CHINSINSI CHA PEMPHERO LOYANKHIDWA

Wolemba wina wa ku Russia, dzina lake Anatoli Levitin, yemwenso ali katswiri pa mbiri, anakhala zaka zambiri ku Gulag wa ku Siberia kumene kukhulupirira mwa Mulungu kudazizira mpaka kutsikiratu. Koma adabwerako ali wodzala ndi uzimu." chozizwa cha zonse ndicho pemphero," Iye adalemba motero. "ndiyenera kutembenukira kwa Mulungu m'maganizo ndipo kamodzi komweko ndikumva mphamvu yachikakamizo yotsanulidwira mwa ine kuchokera kwina kwake, kudza mumtima mwanga, ndi mthupi langa lonse.

Kodi nanga ichi nchiyani? Nanga ine wokalamba, wotopa ndi moyo ndi wopanda pake ine, ndikakhala kuti ndi kupeza mphamvu yondikweza ine pamwamba padziko lapansi? Izi zichokera kunja kwa ine - ndipo palibe mphamvu m'dziko lapansi yomwe ingaletse izi.

Mu phunziro iri, tiona mmene pemphero limathandizira kumanga ubale wamphamvu ndi Mulungu ndi moyo wachikhristu wangwiro.

1. KULANKHULANA NDI MULUNGU

Kodi tingakhale bwanji ndi chitsimikizo kuti Mulungu amamva mapemphero athu?

"Pamenepo mudzandiitana Ine, ndipo mudzanka ndikupemphera kwa Ine, ndipo ndidzakumverani inu." - Yeremiya 29:12, 13.

Kodi ndi chitsimikizo chiti chomwe Yesu adapereka choti adzamva ndi kuyankha mapemphero athu?

"Ndipo Ine ndinena ndi inu, pemphani ndipo adzakupatsani, funani, ndipo mudzapeza, gogodani ndipo adzakutsegulirani." - Luka 11:9.

Pemphero ndi kukambirana kwa mbali ziwiri. Izi ndi zomwe Yesu alonjeza.

"Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine." - Cibvumbulutso 3:20.

Kodi ndizotheka bwanji kukhala ndi mgonero wazokambirana ndi khristu? Choyamba, pomuuza zonse zamumtima mwathu kupyolera mu pemphero. Chachiwiri, pomvera mosamalitsa pamene tipemphera, Mulungu atha kuyankhula nafe chindunji pamene tiwerenga mawu a Mulungu modzipereka, Mulungu adzayankhula nafe m'mawuwo. Pemphero litha kukhala njira yamoyo kwa Mkhristu.

"Kondwerani nthawi zonse PEMPHERANI KOSALEKA; m'zonse yamikani; pakuti ici ndi chifuniro ca Mulungu ca kwa inu, mwa Khristu Yesu." - Atesalonika 5:16-18.

Kodi "tingapemphere bwanji kosalekeza"? Kodi ife tikhale chigwadire nthawi zonse ndi kubwerezabwereza polankhula mapemphero athu ndi zofuna zathu? Sichoncho ayi. Koma tiyenera kukhala pafupifupi ndi Yesu kuti tikhale aufulu kuyankhula naye nthawi iriyonse paliponse.

"Kaya tiri pakati pa anthu ambiri mumsewu, pakati pa ntchito yamalonda, titha kupereka nkhawa zathu kwa Mulungu ndi kupempha chitsogozo chakumwamba… khomo lamtima wathu liyenera kukhala lotsegula nthawi zonse ndi kuitana Yesu kuti adze kudzakhala ngati mlendo wakumwamba mmoyo wathu-mapazi opita kwa khristu, tsamba 99.

"Pomlingirira Iye pandikonde; ndidzakondwera mwa Yehova." - Masalmo 104:34.

Popemphera sitiyenera ife kungofikira kuyala m'ndondomeko wazosowa zathu ayi.Dikirani, mvetserani pemphero lalifupi lakudzipereka litha kukuza ubale wanu ndi Mulungu.

