CHINSINSI CHA MOYO WA THANZI

Akatswiri azofufuzafufuza azunzika ndi ntchito yawo kuti alembe zoonadi za zaka zomwe ziri mu Baibulo kuyambira pachiyambi: Anthu ali athunthu mu chipangidwe chakutumikira kwawo.

Chomwe ife tigawa kuti mwina chiri cha thupi, maganizo ndi uzimu pa munthu zimakhala zogwirizana ndipo zosalekanitsika. Mwa njira ina, tinganene kuti, chomwe chikhudza maganizo, chikhudzanso thupi. Uzimu wathu umakhudzana ndi umunthu wathu ndiponso umunthuwu uli ndi mbali yaikulu pa uzimu wathu. Ife ndife anthu.

Mwachitsanzo, ofufuza motumbatumba amapeza kuti kukondwa, chimwemwe, kuseka zimapanga mu mphamvu yachitetezo ya m'thupi la munthu. Mutha kuthandiza thupi kumenyana ndi matenda mokwanira pakungokhala wokondwa basi! Maphunziro awa amaonetsera mwapafupi thupi ndi maganizo zimagwirira ntchto pamodzi.

Zaka zikwi zapitazo Mawu a Mulungu adaonetsera kugwirizana kumene kulipo pakati pa maganizo ndi thupi zomwe ziri zovomerezekanso kwa malamulo a zachipatala.

"Mtima wosekerera uchiritsa bwino, koma mzimu wosweka uphwetsa mafupa." - Miyambo 17:22.

Molingana ndi zomwe Mtumwi Yohane, akufotokoza za mgwirizano wa maganizo ndi thupi ku Uzimu wathu.

"Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhala bwino, monga mzimu wako ulemera." - 3 Yohane 2.

Mlengi wathu akufuna ife "Tikhale ndi umoyo wathanzi labwino." Mau a Mulungu atha kukhalanso kasupe wathu wathanzi, komanso wa moyo wosatha.

Popeza thupi ndi maganizo ndi uzimu wathu zimayendera pamodzi munchito zawo, Paulo akudandaulira motere:

"Chifukwa cace mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena , citani zonse ku ulemerero wa Mulungu." - 1 Akorito 10:31.

Uthengawu ukuphatikiza kubweretsa zonse za ku thupi ndi za Uzimu. Moyo wathanzi umathandiza ife kukhala akhristu amphamvu ndi amachawi.

Pano pali njira zisanu ndi zitatu zoyenera kutsatilidwa pofuna kuthandiza kukhala ndi moyo wa thanzi komanso opambana.

1. MPWEYA WABWINO

Mpweya wabwino ndi watsopano ndi ofunika pa thanzi kuti likhale labwino. M'nthawi ya tsiku komanso usiku pogona, mpweya wabwino m'nyumba zathu ndim'malo athu ogwirira ntchito uli wofunika kuti magazi athu athe kukhala ndi mbali ija yofunika ya mpweya (oxygen) kuti awutumize kumbali zonse za thupi. Kupumira mpweya wokwanira m'thupi lathu poyenda ndi njira imodzi yopambana kuti thupi likhale ndi mpweya okwanira.

Mpweya umene tipumira m'thupi uli wofunika koposa. Tiyeni tipewe kupumiramo mpweya womwe uli wosafunika komanso oononga. Kusuta kumaononga mpweya ndipo kumapha. Ofufuza motumbatumba apeza ndi kukhazikitsa mfundo yakuti kusuta fodya ndiko kumayambitsa matenda a m'mapapo a mtima ndi ena otero chilako lako cha fodya chikakhazikika zimavuta kuleka kusuta. Tisakokere mthupi mwathu mosasamala mpweya uli wonse woipa ndi zina zamajeremusi zoyambitsa matenda, kusuta fodya kumaononga mpweya ndipo ndi m'mene imfa zambiri zikubwerera chifukwa amapha. Azofufuzafufuza motumba apeza ndi kukhazikitsa mfundo yoti nthenda yam'mapapo imayambika chifukwa chosuta fodya, ndiponso kumayambitsa matenda a mtima ndinso kusokonezeka kwa njira ya mpweya.

