CHINSINSI CHAKUKULA KUPYOLERA MUKUGAWANA

Larry ankasangalala ndi kukambirana kosangalatsa, kokhudzana ndi tiyi wa ku Japani, zakudya zophikidwa kuchokera ku mpunga, kunyumba kwa Komori, pamene alendo ena adayamba kutulutsa ma Baibulo awo. Onse adamuyang'ana iye ndi chiyembekezo."kodi mungatipatse mutu wa kukambirana kwathu lero? Amafunsa bambo Komori....

Larry anali pafupi kutsamwa ndi Tiyiyu.Iye anaganiza kuti kucheza kwawo kudali kodzangosangalala limodzi basi. Ndipo panopa sanathe kupeza choti angagawane nawo anzakewo.

Larry adaphunzitsapo m'makalasi, maphunziro ambiri amu Baibulo pa sukulu ina yophunzitsa chiyankhulo cha chingerezi ku Japan komwe anagwirako ntchito. Komanso onsewo ankayamba wawakonzekera kaye. Ankatha kupereka maphunzirowo mosavuta. Koma kuti angoyankhula mwadzidzi…zinali zosiyana.

Larry adamvapo nthano zonse zamu Baibulo kuyambira ali mwana. Koma sizinkatanthauza kanthu kwenikweni kwa iye payenkha. Ankachita zinthu zomwe iye ankadziwiratu kuti ndizolakwika pamaso pa Mulungu. Ndiye akadayankhula bwanji kwa ena za Mulungu yemwe iye mwini wake sanamudziwe?

Choncho, ali chikhalire pa mpando wasofa, mozunguliridwa ndi anzake omuyembekeza aja, kuyerekeza kwake kudatsala pang'ono kutha. Nthawi yomweyo ali ndi mantha, vesi lamu Baibulo linafikira iye mumtima mwake lonena zamphamvu ya mzimu woyera wotipatsa ife mau oti tinene tiri pakati pa anthu oti tiwachitire umboni (Luka 12:12). Adapezeka atayamba kulongosola nthano yomwe adaiganiza ya: mwana wolowerera.

Mmene analongosola momwe Mulungu amatikondera ife ngakhale ndi omwe asocherera kutari ndi iye, Larry adapezeka akulankhula zochokera pansi pa mtima wake. Mawu ake amanka natsikiratsikirabe kwa nthawi yoyamba m'moyo mwake, Larry adazindikira kuti Mulungu amamukonda iye kwambiri.

Usiku umenewo Larry adagwada pansi pa pakama wake napereka moyo wake kwa Mulungu yemwe pamapeto pake adakhala weni weni kwa iye. Kugawana zachikondi cha Mulungu zidapangitsa chinthu choposa kukhala wongodziwa zinsinsizo. Panopa sizidalinso nkhambakamwa ayi koma zenizeni zomuchenutsa iye.


1. YESU AKUTIBETCHERA KUTI TIKAKULE POGAWANA MAWU AKE

Ophunzira a Yesu adakhala zaka zitatu nditheka akuphunzira mawu a Khristu ndi kuona ntchito zake, komanso imfa yake ndi kuukanso kwake. Pamene Yesu anali pafupi kubwerera kumwamba, adawatuma ophunzirawo kuti akakhale akazembe ake.

"KOMATU MUDZALANDIRA MPHAMVU, Mzimu woyera atadza pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga m'Yerusalemu… ndi kufikira malekezero ace a dziko." - Macitidwe 1:8.

Pamene otsatira ake a Yesu adali pa Pentekoste kupereka mitima yawo mosakayika kwa Iye, Khristu woukitsidwayo adasintha miyoyo yawo ndi mphamvu za mzimu woyera. Adasandulika mboni, osati za kuuka kwa ku thupi kwa Yesu Khristu ndi kukwera kwake kunka kumwamba kokha ayi, komanso za mphamvu zake za kuukitsa zomwe zidasintha miyoyo yawo.

Ife monga akhristu, ndifenso mboni ya pa zakuuka kwa Yesu chifukwa ife talandira ndi kuona nawo mphamvu yakusintha mwatsopano m'miyoyo yathuyi.