"Yandikirani kwa Mulungu, ndipo adzayandikira kwa inu." - Yakobo 4:8.

Pamene tiyandikira kwa Yesu, ndipamenenso tinatha kumva kuti ali pakati pathu. Ndiye tiyeni tikhale pafupipafupi poti tingayankhule naye Yesu, ndipo tisadandaule ndi kuti mawu amene timuuza ndi oyenera kapena ayi. Timuuza chirichonse moona ndi mosasuka. Iye wadutsamo kale muchizunzo cha imfa yeniyeni ndi cholinga choti akakhale bwenzi lathu lenileni.

2. MMENE TINGAPEMPHERERE

Tikamapemphera, titha kusankha kutsatira ndondomeko ya pemphero la Ambuye, lomwe iye adaphunzitsa akuphunzira ake atamupempha kuti "Tiphunzitseni mmene tingapempherere."

"Atate wathu wakumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kucitidwe, monga kumwamba comweco pansipano. Mutipatse ife lero cakudya cathu calero. Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhulukira amangawa athu. ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo. pakuti wanu ndi ufumu ndi mphamvu ndi ulemerero wa nthawi zonse, Amen." - Mateyu 6:9-13.

Potsata ndondomeko ya pemphero yomwe Yesu anapereka mupemphero lake, tiyenera ife kudza kwa Mulungu monga Atate wathu. Tipemphe kuti kufuna kwake kokha ndiko kuchitike m'mitima yathu monga mmene zichitikiranso kumwamba.

Timamufuna Iye kuzosowa zathu zakuthupi, kuchikhulukiro, ndi mtima wokhululukira. Kumbukirani kuti, ife tithe kupewa tchimo, Mulungu ndiye angatithandize. Pemphero la Khristu likutha ndi chiyamiko kapena matamando.

Munthawi inanso, Yesu adawalangiza ophunzira ake kupemphera kwa Atate "m'dzina lake." (Yohane 16:23) kutanthauza kuti, azipemphera mogwirizana ndi ndondomeko ya Yesu. Ndichifukwa chake akhristu ayenera kutseka mapemphero awo ndi mawu awa: "m'dzina la Yesu, Amen" liwu loti "Amen" litanthauza kuti "zikhale chomwecho." muchiHeberi.

Ngakhale pemphero la Ambuye likutitsogolera pa zoyenera kupempha ndi m'mene liyenera kukhalira pempherolo, kulumikizana kwathu ndi Mulungu kumapambana ngati zopempha zathu zikuchokera pansi pamtima.
Titha kupempherera chirichonse. Komanso Mulungu akutiitanira ku kupempherera chikhululukiro cha macimo athu; (1 Yohane 1:9), kuchulukitsidwa kwa chikhulupiriro (Mariko 9:24), zofunika za m'moyo (Mateyu 6:11), Machiritso ku zowawa ndi matenda (Yakobo 5:15), ndi kuvumbitsidwa kwa mzimu woyera (Zekariya 10:1). Yesu akutitsimikizira ife kuti titha kutengera zosowa ndi nkhawa zathu kwa Iye: Palibe chomwe chiri chochepa kuchipempherera.

"Ndikutaya pa Iye nkhawa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu." - 1 Petro 5:7.

Mpulumutsi wathu anakondweretsedwa mu chiri chonse cha m'moyo wathu. Mtima wake umafunda pamene mtima wathu ufikira kwa Iye m'chikondi ndi chikhulupiriro.