Thupi lozoloweretsedwa kusuta fodya limakhala lovuta kuti lidzasiye kusuta chifukwa mankhwala a ululu amufodyamo otchedwa "NIKOTINE" amapangitsa munthu kukhala wofuna kusuta nthawi zonse. Molingana ndi zotumbatumba Kusuta fodya kudzapha anthu zikwi zikwi khumi ndi ziwiri pa chaka mpaka kufikira m'chaka cha 2020 ngati anthu sasintha.

2. KUWALA KWA DZUWA

"Ubwino wa dzuwa ndi wambiri:
(i) Kukhala padzuwa mphindi kuyambira khumi ndi zisanu mpaka makumi atatu m'mawa uliwonse kapena madzulo kumathandiza thupi kuti lithe kupanga ndi kugwiritsa ntchito lokha vitamin D; yemwe ali wofunika kwambiri ku khungu lathu. Ndipo amathandiza magazi kupanga Calcium ndi "Phosphorous" zomwe zimamanga ndi kulimbitsa mafupa athu.

(ii) Dzuwa limakhalanso ngati lopha tizilombo toyambitsa matenda pakhungu monga Bacteria.

(iii) Dzuwa limapereka mphamvu ku zomera zosinthira mpweya wa Carbon Dioxide ndi madzi kuti zikhale chakudya… popanda m'chitidwe umenewu, nyama ndi anthu zingathe kufa ndi njala

(iv) Dzuwa limathandizanso munthu kuti athe kugwira bwino ntchito za usiku ndi kupuma ku zolemetsa zakubwera chifukwa cha usiku wautali wa nyengo za nthawi yozizira (yavuma).

(v) Chenjezo dzuwa lithanso kukhala loipa. Kukhala nthawi yaitali kwambiri padzuwa kutha kuwaula khungu, ndi kuyambitsanso matenda a pa khungu; kumakalambitsanso msanga, ndiponso kumaononga maso ndi kuyambitsa ng'ala. (zonsezizikupezeka mu bukhu la zathanzi lotchedwa "Yang'ana Kumwamba kuti ukhale ndi Moyo" lachingerezi)lomwe lidali Kotale wa maphumziro a Baibulo woyamba m"chaka cha 1993.

3. KUPUMULA

Thupi likuyenera kumapuma kuti lidzipangire lokha mobwezera momwe mwaonongeka. Tiyenera kukhala ndi nthawi yachisangalalo ndi kupuma kuti tipepukidwe ku zolemetsa za ntchito ndi mabanja. Popanda kupuma mokwanira, anthu amakhala olefuka, ndi osachedwa kunyasidwa ndi zochitika. Zoterezi zitha kuyambitsa matenda omwe amakhala ngati chotikakamiza kuti tibwezere kupuma komwe tidakukana kwa nthawi yaitali. Palibe choposa kupuma kwa usiku pogona.

Chinanso chofunika pa thanzi lathu ndiko kukonzanso moyo wathu wauzimu tsiku ndi tsiku. M'khristu wochita nawo mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku powerenga ndi kuphunzira ndi kupemphera adzachiza thupi lake ndi mzimu wake. Tiyeneranso ife kupuma ku ntchito zathu za nthawi ndi nthawi, pakupuma kamodzi tsiku lonse pa Mulungu, komanso pokhala ndi maholide a pachaka ndi pakati pachaka.

4. MACHITA CHITA OLIMBITSA THUPI

Machitachita olimbitsa thupi ali ofunika kwambiri ku thupi lathu motere:
(i) "Amatithandiza kuteteza matenda a kuthamanga magazi.
(ii) "Amathandiza magazi ambiri kuti afikire mbali zonse za thupi lathu, ndi kuti pali ponse pakhale pofundira.
(iii) "Amathandiza kuchotsa zipsinjo za thupi ndi za maganizo zomwe; zimapangitsa kumva bwino moyo. Machitachita olimbitsa thupi ndiwo machiritso ku madandaulo ndi kuthodwa nkhawa.
(iv) "Amatipatsa ife mphamvu ngati zamagetsi ku ubongo wathu ndi mbali zing'ono zing'ono za minyewa yathu, zomwe zimafikitsa paliponse poyenera zochitika zonse za m'thupi. Ndipo zimalimbitsa thanzi lathu polithandiza mu mphamvu ya thupi yomenyana ndi kuteteza matenda. Thupi likakhala lochitachita masewera

(v) olimbitsa thupi, maganizo amakhala ogwira bwino ntchito ndi achangu poganiza zinthu zatsopano zabwino.
(vi) "Amathandiza ku maonekedwe a thupi lanu ndi ku kusungani pa muyeso woyenera.
(vii) "Amakupangitsani kukhala a mphamvu zoposa, kuti musamatopa pakugwira ntchito ngakhale poganiza.

