang'ono chichitikire ubatizowo, mbaleyu adamasulidwa, ngakhalebe idali nthawi yake isadakwane yomasulidwa. Pamene ndidafunsa kuti izi zachitika bwanji, ndidauzidwa kuti moyo wake udasintha modabwitsa, ndipo adachitira umboni za Khristu Mpulumutsi wake ndi mpingo wake moti sanaonekenso ngati mkaidi, kapena kuchitiridwa ngati mmodzi wa iwo ayi. Munthuyu adalunzanitsidwa ndi banja lake moti panopa ndi mtsogoleri wa umodzi mwa mipingo yathu ikuluikulu"

1. KODI TANTHAUZO LA UBATIZO NDI CHIYANI?

Pamene wandendeyu adakhala Mkristu ndipo moyo wake nusinthika, ndi chifukwa chiyani kuti abatizidwe? Pokambirana ndi Nikodemo, mtsogoleri wa anthu anadza kwa Yesu usiku, ndipo Yesu namuonetsera poyera kufunika ndi tanthauzo la ubatizo:

"Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sakhoza kuona ufumu wa Mulungu… ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa ufumu wa Mulungu." - Yohane 3:3, 5.

Mukufotokoza kwake kwa Yesu tiyenera ife kubadwa "Mwa madzi ndi Mzimu". Kubadwa mwa Mzimu kumaimira kulowa moyo watsopano posinthika maganizo ndi mtima. Popeza kulowa ufumu wakumwamba kumafunika moyo wosinthika watsopanodi, osati moyo wakale wokhala ndi zigamba za makhalidwe osiyanasiyana ayi, ndipo uku kumatchedwa kubadwanso mwatsopano.

Ubatizo wa madzi ndi chionetsero cha kunja kwa thupi choonetsa kusinthika kwa mkati. Wotiyimira wathu anabatiza wa ndende uja kusonyeza kudzipereka kwake kwa Kristu ndi chiyerekezero cha kusinthika komwe Mzimu woyera udayambitsa mkhalidwe lake.

2. KODI NDIBATIZIDWE CHIFUKWA CHIYANI?

Chipulumutso chathu chimazungulira mu ntchito zazikuru zitatu za Khristu.

"Khristu anafera zoipa zathu monga mwa malembo;… anaikidwa; ndikuti anaukitsidwa tsiku lachitatu, monga mwa malembo." - Akorinto 15:3, 4.

Khristu anachipanga chipulumutso kukhala chotheka kupyolera mu imfa, kuikidwa mmanda ndi kuuka kwake kwa akufa.

"Kapena kodi simudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu tinabatizidwa mu imfa yache? Chifukwa chache tinaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo kulowa muimfa; kuti monga Kristu anaukitsidwa kwa akufa mwa ulemerero wa Atate, chotero ifenso tikayende m'moyo watsopano." - Aroma 6:3, 4.

Yesu adafera zochimwa zathu, naikidwa m'manda, ndipo nauka m'manda kutipatsa ife moyo watsopano wa chiyero. Tikabatizidwa timachita nawo mu imfa, kuikidwa ndi kuuka kwa Yesu. Ubatizo utanthauza kuti tafa ku uchimo, ndi Khristu kuika mmanda moyo wakale wa uchimo ndi Khristu ndipo mkuuka kukhala mmoyo watsopano mwa Khristu. Imfa ndi kuuka kwa Khristu ziri imfa ndi kuuka kwathunso. Mulungu angatipange ife kufa ku tchimo, ngati kuti tidapachikidwanso. Atha kutikhazikitsa ife amoyo ku zinthu za Uzimu, monga ngati kuti tauka kwa akufa. Ubatizo weni-weni umaimira makwerero akutembenuka. Choyamba, polowetsedwa mmadzi, kumizidwa kwathunthu, monga m'mene anthu akufa amatsitsidwira m'manda nakwiriridwa. Izi zikunena kuti ali olola kufa naye Yesu ndi kukwirira moyo wathu wakale. Ubatizo ndi maliro, kutsazikana ndi khalidwe lomwe uchimo unalenga malo. Chachiwiri, timakwezedwa poturutsidwa m'madzi ndi uyo wobatizayo, monganso munthu woukitsidwa kwa akufa. Izi zikunena kuti ndife "cholengedwa chatsopano" choperekedweratu ku "Moyo watsopano" womwe Mulungu amatipatsa. Ndi kumizidwa kokha mmadzi komwe kungapereke tanthauzo leni leni la ubatizo - kufa, kukwiriridwa ndi kubadwanso "Ubatizo" owaza madzi suli wokwanira kuimira kubadwanso mwatsopano, zimatanthauza chiyani kufa pamodzi ndi Khristuyo?