3. PEMPHERO LAMTSERI

Ambiri aife tiri ndi zinthu zina zomwe sitingamasuke kuuza ngakhale abwenzi athu apamtima. Chotero Mulungu akutiitanira ife kuti timumasulire ife tokha izi mu pemphero lathu lamtseri: inu ndi iyeyo basi. Sikuti akufuna kupezapo nkhani yanuyo ayi. Mulungu wamphamvu zonsezi amadziwa zinsinsi zathu, zotiopsa zathu, malingaliro athu obisika, ndi zokwiririka zathu zomwe tazichita koposa m'mene ife eni ake tikudziwira. Koma tiyenera tiyambe tamasuka naye Iye wodziwa zonsezi ndi kumutsegulira mitima yathu, popeza Iye wotikondayo amatidziwa chiyambi mpaka mapeto athu. Kuchira kungayambike ndi kukhuza kwa Yesu ku mabala athu. Pamene tipemphera, Yesu, wansembe wathu wamkuru, ali pafupi kuti atithandize:

"Pakuti sitiri naye mkuru wa ansembe wosatha kumva cifundo ndi zofoka zathu; koma woyesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda ucimo. Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wacifumu wacisomo, kuti tilandire cifundo ndi kupeza cisomo ca kutithandiza nthawi yakusowa." - Ahebri 4:15, 16.

Kodi mumachita mantha, kupsinjidwa ndi kumva kuti muli wolakwa? Zonsezi zituleni pamaso pa Ambuye. Ndipo adzatipatsa chosowa chathu chiri chonse.

Kodi tiyenera ife kukhala ndi malo apadera ochitira mapemphero athu amtseri?

"Koma iwe popemphera, lowa m'chipinda cako, utseke citseko cako, nupemphere Atate wako ali mtseri... ndipo adzakubwezera iwe." - Mateyu 6:6.

Tithanso kupemphera moonjezera pamene tikuyenda pa msewu, pamene tikugwira ntchito, pamene tiri pachisangalalo ndi anzathu; Mkhristu aliyense apeze kanthawi tsiku lirilonse kopemphera payekha ndi kuwerenga Bukhu lopatulika. Lumikizanani ndi Mulungu tsiku ndi tsiku munthawi imene mukuona kuti muli tcheru ndipo mutha kumvana bwino naye.

4. PEMPHERO LA PAGULU

Kulumikizana ndi ena m'mapemphero kumabweretsa ubale wina wake wapadera ndi kuitanitsa mphamvu ya Mulungu mwa njiranso yapadera.

"Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndiri komweko pakati pao." - Mateyu 18:20.

China mwa zinthu zoposa chomwe tingathe kuchita ngati banja ndicho kukuza moyo wathu wakupempherera pamodzi. Onetsani ana anu kuti titha kupereka zosowa zathu mwachindunji kwa Iye. Iwo adzasangalatsidwa ndi Mulungu poona kuti mapemphero akuyankhidwa ndi Iye moonekeratu m'moyo. Pangani mapemphero a m'banja kukhala wosangalatsa ndi kukhala nthawi yakugawana momasuka.

5. ZINSINSI ZISANU NDI ZIWIRI ZAKUYANKHIDWA KWA PEMPHERO

Pamene Mose adapemphera, panyanja yofiira, madzi anagawanika. Pamene Eliya adapemphera, moto unatsika kuchokera kumwamba. Pamene Danieli anapemphera, mngelo wa Mulungu adatseka pakamwa pa Mikango yolusa. Bukhu lopatulika likutionetsera ife ndi zitsanzo zosangalatsa zambiri za kuyankhidwa kwa mapemphero. Ndipo likuchitira umboni kuti pemphero ndi njira yotsitsira mphamvu za Mulungu zazikulu kuti zidze pansi pano. Yesu akulonjeza kuti:
"Ngati mudzipempha kanthu m'dzina langa, ndidzacita." - Yohane 14:14.

Komabe mapemphero ena amaoneka ngati sakuyankhidwa. Nanga ndi chifukwa chiyani? Pano pali malamulo otsogolera asanu ndi anayi omwe amathandiza kuti mapemphero anu akhale a mphamvu.