"Koma Mulungu wolemera cifundo, cifukwa ca cikondi cace cacikuru cimene anatikonda naco, tingakhale tinali akufa m'zolakwa zathu, anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu (muli opulumitsidwa ndi cisomo)…kuti akaonetsere m,nyengo zirinkudza cuma coposa ca cisomo cace, m'kukoma mtima kwa pa Iye mwa Yesu Khristu."
- Aefeso 2:4-7.

Ife tapangidwa a moyo ndi Khristu kuti tikathe "kuonetsa chuma chosayerekezeka cha chisomo chake." Ndipo akutifunsa ife kuti tifalitsire uthenga wabwinowu, wa zomwe Iye amachita m'moyo wamunthu, ku dziko lonse lapansi, ndikutilonjeza kunka nafe kulikonse kumene tikagwira ntchitoyi (Mateyu 28:19-20).

Munthu wina wotchedwa H.M.S. Richards, Yemwe adayambitsa utumiki wa Mawu a Chinenero wachinenero wa pa wailesi, adachitira umboni wotere nthawi ina:
"Ndaona kusintha m'mitima ya anthu amene anamva uthenga wa Yesu Khristu. Ndayenda m'malo m'mene dzina la Mulungu ndi la Khristu samadziwidwa mpaka pamene mpingo wake udatengerako uthengawu. Ndaona anthu akusintha kuchoka ku moyo wonyansa kupita ku moyo woyera, kuchoka kumatenda kupita ku thanzi, kuchoka ku mantha wosatha a mizimu yoipa kunka ku chisangalalo cha chikhristu. Ndaona ine kusintha kwa amayi okhala m'banja. Ndaonanso mabanja a chikhristu enieni akuchoka ku moyo wachikunja. M'dela lirilonse limene ndayendako ndaona miyoyo ikusintha. Ndikudziwa kuti "uthenga wabwino wa Khristu… uli mphamvu ya Mulungu ya ku chipulumutso" (Aroma 1:16). Ndikudziwa kuti pamene mpingo ufalitsa uthengawu, kusintha kumachitika m'mitima ya anthu ndi mabanja awo, ndipo izi zimaonekera m'miyoyo ya awo amene avomereza kudandauliraku."

Mulungu watipatsa ife anthu amene tiri ofoka mbali yapadera yoti tichite mu ntchito yake yokondweretsayi, chifukwa chakuti kugawana mawu ake iri mbali yofunika kwambiri mu kukula kwathu. Kuti chikhulupiriro chathu chikhalebe chabwino, chiyenera chionetsedwe. Monga anapezera Larry, mosayembekezera, kugawananso chikhulupiriro chathu kumatithandiza ife kuchita nacho mwathunthu, ndikutipangitsa ife kukula.

2. TIMAGAWANA ZA KHRISTU MU NJIRA YA M'MENE TIKHALIRA

Msungwana wina yemwe adakula mu banja la chizungu adapeza motere nthawi ina nati: "Ndidayang'ana makolo anga ndi zitsanzo zomwe anandionetsera zinandichotsa maganizo a umulungu; ndidalibenso chitsanzo cha wina ali yense wa thupi la umutnhu yemwe adandikonda ine." Anthu otizungulira amasowa wina wake woti awapatse chithunzi chenicheni cha Mulungu. Akufuna wina wake wa "khungu ngati lawo" yemwe angawaonetse makhalidwe abwino. Ulaliki wamphamvu umene tingapereke ndi m'mene tikhalira. Munthu asanafike posamala zomwe ukudziwa, ayenera kudziwa chisamaliro chomwe uli nacho. Petro akutiumiriza kuti:

"Ndipo mayendedwe anu mwa amitundu (osapemphera) akhale okoma,… akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino m'tsiku la kuyang'anira. Pakutinso Khristu amamva zowawa m'malo mwanu, nakusiyirani citsanzo kuti mukalondole mapazi ake." - 1 Petro 2:12, 21.