(viii) "Amathandiza bongo kuti udzipanga mankhwala omwe amapangitsa umunthu wabwino ndi kuonjezera mphamvu yakuti muzitha kupirira ku zowawa. Ngati simunayambepo kuchita masewera olimbitsa thupi, yambani tsopano pang'ono pang'ono ndipo nkumaonjezera pang'ono nthawi iriyonse. Mutha kuwapeza a dotolo anu kuti akulangizeni musanayambe kupanga machitachita. Cholinga chanu chikhale kuchita nawo masewero aliwonse olimbitsa thupi omwe angafanane ndi kuyenda mtunda umodzi kwa mphindi khumi ndi zisanu, kanayi kapena kupitirirapo pa Sabata iriyonse.

5. MADZI

Popeza madzi ndi ofunika kwambiri ku mbali iri yonse yochepetsetsa ya thupi lathu, tiyenera kumamwa kowirikiza.

"1. Pakulemera konse kwa thupi lathu, madzi ndiwo apanga mbali yayikulu pafupifupi maperesenti makumi asanu ndi awiri ndiwo madzi mthupi lathu.

"2. Thupi limafuna madzi osachepera mabotolo (malita) awiri patsiku kuti ligwire bwino ntchito zake zonse. Zina mwa ntchitozo ndizo kuyenda kwa magazi, kuchotsa zoipa m'thupi, kuyenda kwa chakudya ndi kugaya kwa chakudya.

"3. Munthu aliyense ali ndi pafupifupi zikwi zikwi pakati pa khumi ndi zisanu ndi makumi anayi za maselo (mbali zochepetsetsa zomwe zipanga) ku ubongo. Selo ina iri ndi pafupifupi maperesenti makumi asanu ndi awiri kapena asanu ndi atatu a madzi. Madzi okwanira ku maselo amenewa amathandiza kukhazikitsa maganizo abwino ndi oongoka kwa munthu, ndipo amateteza kukhumudwa ndi kukhudzidwa ndi zochitika monyansidwa.

"4. Simadzi okhawo omwe mumwa ali ofunika, kusamba madzi ozizira bwino tsiku ndi tsiku kumathandizanso, ku machitidwe a zoyendayenda mthupi; kupatsa mphamvu thupi ndi ubongo. Kusambakunso kumathandiza MINYEWA yomwe yosokonezeka, yomwe INGATHE kuyambitsa matenda popangitsa mphamvu yathupi yachitetezo kumatenda kukhala yofooka. Kusamba m'thupi kumachotsa zoipa zonse pa khungu ndipo kumachepetsa kutentha kwa thupi.

6. CHAKUDYA CHABWINO

Pachilengedwe, Mulungu adalangiza Adamu ndi Hava kuti adye mtedza, mtengo wakubala mbewu ndi therere, komanso zipatso (Genesis 1:29). Adamu ndi Hava atachimwa, masamba adaonjezeredwa ku chakudya chawo (Genesis 3:18) chitatha chigumula, Mlengiyo adaonjezera "Nyama yosadetsedwa" ku chakudya chawo(Genesis 7:2-3, 9:1-6).

Nyama ziri ndi mafuta ambiri komanso otchedwa "Cholesterol", omwe amaonjezera ngozi ya matenda aja akuthamanga kwa magazi kwakukuru, kufa kwa ziwalo za thupi, matenda a mtima, matenda a ndaka, kunenepa koipa, matenda a shuga ndi matenda ena ambiri. Lero lino, madotolo ambiri amalangiza iwo amene amadya nyama kuti achepetse madyedwewo, kapena aiphike bwino nyamayo ndi nsomba mosamalitsa.

Popeza anthu omwe amadya masamba okhaokha amakhala athanzi ndi a moyo wautali, akatswiri ambiri oona zachakudya ndi thanzi amatiumiriza ife kudya zomwe zidapatsidwa kwa makolo athu pachiyambi monga mtedza, mbeu ndi zipatso komanso kuonjezerapo masamba.

Ngati mufuna kuti mudzidya masamba, yambani mwaona ndi kudziwa mbali za chakudya chofunikira m'thupi zomwe zingapezeka popanda nyama. Idyani zipatso zosiyanasiyana kasanu kapena kasanu ndi kamodzi patsiku, komanso mtedza ndi mbewu, masamba ndi mtundu wonse wanyemba.