(1) Khalani chifupi ndi Khristu nthawi zonse.
"Ngati mukhala mwa Ine, ndi mawu anga akhala mwa inu, pemphani cimene ciri conse mucifuna ndipo cidzacitika kwa inu." - Yohane 15:7.

Pamene tiri pa ubale ndi Mulungu kukhala chinthu choyambirira ndi kukhala ndi Iye nthawi zonse, tidzakhala omvetsera ndi oyang'ana kwa Iye pa mayankho a mapemphero athu; kupanda apo, titha kukhala osazindikiridwa.

(2) Khalani okhulupirira mwa Mulungu nthawi zonse.
"Ndipo zinthu ziri zonse mukazifunsa m'kupemphera ndi kukhulupirira, mudzalandira." - Mateyu 21:22.

Kukhulupirira, kapena kukhala ndi chikhulupiriro, zitanthauza kuti ife tikuyang'ana kwa Atate wathu wakumwamba yekha kutipatsa zosowa zathu. Ngati mukuvutika ndi kusowa chikhulupiriro, kumbukirani kuti Mpulumutsi wathu anachita zozizwa kwa mwamuna yemwe adalilira kwa Iye atasowa
"Pomwepo atate wakumwamba amapfuula, nanena, ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga."- Mariko 9:24.
Inu yesetsani kuchita ndi chikhulupiriro chimene muli nacho; musadandaule ndi chikhulupiriro chomwe inu mulibe.

(3) Mudzipereke kwathunthu ku cifuniro cha Mulungu.
"Ndipo uku ndi kulimbika mtima kumene tiri nako kwa Iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa cifuniro cace, atimvera." - 1 Yohane 5:14.
Kumbukirani kuti Mulungu akufuna kutiphunzitsa ife, ndiponso kutipatsa ife zinthu, kupyolera mu pemphero. Choncho, nthawi zina Iye amayankha kuti, "AYI,"nthawi zina amatilozera kunjira ina yosiyana ndi kufuna kwathu. Pemphero ndi njira yokhayo yopezera zambiri polumikizana ndi Mulungu ndi chifuniro chake. Tiyenera kusamalitsa kumayankho a Mulungu ndi kuphunzirirapo. Kukhala oyang'anirapo zofuna zathu zenizeni ndi zomwe zimatsatira pa izo zidzakhala zotithandiza.

Mzimu woyera adzakuthandizani kukhala pa mzere weniweni. "Mzimu amatinenerera oyera ake motsata chifukwa cha Mulungu" (Aroma 8:27). Kumbukirani kuti kufuna kwathu kumatsutsana nthawi zambiri ndi kufuna kwa Mulungu, tikadakhala kuti timaona m'mene Iye, Mulungu amaonera.

(4) Dikirani modekha mtima.
"Kuyembekeza ndayembekeza Yehova; ndipo anandilola, namva kupfuula kwanga." - Masalmo 40:1.
Mfundo yeniyeni apa ndi yotilozera ife kuti tiyang'anitsitse pamulungu, ndi mayankho ake. Ndipo tisamupemphe Iye kuti atithandize mphindi imodzi yokha ndi kumuleka kwinako kuti tichite zofuna zathu m'moyo. Dikirani modekha pa Ambuye, tikufunika ife kukhala ndi khalidwe lotere.

(5) Osamamatira pa tchimo lina liri lonse.
"Ndikadasekera zopanda pace m'mtima mwanga, Ambuye sakadamvera." - Masalmo 66:18.
Tchimo lodziwika limadula mphamvu ya Mulungu m'moyo mwathu; limatilekanitsa ife ndi Mulungu wathu (Yesaya 59:1-2). Simungakangamire pa tchimo ndi dzanja limodzi ndi kufuna mphamvu ya Mulungu kuti ithandize ndi dzanja linalo kulapa moona mtima ndi kusiya zochimwazo kumathetsa mavuto athu. Ngati sitiri olola kumpanga Mulungu kuti atimasule ife ku zoipa ndi maganizo oipa, mau oipa, zochita zoipa; mapemphero athu sadzagwira ntchito.
"Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukazimwaze pocita zikhumbitso zanu." - Yohane 4:3.
Mulungu sadzayankha kuti "INDE) Kwa pemphero lodzikonda
Tcherani khutu lanu lotsegukira kwa Mulungu ndi lamulo lake, chifuniro chake, ndipo Iyenso adzatsegula khutu lace kumvetsera madandaulo anu.
"Wopewetsa khutu lace kuti asamve cilamulo ngakhale pemphero lace linyansa." - Miyambo 28:9.