Chifukwa "Khristu anazunzidwa" chifukwa cha ife pa Karivari, ife tsono tiri ndi chitsanzo cha chikondi chakudzipereka nsembe chomwe tiri nacho pafupi. Chikondi chimenecho, chinaonekeranso mwa ife pakukonda anzathu, ndipo chimasandulika mphamvu yoposa yosendezera anthu wosakhulupirira m'manja a Khristu.

3. TIMAGAWANA ZA KHRITSU MNJIRA IMENE TIMAGANIZIRA

Pamene mdierekezi anamuyesa Yesu m'chipululu muja ndi nkhani yakufuna chakudya, kunyada ndi kungoganizira, Yesu adagonjetsa pogwiritsa ntchito mawu a m'bukhu lopatulika (Mateyu 4:4, 7, 10). Khristu anali atakonzekera ndi chifukwa anali atazama m'malembo oyera. Ndipo ndi m'menemo momwe nkhondoyo inagonjetsedwera-m'mitima yathu.

"Pakuti monga asinkha (munthu) m'kati mwake, ali wotere; ati kwa iwe, idya numwe; koma mtima wace suli pa iwe." - Miyambo 23:7.

Akhristu omwe akukula amaganiza zakumwamba. Amaganizira kwambiri pa zabwino zomwe ayenera kuchita kuti afikirepo pachimake.

"Kondwerani mwa Ambuye nthawi zonse;… komatu m'zonse ndi pemphero, ndipembedzero, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana cidziwitso conse udzasunge mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu. Chotsalira, abale, zinthu ziri zonse zoona, ziri zonse zolemekezeka, ziri zonse zolungama, ziri zonse zoyera, ziri zonse zokongola, ziri zonse zimveka zokoma; ngati kuli cokoma mtima cina, kapena citamando cina, zilingirireni izi. Zimenezonso mudaziphunzira, ndikuzilandira, ndikuzimva, ndi kuziona mwa Ine, zomwezo citani, ndipo Mulungu wamtendere adzakhala pamodzi ndi inu." - AFILIPI 4:4-9.

Chomwe tidyetsa mtima ndi maganizo athu, chimatipangitsa kusinthika. Kaya muzoipa, zimatulutsanso zoipa. Kaya ndi mawu a Mulungu, amatulutsanso moyo waumulungu.

4. TIMAGAWANA ZA KHRISTU M'MAONEKEDWE ATHU

Monga kazembe wa Khristu, mkhristu ayenera kukhala wodzichepetsa kwa anthu onse kupewa makhalidwe ndi machitidwe onse osayenera.

"Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu ainu nokha kuti ngatinso ena samvera mau, akakondwe opanda mau mwa oyera ndi kuopa kwanu. Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kubvala za golidi kapena kuvala cobvala, koma kukhala munthu wobisika mumtima, m'cobvala cosaola ca mzimu wofatsa ndi wacete, ndiwo wamtengo wace wapatali pamaso pa Mulungu. Pakuti koteronso kale…(iwo) akuyembekezera Mulungu, anazikometsera okha, namvera amuna ao a iwo okha." - 1 Petro 3:1-5.

Kukhala mumavalidwe oyenera ndi zozikometsera zoyenera zimaonetsera chikhritsu chenicheni. Cholinga ndi choti, ena akopekere kwa ife ngati akhristu osati chifukwa chazomwe tiwauza za mavalidwe amakono, koma chifukwa cha zomwe maonekedwe athu a m'moyo akulankhulira kwa iwo za Yesu.

5. TIMAGAWANA ZA KHRISTU M'MACHITIDWE ATHU

Katswili wa mbiri zakale wotchedwa Edward Gibbon akutiuza ife kuti pamene Galerius adagonjetsa asirikali achiperezi, thumba lodzala ndi ngale lidapezeka m'manja a msirikali wina wotenga zinthu wolanda.Mwamuna ameneyu adalisunga thumbali mosamala, natayamo ngalezo.