"Podziwa ichi, kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye, kuti thupi la uchimo likaonongeke, kuti ife tisakhalenso akapolo a uchimo." - Aroma 6:6.

Ubatizo umaimira moonekera zomwe munthu ayenera kuchita mkati kupereka zonse kwa Yesu. Tikasunga kena kake kubisila Mulungu, ndi chachidziwikire kuti tidzakhalabe mu "ukapolo wa tchimo". Pamene tidzipereka kwathunthu kwa Kristu, zilakolako zathu za uchimo zimasandulika "zopanda mphamvu," ndipo kusinthika kwathu kumayambika. Kodi yemwe amapangitsa kuti kusinthaku kuchitike ndani?

"Ndinapachikidwa ndi Khristu; koma ndiri ndi moyo wosatinso ine ai, koma Khristu ali ndi moyo mwa ine; koma moyo umene ndiri nao tsopano mthupi ndiri nao m'chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine." - Agalatiya 2:20.

Ndikakhala mbali ya kupachikidwa kwa Khristu kupyolera mu ubatizo, ndimaitana mphamvu yaikuru m'moyo wanga. "Kristu amakhala mwa ine" Pofuna kuika moyo wanu kwathunthu mmanja mwa Khristu, choyamba muoneni Khristu akufa pa mtanda. Musayang'ane patchimo lomwe likukuopsezani, musayang'anenso moyo wanu wakale ndi kumva nawo chisoni; yang'anani kwa Yesu. Poona imfa yolimba mtima ndi yachisomo ya Yesu pa Karivale, mungathe kuonetsera kuvomereza kwanu ndi Iye. "Mwa mphamvu ya mtanda ndikudzitenga kuti ndafa ku zizolowezi zoipa zakale ndikubvomera kwa Mulungu. Ndikupanga chitsimikizo changa ndi Kristu. Kuyambira tsopano kupita mtsogolo, ndidzakhala mwa chikhulupiriro mwa mwana wa Mulungu, yemwe adandikonda nandzipereka Yekha mmalo mwanga." Pamene tilawa mphamvu ya imfa ya Khristu ndi kuuka kwake timaona zambiri zaubwino wake zikulowa mmalo mwa zizolowezi zathu zakale zoipa.

"Chifukwa cace ngati munthu ali yense ali mwa Khristu ali wolengedwa watsopano, zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano." - 2 Askorinto 5:17.

Kupyolera mu ubatizo, timaonetsera khumbo lathu logwirana manja ndi Yesu kuti tikakhale moyo watsopano ndi wabwino "Mwa Khristu." Yesu amatichitira ife zomwe ife tokha sitingathe kudzichitira. Timaturuka m'madzi cholengedwa chatsopano; Iye amatipatsa mphamvu yokhalira moyo watsopano.

3. NDI CHIFUKWA CHIYANI YESU ANABATIZIDWA?

Pa tsiku la Pentekoste, Petro adawauza omwe amafuna kumasulidwa ku chitsutso kuti "mulape ndi kubatizidwa" kuti Khristu akukhululukire "zochimwa zanu" (Machitidwe 2:38). Popeza Yesu sadachimwepo m'kamodzi komwe, nanga adalola bwanji kuti abatizidwe?

"Pamenepo Yesu anachokera ku Galileya nadza ku Yordano kwa Yohane, kudzabatizidwa ndi Iye,… kukwaniritsa chilungamo chonse motero." - Mateyu 3:13, 15.

Yesu adali wopanda tchimo. Adalibe choti alape koma adabatizidwa pa chifukwa china; "kukwaniritsa chilungamo chonse." Pobatizidwa, Yesu adaonetsa chitsanzo chabwino kwa ife anthu ofooka, ochimwa. Khristu sadafunsepo omutsatira ake kupita komwe iye sadafikeko. Choncho pamene wokhulupirira amizidwa m'madzi aubatizo, akungotsatira m'mapazi a Mbuye wawo. Pakuti Kristu adafera machimo athu, athanso kutipatsa chilungamo chake.

"Ameneyo sanadziwa uchimo namuyesera ucimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo ca Mulungu mwa Iye." - 2 Akorinto 5:21.

Kusinthidwa pamaso pa Mulungu kuchoka wochimwa kusandulika woyera, timakula kukhala "chilungamocho" potero timakhala moyo watsopano mwa Yesu.

4. NDI CHIFUKWA CHIYANI NDIYENERA KUMIZIDWA?

Khristu anamizidwa pa ubatizo wake, Iye sadawazidwe madzi. Yohane adam'batiza Iye mu mtsinje wa Yordano "chifukwa mudali madzi ambiri" (Yohane 3:23). pamene Yesu anabatizidwa, adalowa m'madzi ndipo "atangobatizidwa (kumizidwa) adaturuka m'madzi (Mateyu 3:16).

