CHINSINSI CHA CHIMWEMWE M'chaka cha 1943, mabungwe oona zantchito ku Japan adalamula mazanamazana a anthu a ku Amerika ndi Ulaya kuti akhale "adani," nawasunga m,ndende zina ku China. Adapitirira miyezi yambiri yokhala okha, kukhumudwa, ndi kukhala mopanikizana ndi mantha. Makhalidwe osiyanasiyana apa adakhalira limodzi motsutsana, mitima yopsetsana idali pafupipafupi. Timikangano pa zinthu zazin'gono tinakula. Koma mwamuna m'modzi yemwe andendewa adamutcha "wosakaika, wokondedwa ndi wopatsidwa ulemu ndi wosoweka" - adali Erick Liddell, wachimishoni wochokera ku Scotland. Mayi wina wadama wa ku Russia m'ndendemo, nthawi ina adakumbukira kuti Liddel anali mwamuna yekhayo yemwe adachita chirichonse kwa iye popanda Malipiro. Pamene maiyu adafika m'ndendeyo, yekhayekha atabaidwa, adamuikira iye malo. Winanso wandende adakumbukira, "iye adali ndi njira yofatsa, ndiyosangalatsira motsitsa mitima ya omwe adali okwiya." Pamsonkhano wina wa mkwiyo wa andendewa, aliyense ankafuna kuti aliyense wa iwo kapena wina wake wa iwo achitepo kanthu pouza achinyamata an'gono ang'ono omwe amakhala osakhazikika nalowa mmavuto. Liddel adadza ndi yankho. Adakonza masewero, ntchito zamanja, ndi makalasi a maphunziro a ana, nayamba kukhala nawo mwapadera madzulo aliwonse. Liddel adatchuka nalemekezedwa pa masewero a Olympic a m'chaka cha 1924, komwe adalandira mendulo ya golidi pa mpikisano wothamanga wa mtunda wa mamitala 400. Koma mumpanipani umenewo, adaonetsa kukhala wopambana mu ulendo wake wa uzimu, nasiriridwa ndi andende ambiri a dziko lapansi. Kodi chidamupangitsa iye kukhala wapadera chonchi ndi chiyani? Mutha kupeza zinsinsi zake pa ola lachisanu ndi chimodzi m'mawa uliwonse. Iyi idali nthawi yomwe amadzuka ndikuyenda moyang'ana kudutsa andende anzake akugona, napita pa gome, nayatsa muuni waung'ono kuti aone m'kabukhu kake kakang'ono ndi Bukhu lopatulika. Eric Liddel adapeza chisomo ndi mphamvu tsiku ndi tsiku mu chuma cha mawu a Mulungu. 1. BUKHU LOTSOGOLERA MOYO WA CHIKRISTU Bukhu lopatulika lidalembedwa ngati lotsogolera kwa m'khristu liri lodzala ndi nthano zenizeni za anthu monga ife tomwe omwe adakumana ndi zobetchera ngatinso zomwe tikukumana nazo ife tsiku ndi tsiku. Podziwa anthu amenewa zisoni zawo ndi zisangalalo zawo, mavuto awo ndi mwayi wao-zitithandiza kukula ngati akhristu. Davide, wolemba Masalimo akuonetsera chithunzithunzi cha mmene moyo wathu watsiku ndi tsiku uyenera kukhalira wodalira pa Mawu a Mulungu pouyerekeza moyowo ndi kuwala kwa muuni: "Mau anu ndiwo nyali ya kumapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga." - Masalimo 119:105. Kuwala komwe timakupeza tsiku liri lonse kuchokera mu Baibulo kumapangitsa kuonetsera poyera makhalidwe omwe tiyenera kukhala nawo m'moyo mwathu ndi zofunikira kuti tikule muuzimu. Mwa zonse, Baibulo limationetsera ife ngati Yesu akuwalira pa moyowo. 2.