Masamba obiriwira komanso a chikasu, kuphatikizapo zipatso ndi zofunika
kwambiri. gwiritsani ntchito ufa wa mtengo wakubala mbewu ndi mpunga womwe si woyera koma woderapo pachakudya chanu. Kudya zakudya zolimbitsa thupi zokhala ndi starichi kukhale kasanu ndi kamodzi kapena kupitirirapo patsiku. M'malo modya nyama ndi mafuta ake (monga "butter kirimu ndi zina) idyani mafuta a mtedza, chakudya tanenachi ndi chokwanira popanda nyama ngati mugwiritsanso ntchito zakudya zopangidwa ku mkaka.

Iwo amene asankha kudya nyama monga mbali yachakudya chawo, adye nyama zomwe Bukhu Lopatulika likuvomereza kuti ndi "Zoyera" kapena zoyenera pa munthu kuti zidyedwe. Pamene Mulungu adaloleza anthu kudya nyama, chitatha chigumula (Genesis 7:2-3) (Levitiko 11:47), adawauza nyama zake zomwe ziri zoyenera ndi zomwe ziri zosayenera kudyedwa.

Weregani mutu wa khumi ndi chimodzi wa Levitiko komanso wa khumi ndi chinayi wa Deuteronomo za mundandanda wa mbalame, nyama zamtchire ndi nsomba zomwe Mulungu adazitcha zoyenera kudyedwa. Potsatira mitu imeneyi, nyama zoyenera zikhale zogawanika ziboda ndi zobyikula. Nsomba zoyenera zikhale ndi mamba. Mbalame zodya nyama ndi zosayenera kudyedwa.

Mwa nyama zosayenera kuzidyazi, nkhumba ndiyo yomwe yatchulidwapo ndi kuletsedwa (Deuteronomo 14:8). Matupi ambiri a anthu aipitsidwa ndi matenda oopsa a nyongolosi zotchedwa "trichimae" nyongolosi zazing'onozi zimafalitsidwa kwa anthu podya nyama ya nkhumba. Chifukwa china chingakhale kuipa kwa kuchuluka kwa mafuta mu ziwalo zogaya chakudya za muthupi la munthu.

7. PEWANI ZINTHU ZAULULU

Kodi Baibulo likuchenjezanji pa zamowa (Kachasu)?

"Vinyo achita chiphwete, chakumwa chaukali chisokosa; wosochera nazo alibe nzeru." - Miyambo 20:1.

"Kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa ufumu wa Mulungu." - Akorito 6:10.

Kachaso (mankhwala aululu opezeka mu mowa) amasokoneza zochitika zofunika zathupi izi:

"1. Mphamvu yachitetezo cha mthupi - kachaso amachepetsa maselo a magazi oyera omwe amamenyana ndi matenda m'thupi, potero thupi limakhala pachoopsa chogwidwa ndi chibayo, chifuwa chachikulu, matenda a chiwindi, ndi matenda a ndaka a mitundu yosiyanasiyana.

"2. Mphamvu yakupangitsa zochitika zonse za mthupi potulutsa zoyenerera zache mthupimo. Kumwa kawiri kapena katatu kokha patsiku kwa zoledzeratsa kumapangitsa amayi kupita padera ngati ali oyembekezera, kubereka ana akufa kale, ndi kubereka nthawi isanakwane.

"3. Mphamvu ya kuyenda kwa magazi m'thupi lonse. Kumwa mowa kumaonjezera ngozi ya matenda a mitima, kuchepetsa shuga m'magazimo komanso kukweza mafuta m'magazi ndi kuthamanga kwa magazi, omwe ali matenda oopsa kwambiri.

"4. Kugaya kwa zakudya muthupi. Mowa umasokoneza m'mimba kupangitsa kuti idzitaya magazi. Kuchokera kukumwa mowa kumabweretsa mafuta m'chiwindi zomwe zimayambitsa matenda a chiwindi ambiri mbiri."

Mowa ndiwo umapangitsa anthu ambiri kudzipha okha, komanso kufa pa ngozi zapamsewu, kuzunza ana ndi nkhanza za pa nyumba.