Tikamvetsetsa tanthauzo leni-leni la ubatizo, sitibvutikanso kudziwa mtundu weni weni waubatizo liwu lokhalo loti "ubatizo" linachoka ku chi Herene, liwu loti "Baptizo", kutanthauza kumiza (kulowa pansi). Pamene John Wesley amacheza ku Amerika mu chaka cha 1737, gulu la mpingo loweruza la anthu makumi atatu ndi anayi lidamupatsa mlandu chifukwa "chokana kubatiza mwana wa bambo Parker, ubatizo wina uliwonse woposa kumiza." Pali umboni woti tate wa mpingo wachi Methodist adabatiza otembenuka ake powamiza.

Wokonzanso John Calvin adati : "Ndichokhazikika ndithu kuti ubatizo womiza udayamba ndi mpingo wakalelo." - Institute of the Christian Religion Bk 4 chapt. 15 Dec 19. Mbiri ya mpingo wakale imaonetseratu poyera kuti ubatizo koma womiza. Dean Stanley, wa mpingo wa ku Mangalande, adalemba kuti," "Kwa zaka mazana khumi ndi anayi zoyambirira, ubatizo wa dziko lonse udali womwe tawerenga mu Chipangano chatsopanochi, womwenso uli tanthauzo la " kubatiza" - kuti iwo omwe adabatizidwa, adalowetsedwa, kumizidwa m'madzi." - Christian Institutions p. 21.

Malo obatizira akhristu momiza akupezeka m'makachisi ambiri omwe adamangidwa pakati pa zaka za mazana anayi ndi mazana khumi ndi anayi ku Ulaya ndi ku Asiya, monga ku kachisi wamkulu wa ku Pisa, ku Italy ndi St. John, kachisi wamkuru kwambiri ku Roma. Kubatiza mowaza madzi kudayambika pamene khonsolo ya ku Ravenna ya mpingo wa katolika idavomereza kuwaza kuti ndi kofanana ndi kumiza mu zaka zoyambirira za mu zaka za mazana khumi ndi asanu.

Pochita za mpingo, sitiyenera kutsatira zomwe munthu ophunzitsa koma zomwe Khristu ndi atumwi ake akuphunzitsa. Akhristu ambiri oona mtima amatsatira mwambo wobatiza wana, ndi kuwapereka ana athu kwa Mulungu kuyambira pa chiyambi. Izi ndi zololeka. Komabe bukhu lopatulika, likuonetsera poyera kuti munthu ayenera kuphunzitsidwa njira ya chipulumutso asadabatizidwe (Mateyu 28:19, 20) kuti munthu ayenera akhulupirire mwa Yesu asanabatizidwe (Machitidwe 8:35-38) ndikutinso munthu alape machimo ake ndi kukhululukidwa asanabatizidwe (Macitidwe 2:38).

Mwana wakhanda sangathe kukhulupirira, kulapa, kapena kuulula mphulupulu, zomwe ziyenera kuchitika munthu asanabatizidwe.

5. KODI NKOFUNIKA BWANJI KUBATIZIDWA?

Monga mwa kunena kwa Yesu, ubatizo ndi wofunika kwa iwo ofuna kukalowa kumwamba:
"Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sakhoza kulowa Ufumu wa Mulungu." - Yohane 3:5.

Yesu akungopereka chitsanzo chapadera. Mbala ya pamtanda ija idabadwa mwa Mzimu" ngakhale sadathe kuchoka pamtanda paja kuti akamizidwe mu ubatizo monga chizindikiro chakulapa kwake ndi kusintha mtima kwake. Ndipo Yesu adamulonjeza iye kukakhala naye mu Ufumu wake (Luka 23:42, 43). Kwa mbalayi, "kubadwa mwa madzi ndi Mzimu" kudaimiridwa ndi mwazi wa Yesu wokhetsedwa kumuyeretsa iye ku machimo ake.

Augustine adaonetsetsa mosamala, "kuti umboni umodzi basi wolembedwa wa kulapa uli pafupi kufa, ndiko kwa mbala ya pa mtanda, sizoti wina ataye mtima, chifukwa ndi yekhayo basi, palibenso."

Yesu adapereka chenjezo iri:
"Amene akhulupirira nabatizidwa, adzapulumutsidwa; koma amene sakhulupirira adzalangidwa." - Marko 16:16.

Pofa mmalo mwathu pa Karivari, Yesu adaonetsera poyera chikondi chake pa ife. Tiyenera kubvomerezanso poyera, polapa mopanda kuchita manyazi za kudzipereka kwathu kwa Khristu mu ubatizo. Kodi mwayamba moyo watsopano mwa Yesu Khristu? Kodi mwabatizidwa? Ngati siziri choncho, bwanji wosakonzekera kuti mudzabatizidwe m'tsogolomo?