UBWENZI WAKUSINTHA Khristu akufuna kuti Bukhu lopatulika kuti likhale lenileni kwa inu monga kalata yolembera inu kuchokera kwa bwenzi lapamtima. "Sinditchanso inu akapolo; cifukwa kapolo sadziwa cimene mbuye wace acita; koma ndacha inu abwenzi; cifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziwitsani." - Yohane 15:15. Yesu amatifunira ife zabwino zokhazokha komanso amayembekeza zabwino zokhazokha komanso amayembekeza zabwino koposa mwa ife. Mawu ake amatibweretsa ife mundandanda wa Mulungu: anthu amene Iye awadalira ndikuwadzudzula paokha. "Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa Ine mukakhale nao mtendere. M'chibvuto, koma limbikani mtima." - Yohane 5:33. Ngati mufuna kukhala nawo mtendere umenewu ndiubale wotetezedwa umenewu ndi Khristu, tiyenera kuwerenga mukalata yomwe atitumizira ife. Umu ndi momwe Baibulo liliri kukambirana kochokera kumwamba. Musalole kuti makalata amenewa akhale osatsegulidwa. Uthenga wakusintha umene uli m'menemo ndi umene uli wofunika kwa ife. Apa pali umboni wodziwika bwino wa mphamvu ya Baibulo. "Ndidafuna thandizo ndipo ndidalipeza mwa Yesu. Chirichonse chofunika andipatsa, njala ya m'moyo mwanga anaithetsa; Baibulo kwa ine liri chivumbulutso cha Khristu. Ndikhulupirira Yesu chifukwa ndi Mpulumutsi woyera. Ndikhulupirira Baibulo chifukwa ndapeza kuti iloli ndi liu lochokera kwa Mulungu kudza ku moyo wanga." - Utumiki wa kuchiza, tsamba 461. 3. ZOTSOGORERA KUKHALA MOYO WA MAWU A BAIBULO NDI MALAMULO KHUMI Poonetsetsa Malamulo khumi a Mulungu kumathandiza kumvetsa chifukwa chomwe malamulowo ndi Baibulo ziri zofunika ndi zosatha pa kakhalidwe kathu. Malamulowa amagawidwa pawiri. Gawo loyamba limatanthauzira ubale wathu ndi Mulungu. Ndipo liri ndi malamulo anayi Gawo lachiwiri la Malamulo asanu ndi limodzi litanthauzira ubale pakati pa munthu ndi m'zake. Onsewa akupezeka pa Eksodo 20:3-17. Malamulo
awiri oyambirira akuonetsera ubale wathu ndi Mulungu ndi kumulambira. Malamulo khumi amaonetsera ubale wathu kwa Mulungu komanso kwa anthu ena. Iwo ali otitsogolera mu moyo wauzimu. 4.
ZOMWE YESU ADANENA PA ZA MALAMULO KHUMI Tsiku lina Yesu akuphunzitsa, mnyamata wachidwi kwambiri adamthamangira iye namufunsa, "mphunzitsi, kodi ndingachite chiyani chabwino kuti ndipeze moyo wosatha?" (Mateyu 19:16). Khristu anatha kuona kuti mnyamatayu chuma chakecho "ndikumvera malamulo kuwatsata" (vesi 17). Mnyamata anayesetsa kuti Yesu asaone bvuto lapandalama lomwe adali nalo, napitiliza kufunsa za lamulo lomwe liri loposa onse, kuti iye alitsate. Yesu adamuyalira angapo mwa Malamulo khumi (vesi 18,19). Pamapeto pake, mnyamata "mwini chumayu" adakhumudwa nachokapo (mavesi 20-22). Amatha kuwadziwa malamulowo koma samatha kudziwa mzimu womwe udali m'malamulowo kuti akafike posiya kudzikonda kwake m'moyo. Malamulo khumi amationetsera ife malire omwe afikiridwa ndi ubale weniweni ndi Mulungu komanso anthu. Yesu anaonetsera kuti kumvera kuti kuli njira yakuchisangalalo chenicheni. "Ngati musunga Malamulo anga, mudzakhala m'chikondi canga; monga Ine ndasunga Malamulo atate wanga, ndipo ndikhala m'chikondi cace. Izi ndalankhula ndi inu, kuti chimwemwe canga cikhale mwa inu, ndikuti chimwemwe canu cidzale." - Yohane 15:10, 11. 5. CHOTSOGOLERA KU MOYO WOKONDWA Bukhu