Anthu omwe amamatira ku zosangalatsa zomwe dziko lipereka-nakana za Yesu, ngale ya mtengo wapatali-ali pachoopsa choposa msirikali wakubayu. Simwayi wongotipeza kokha ayi komanso chipulumutso chamuyaya. Chotero Malembo oyera akutidzudzula kuti:

"Musakonde dziko lapansi, kapena za m'dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichiri mwa iye. Pakuti chiri chosatha cha m'dziko lapansi, chilakolako chathupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo (kunyada) sidzichokera kwa Atate, ku dziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita ndi chilakolako chache, koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhale ku nthawi yonse." - 1 Yohane 2:15-17.

Satana akugwira ntchito yoopsa kuti adzetse tchimo loononga kwambiri ndi loipitsitsa. Olengeza za zakumwa zoledzeletsa amaonetsera achinyamata abwino, okongola, olimbika pa ntchito ndi okondwa. Sitinaoneponso womvetsa chisoni m'maonekedwe awo ngati yemwe adzandima ndi zoledzeretsa pochoka mu sitolo yomwela mowawo atanyamula thumba la zinthu m'dzanja lache.

Tiyenera kusamala ndi magulu omwe amaipsa Malamulo athu achikhritsu (2 Akorinto 6:14). Khristu, inde, akufuna tikafikire onse osapembedza. Ubale weniweni ndiwo umafalitsa ndi kugawa chikhulupiriro pakati pa wina ndi mzake. Inu mungoonetsetsa kuti magulu anu sali akukubwezeretsani inu ku zoipa zomwe mumachita kale mu moyo wanu. Zomwe titenga mmoyo wathu, ngakhale zokhudza chisangalalo, ziri ndi mbali yaikulu mu moyo wathu wachikhristu. Tiyenera kusamala pa zomwe tidyetsa maganizo athu.

"Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira." - Masalimo 101:3.

Ngati maganizo athu adzala ndi zabwino, zoipa sizingatikokere ife pansi. Poganizira mwakuya mu zinthu zomwe tingabweretse kunyumba ndi m'mitima yathu sizingachepetse miyoyo yathu. Mkhristu ali ndi zambiri zomupangitsa kukhala wokondwa kuposa wina ali yense.

"Mudzandidziwitsa njira ya moyo: Pankhope panu pali chimwemwe chokwanira; m'dzanja lanu la manja muli zokondweretsa zonka muyaya." - Masalmo 16:11.

6. TIMAGAWANA ZA KHRISTU M'KUPEREKA KWATHU

Malemu M'busa H.M.S Richards, ali pafupi kubatiza wokhulupirira wina wake, adaona kuti munthuyo adali ndichikwama cha ndalama zamapepala okhaokha m'thumba mwake. Mbusayu adamufunsa iye ngati mwina adaiwala kuchisiya polowa m'madzimo. "Chikwama changa ndi ine tibatizidwira pamodzi," munthuyo adayankha. Adali atapeza mzimu weniweni wachikhristu.

"Kupatsa ena mowathandiza. Akhristu amakula pakupereka, ndi chifukwa chake "Yesu adati:Nchodalitsa kupereka koposa kulandira" (macitidwe 20:35). Zomwe tipereka zokulitsa ufumu wa Mulungu zimabweretsa cholowa chosatha.

"Musadzikundikire nokha cuma padziko lapansi pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba. Koma mudzikundikire nokha chuma m'mwamba… pakuti kumene kuli cuma cako, komwe udzakhala mtima wakonso." - Mateyu 6:19-21.

Pamene mupereka, kumbukirani: "Dziko lapansi ndi la Ambuye, ndi zonse zokhala m'menemo" (Masalmo 24:1), kuphatikizapo Siliva ndi golidi (Haggai 2:8). Tonse tiri a mwini wake Mulungu, chifukwa adatilenga ife ndikutipulumutsa kumachimo athu polipira dipo lamachimo athu ndi mwazi wake (Akorinto 6:19-20). Zonse zomwe tiri nazo ndizake za Yehova Mulungu chifukwa amatipatsa ife "mwayi wopezera chuma" (Deuteronomo 8:18).

Kodi Ambuye wathu wophedwa ndi woukitsidwa kwa akufayu akutiitana ife motani kuti tigawane naye popereka uthenga wabwinowo kwa ena?