6. UBATIZO NDICHO CHIYAMBI CHABE

Ubatizo umaimira kudzipereka kwathu ku moyo wa chi Khristu. Koma kudzipereka kwathu ku ubatizo sikukhala nthawi zonse. Mwana akabadwa, kumakhala kofunika kusangalala, tsiku lobadwa likadutsa ndi chisangalalo chija chitha, mwanayo amafunika kudya tsiku ndi tsiku, kusamba, ndi kumuchitira zofunika zake zonse tsiku ndi tsiku. Ndi chomwechonso ndi ubatizo.

Paulo ananena motere pa zomwe adakumana nazo, "Ndimafa tsiku ndi tsiku" (1 Akorinto 15:31). Mwa kubwerera kuchoka ku kudzikonda tsiku ndi tsiku, timakhala tikuyankha moyenera kwa Khristu moonjezera. Mwambo wa ubatizo, monganso wa ukwati woyera, zaikidwa kukhala chitsimikizo kuti ubale wayambika ndi wokula. Kuti ubalewo ukulebe kosalekeza, tiyenera kudzipereka tokha tsiku ndi tsiku kwa Khristu, kulandira moyo watsopano tsiku ndi tsiku mwakupemphera ndi kuphunzira Baibulo.

7. CHIFUKWA CHOSANGALALIRA

Ubatizo uyenera kukhala chifukwa chosangalalira, chifukwa omwe aika chikhulupiriro mwa Yesu ali ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. "Yense amene akhulupirira nabatizidwa adzapulumutsidwa" (Marko 16:16). Pamene tibatizidwa, tiri pa ulendo wokwera kunka ku chikondwerero chosatha.

Ubatizo ndi chikondwerero cha chimwemwechi cha lero ndi Yesu. Iye akulonjeza mphatso yaulele ya Mzimu woyera kwa iwo obatizidwa (Machitidwe 2:38). Mzimu umadza ndi zipatso za Mzimu "Chikondi," chomwe chimadzaza moyo ndi "kufatsa, chifundo, ubwino, kukhulupirika, kudekha ndi kudziletsa" (Agalatiya 5:22-23).

Kukhala ndi Yesu mwa ife mwa Mzimu wake woyera kumatipatsa chikhalidwe cheni-cheni chakuya. Popezanso Mzimuyo mwini achitira izi umboni… kuti ife tiri ana a Mulungu" (Aroma 8:15,16). Ubale wathu wotetezedwa pakati pathu ndi Mulungu umatibweretsera ife zabwino zambiri, koma sichitsimikizo kuti sitingakumane ndi mabvuto ayi. Ndiponsotu, mdaniyo amayesetsa nthawi zambiri kubweretsa mavuto ochuruka kwa iwo amene angodzipereka kumene kwa Khristu.

Komabe, ngati tilumikizana manja athu ndi a Mulungu, tidzadziwa kuti Iye atha kugwiritsa ntchito chiri chonse chomwe Iye akufuna kwa ife kuti chichitike, chabwino ngakhale choipa, kutipulumutsa ndi kutithandiza kuti tikule (werengani Aroma 8:28).

Mayi wina wachisungwana adapanga chitsimikizo choti apereke moyo wake kwa Khristu ndi kubatizidwa ngakhale mwamuna wake adamuwopseza kuti amuleka ukwati akangochita zimenezo. Bambo samafunafuna mpangono pomwe kusiya chikhulupiriro chake, chatsopanocho komabe anaumirira kwa Yesu nakhala wachikondi chachikuru kuonetsera kwa mamuna wake. Koposa kale kwa kanthawi, mwamunayu anayesetsa kumapanga zinthu zoti mayiyu azivutika pakhomopo. Koma pamapeto pake adagonja pa mafunso omwe sadathe kuyankha. Kusinthika kwa moyo wa mayiyu. Mwamunayu adaupereka moyo wake kwa Yesu ndipo nayenso adabatizidwa.

Kuumirira chifupi ndi Yesu Khristu "mu nthawi zowawitsa ndi zokoma" kudzatipanga ife kukhala zida zamphamvu m'manja mwake. Titha kuipereka miyoyo yathu kwa Iye mopanda kukaikira chifukwa Iye adadzipereka kale kwa ife pamene adalipira dipo laulere la machimo athu pa mtanda paja. Mwayitu nanga uwu wakuti tikanene poyera, kumupatsa Iye chikondi chathu ndi kumumvera Iye! Ngati simunachite kale izi, bwanji osatero tsopano. Mufunseni Iye kuti akulengereni moyo watsopano mwa inu mwa mphamvu ya Mzimu woyera, ndi kuti mubatizidwa mwa Khristu.

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.