la Mlaliki ndi dongosolo loperekedwa lazofufuza zomwe Solomoni adafufuza
zokhuza kukondwa. Iye adalemba zakukondwa mu chuma cha dziko lapansi:
nyumba zokongola, minda yakupatsa zakucha zambiri, minda yokongola,
ndi m'minda yazipatso zobala zokoma. Anaonjezera antchito. Napeza kuti
iye ali nazo zonse zofunika pa moyo wamunthu. Komabe adapezeka wosakondwa,
ndipo analemba kuti: "Pamenepo ndinayang'ana zonse manja anga anazipanga, ndi ntchito zonse ndinasankha pozigwira, ndipo taona, zonse zinali zacabecabe ndi kungosautsa mtima, ndipo kunalibe phindu kunja kuno." - Mlaliki 2:11. Solomoni tsono adafufuzabe ndicholinga chopeza chisangalalo m'dziko lapansi. Analedzera, nakhala ndi akazi, naimba nyimbo. Pamapeto pake analemba: "Cabe zacabetu, ati Mlalikiyo; zonse ndi cabe." - Mlaliki 12:8. Solomoni adapeza kuti Ambuye ndi wabwino. Poyerekeza moyo wake woyamba wakumvera Mulungu ndi moyo wake wina wakufuna kukondwa mu zinthu za uchimo, adalembanso: "Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ace; pakuti coyenera anthu onse ndi ici." - Mlaliki 12:13. Solomoni
adaona ngati andapeze chifupi chake cha moyo wokondwa mkati mwa nyama
zakutchire. Kumapeto kwa moyo wake, iye adali munthu wotha kuvomera
kulakwa kwake ndipo adalemba kuti: 6. MALAMULO KHUMI NDI CHIPANGANO CHATSOPANO CHOSATHA M'chipangano
chatsopano, Yakobo akuchitira umboni kuti: Wolalikira wina wotchuka wakale wotchuka wachi Baptist, dzina lace Charles Spurgeon, adalalika," lamulo la Mulungu ndi loyera, lakumwamba, ndi langwiro palibe lamulo lalikuru, kapena laling'ono, koma ndilosayerekezeka mu Umulungu wake ndi umboni wake." John Wesley, m'modzi wa omwe adayambitsa mpingo wa Methodist, adalemba izi zokhudzana ndi chipiliro cha chilamulo: "m'chilamulo cha chikhalidwe munali malamulo khumi Iye (khristu) sanachititsepo mbali iri yonse ya lamulo liyenera kukhala chikhalire kwa anthu onse kumibadwo yonse." Billy Graham, wolalikira wotchuka kwambiri padziko lapansi, amawatenga Malamulo khumi kukhala akuya ndipo adalemba bukhu lonse lokhudzana ndi kufunika kwake ku moyo wa chikhristu. 7. MPHAMVU YA KUMVERA Bukhu lopatulika ndi malamulo khumi sizisintha, ndipo siziyerekezeredwa, ndiponso ziri zotsogolera mwangwiro ku moyo wachisangalalo. Komabe mitima iri yosakhazikika ndipo iri pachimkangano. Mayi wina adalongosola motere: "ndikhulupirira kuti malamulo khumi amamanga, ndiri ndi umboni kuti kusunga malamulowa kumabweretsa chisangalalo. Ndayesera ine ndi moyo wanga wonse kuwasunga koma ndikulephera. Ndayamba kukhulupirira kuti palibenso angathe. Khalidwe
la munthu liri loti ayesere kusunga malamulo a Mulungu. Koma yankho
la kuyesera konseko ndi kukhumudwa nthawi zonse mumtima wa munthu, "sindingathe
kumvera!" Chifukwa chiyani? "Cifukwa
cisamaliro ca thupi cidana ndi Mulungu; kutero." - Aroma 8:7. Kodi
cholinga cha malamulo khumi a Mulungu ndi chiyani? "Pakuti
ucimo udziwika ndi lamulo." - Aroma 3:20. Ntchito
yalamulo ndi kutitsogolera kukuzindikira kuti tiribe chiyembekezo chifukwa
tidataika muuchimo, ndipo tisowa mpulumutsi. "Momwemo cilamulo cidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Khristu, kuti tikayesedwe olungama ndi cikhulupiriro." - Agalatiya 3:24. Yesu ndi yankho! Nthawi ina yakebe timapezeka tiri osowa chiyembekezo pamapazi a Yesu, ndipo mwa chikhulupiriro titha kulandira chikhulukiro cha machimo athu ndi mpahmvu yakwa Iye kuti tikasunge ndi kumvera malamulo ake. 8. KUMVERA KWA CHIKONDI KU MALAMULO KHUMI Yesu