"Kodi munthu adzalanda za Mulungu? Ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, takulandani zotani? Limodzi limodzi la magawo khumi ndi zopereka… mubwere nalo limodzi lonse lakhumi, kunyumba yosungiramo kuti m'nyumba mwanga mukhale cakudya; ndipo mundiyese nako tsono ati Yehova wamakamu ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndikukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira." - Malaki 3:8-10.

Limodzi lakhumi "chachikhumi" cha "zoonjezera" zathu (Deuteromo 14:22; 14:22; Genesis 28:22). Kwa mlimi kapena wa Malonda, choonjezera kapena phindu ndicho chomwe chibwera pamwamba pazomwe tataya pogula zinthu zathu zantchito kwa wolembedwa ntchito, chimakhala malipiro ake. Kupereka chachikhumi ndi lamulo lachikhalidwe chifukwa limakhudza khalidwe khalidwe. Polephera kupereka chachikhumi tima "mubera" Mulungu. Chachikhumi ndi cha Mulungu ndipo chiyenera kugwiritsidwa pa ntchito yokhayo yotumikira ntchito ya Khristu. (Akorinto 9:14), ndi kumalizitsa ntchito yake padziko lapansi kuti athe kubwera (Mateyu 24:24).

Pamene Yesu anadza kudzakhala nafe, anatipatsa chitsimikizo cha kupereka chachikhumi mu Chipangano Chatsopano (Mateyu 23:23). Kodi tiyenera kupereka zingati monga chopereka? Zopereka ziyenera kukhala monga mmene munthu woperekayo akuganizira. Munthu aliyense "apereke monga momwe mtima wake ufunitsa" (2 Akorinto 9:5-7). Simungapereke zoti muyeso wake wochulukitsa kwa Mulungu:

"Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu muyeso wabwino, wotsendereka, wokucumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'maanja mwanu." - Luka 6:38.

H.M.S. Richards adayerekezapo nthawi ina izi ndi "Munthu wolanda moyo wake wonse yemwe adakhala naye pa msonkhano ku Los Angeles, ndipo sindidzaiwala nthawi imeneyi yomwe ndinkayankhula naye payekha paseri pa nyumba yochitiramo msonkhano. Adatulutsa m,ndandanda wa ngongole m,thumba lake zomwe zimakwana $500, nandipatsa ine zonsezo, nati, (ichi ndicho chachikhumi chomwe ndiyenera kupereka poyambirira."

Munthuyu sadali bwino ayi, ndipo ntchito yake idali kulanda ndi kuyenda juga kwa zaka pafupifupi makumi atatu kapena makumi anayi, ndipo ine ndidati, "kodi iwe tsono udzakhala bwanji ndi moyo?" "Iye adandiyankha, "ndatsala ndi ndalama zokwana zisanu ndi modzi za chi Amerika basi, koma inayonso ndi ya Mulungu."
"ndipo ndidafunsanso, "ndiye uchita bwanji?"
"sindikudziwa." Adayankha, koma ndidziwa kuti ndiyenera kupereka chachikhumi kwa Mulungu, ndipo iye adzandisamalira."
"ndipo Mulungu adamusamaliradi kulapa kwa munthuyu kudali koona. Adavula zonse ndi kudzipereka ndipo adakhala wokondwa mu moyo wake wonse wa chikhristu. Ndipo Mulungu adampatsa iye zonse zosowa zake moyo wake wonse mpaka imfa." Mulungu sakulonjeza kuti Akhristu wokhulupirika onse adzakhala a chuma ayi, koma tiri ndi podalira pathu kuti Mlengi wathu adzatipatsa zosoweka mmoyo wathu.

Yesu anapereka zonse kwa ife. Tiyeni nafenso tipereke mitima yathu kwa iye tsopano lino. Tiyeni tigawire anzathu ena za Yesu kupyolera mu kakhalidwe, kaganizidwe, kaonekedwe, kachitidwe ndi kaperekedwe kathu. Bwanji osafufuza chimwemwechi chakugawana za Yesu ndi anzathu ndi ukulu m'chisomo chake chodabwitsachi?

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.