8. KHULUPIRIRANI MU MPHAMVU YA MULUNGU

Munthu yemwe ali ndi mantha kapena atatsutsika saona phindu lakuchita zathanzi zomwe tanenazi. Koma munthu yemwe akusangalala m'chikhulupiriro cha Mulungu moyenera adzapeza gwero leni-leni la umoyo wabwino:

"Lemekezani YEHOVA, moyo wanga ndi kusaiwala zokoma zache zonse atichitirazi: Amene akhululukira mphulupulu zake zonse; nachiritsa nthenda zako zonse. Amene aombola moyo wako ungaonongeke." - Masalimo 103:2-4.

Munthu wina wotchedwa Davide Larson, woona za anthu amisala ku chipata china ku America, adapanga kafukufuku wamkuru pazakugwirizana kwa Chikhristu ndi thanzi labwino. Kufufuza kwake kudaonetsera kuti zinthuzi ndi zogwirizana kwambiri. Anadabwanso kupeza kuti anthu omwe amapita kukapembeza ku kachisi amakhala moyo wautali kuposa omwe sapita, ndipo opita ku kachisiwa sagwidwa gwidwa ndi matenda ambiri a magazi ndi mtima ayi. Omwe akhulupira mwa Mulunguwa, amakhala moyo waphindu chifukwa sakhumudwa, kuti mpaka akayambe kumwa mowa, kapena kukhala m'ndende chifukwa cha kulakwira kawiri kawiri kapena kukhala ndi banja losakondwa ayi kukhulupira mu mphamvu ya Mulungu yoyera ndilo khwerero lakukhala moyo wabwino, wathanzi ndi wokondwa.

Pafupifupi akhristu zikwi makumi asanu a chi Seventh-Day adafufuzidwa ku dziko la California, kwa zaka zoposa makuni atatu. Zotsatira zaka zinali zoti amuna a chi Adventist amakhala zaka pafupifupi zisanu ndi zinayi zoonjezera ndipo akazi, pafupifupi zaka zisanu ndi zitatu zoonjezera poyerekeza ndi amuna kapena akazi ena onse.

Zotsatira za ku Holland, Norway ndi Poland, zikusonyezanso chimodzimodzi. Ofufuzawa apeza kuti izi ziri chomwechi chifukwa cha mfundo za thanzi zomwe amuna ndi akazi ambiri a Seventh-day Adventist amatsatira, monga zomwe tanena mu phunziroli. Onse amene amatsatira mfundozi sangokhala kokha ndi moyo wautali ayi, komanso moyowo umakhala wabwino ndi wosiririka.

Kugwiritsa ntchito Baibulu ndi mau ake pa moyo wathu zikutisiyanitsa ife muzochitika zonse mudziko ndipo zimatipatsa njira zenizeni, zokhutitsa ndi umboni wakuti chikhristu ndi chipembedzo chenicheni, chofanizira m'zochitika m'dziko. Chimawasintha anthu - kupyolera m'maganizo komanso m'machitidwe awo- ndi kuwatengera ku moyo wamachitidwe atsopano.

Chifukwa cha kugwirizana kwa maganizo, thupi ndi moyo wathu wauzimu, Akhristu okhazikika ndi mau a Mulungu adzafuna kutsatira mfundo za moyo wa thanzi pamene akukonzekera kubweranso kwachiwiri kwa Yesu (Yohane 3:1-33). Khristu sangofuna kokha kuti tikonzekere kukumana naye pamene adzabweranso ayi. Koma akufunanso kupanga miyoyo yathu yaleroyi kukhala yabwino ndi yolongosoka. Tithe kugwirizana naye pa izi pongotsatira mfundo za moyo wa thanzizi.

Yesu akulonjeza kutimasula ife ku chizolowezi chakuchionongeko, kupyolera mu "Mphamvu yake yomwe iri pa ntchito mwa ife" (Aefeso 3:20). Ngati mukufuna kuthana ndi makhalidwe kapena zizolowezi zomwe zimaononga thupi monga kumwa mowa ndi kusuta fodya, thandizo lanu loposa la kusiya izi ndi kuitana mphamvu ya Mulungu yomwe imagwira ndipo ikugwira ntchito "Mwa Inu" Panokha simungathe. Mulungu atha kukupatsani mphamvu zogonjetsera. Mawu a Mulungu akulonjeza: "Nditha kuchita zonse mwa Khristu yemwe amandipatsa ine mphamvu" (Afilipi 4:13).

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.