akutiuza ife kuti kumvera ndi zotsatira za chikondi: Munthu
yemwe akhumudwa pa malamulo khumiwa achimwa: "Yense wakucita cimo acitanso kusayeruzika: ndipo cimo ndilo kusayeruzika." - 1 Yohane 3:4. Koma
tithokoze Mulungu, tiri ndi Mpulumutsi yemwe adadza kudziko lapansi
natifera, naukitsidwa, ndipo ali ndi moyo ndi cholinga chimodzi. "Ndipo
mudziwa kuti Iyeyu anavomera kudzacotsa macimo, ndipo mwa Iye mulibe
cimo." - vesi 5. Mpulumutsi
wathu amakhululukira ndi kucotsa kucimwa kwathu (1 Yohane 1:9). Ndipo
akulonjeza kutipatsa ife moyo wachilikati weniweni: wodana ndi kudzikonda
nditchimo: "Cifukwa cikondi ca Mulungu cinatsanulidwa m'mitima mwathu mwa Mzimu woyera, amene wapatsidwa kwa ife." - Aroma 5:5. Tiribe ife chotiyenereza kuti tingasunge malamulo a Mulungu chikondi cha Mulungu "chotsanulidwira m'mitima yathu" ndicho chiyembekezo chathu chokha. 9. CHISOMO CHA MULUNGU NDI KUMVERA KU CHILAMULO Chipulumutso
ndi mphatso. Sitingathe kuchigwirira ntchito. Ife tingathe kungochilandira
kwa ulere mwachikhulupiriro. Timalungamitsidwa (kukhala woyenera pamaso
pa Mulungu) ngati mphatso kupyolera mu chikhulupiriro chokha basi chifukwa
cha chisomo cha Mulungu. "Pakuti
muli opulumutsidwa ndi cisomo cakucita mwa cikhulupiriro, ndipo ici
cosacokera kwa inu: ciri mphatso ya Mulungu." - Aefeso 2:8. Sitingathe kusunga malamulo mwantchito zathu poyesetsa sitingathenso kusunga malamulo kuti tikapulumuke. Koma tikadza kwa Yesu mwa chikhulupiriro ndi kudzipereka ndi kupulumutsidwa, chikondi chake chimadzala mu mitima yathu. Zotsatira za mphamvu ya umulungu iyi ya cisomo ndi kulandira, tifunika kumtsatira Iye ndi kumumvera Iye kupyolera mu mphamvu ya chikondi chake m'mitima yathu (Aroma 5:5). Paulo akutsimikizira kulephera kwa umunthu mukuyesetsa kwake ndikutionetsera kuti pansi palamulo ngati njira ya chipulumutso, koma "pansi pa cisomo" ndipo "Tidzacimwa kodi cifukwa sitiri alamulo, koma a cisomo? Msatero ayi" - Aroma 6:15. Chifukwa
chiyani? Pakuti mtima wodzazidwa ndi chikondi umabala moyo wacikondi
chakumvera! (Aroma 13:10). Kukonda Khristu ndiye kumvera Iye. "Iye wakukhala nao malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda Ine." - Yohane 14:21. Eric Liddel akuonetsera kuti, ngakhale munthawi yovuta, wokhulupirira amene wazikika mwa mphamvu ya Mulungu amakhala wokwanitsidwa, ndi womvera. Liddel akutionetseranso chisomo chakugonjetsa nthawi ya chisautso ndi mantha. Ubale wake wachikondi ndi Yesu Khristu udampatsa mphamvu za mzimu woyera, ndi kumupangitsa iye kukumana ndi "zofunika zachilungamo za chilamulo" (Aroma 8:1-4). Ubwenzi wachikondi ndi Mpulumutsi wopachikidwa woukitsidwa umabweretsa moyo wamtengo wapatali. Kodi inu mwapeza chinsinsi ichi mwa inu nokha? Chikondi cha Yesu pa inu chidampangitsa Iye kupereka moyo wake chifukwa cha machimo anu. Akudzipereka kukupatsani mphamvu mu ubale wanu ndi chikondi chake ndi ku "kukhwimitsani ndi zonse zabwino kuti mukachite chifuniro chake" (Ahebri 13:21). Kodi mukuyankha bwanji?
© 2003 The
Voice of Prophecy Radio Broadcast |
|