(6) Imvani zomwe Mulungu akuzifuna.
Mulungu amayankha kwa anthu omwe apempha, momuitana Iye kuti akhale m'moyo mwawo ndi mphamvu yake.
"Odala ali akumva njala ndi ludzu lacilungamo, cifukwa adzakhuta." - Mateyu 5:6.

(7) Musatope ndi kupemphera (pempherani mosalekeza).
Yesu adalongosola za kufunika kwa kupemphera kosalekeza, potiuza nthano ya mayi wamasiye yemwe sadatope ndikupitabe ndi dandaulo lake kwa woweruza. Pa mapeto pake woweruzayu ananena chifukwa chotopetsedwa. "Popeza mayi wamasiyeyu akundivutitsa, ndiyesetsa kuti ndipereke chiweruzo choyenera chachilungamo." Ndipo Yesu adamaliza ndi kuti: "kodi Mulungu sadzachita mwa chilungamo kwa osankhidwa ake, omwe alilira kwa Iye tsiku ndi tsiku, masana ndi usiku? Kodi adzakhala akuwakhumudwitsa? (Luka 18:5-7).

Kambiranani ndi Mulungu zofuna, ziyang'aniro ndi maloto anu pemphani madalitso apadera, chithandizo munthawi yakusowa. Mufuneni, mumvereni nthawi zonse mpaka mutaphunzira china chake ku mayankho ake a Mulungu.

6. ANGELO AMATUMIKIRA KUZOSOWA ZA IWO AKUPEMPHERA

Wolemba Masalmo adasangalala kuti kupyolera mu utumiki wa angelo a Ambuye, mapemphero ake adayankhidwa.

"Ndinafuna Yehova ndipo anavomera, nandilanditsa m'mantha anga onse... Mngelo wa Yehova azinga kuwacinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo." - Masalmo 34:4-7.

Pamene tipemphera, Mulungu amatumiza angelo ake kudzayankha mapempherowo (Ahebri 1:4). Mkristu aliyense ali ndi mngelo wake womutsogolera:

"Yang'anirani kuti musanyoze mmodzi wa ang'ono awa; pakuti ndinena kwa inu, kuti angelo ao apenye cipenyere nkhope ya Atate wanga wa kumwamba." - Mateyu 18:10.

Chifukwa cha mapemphero athu:
"Ambuye ali pafupi. Musadere nkhawa konse; komatu m'zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi ciyamiko zopempha zanu zidziwika kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana cidziwitso conse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa khristu Yesu." - Afilipi 4:5-7.

7. UMOYO WA KHRISTU

Bukhu lopatulika limalongosola moyo weniweni wa Mkhristu, monga akunena pa Aefeso 4:22-24, wokhulupirira ayenera "kusiya" moyo wake wakale womwe udadza cifukwa ca "zokhumba zachinyengo," ndi "kuvala" moyo watsopano umene "ulengedwa kufanana ndi Mulungu." Mu malembo awa ndi mu phunziro lathu lotsogolera lija lachisanu ndi chimodzi, tidapeza kuti pakubadwanso mwatsopano ife "timalengedwanso mwatsopano" kukhala munthu wosinthika mwa khristu.

Phunziro ili ndi maphunziro asanu ndi limodzi otsatirawa, akuonetsa moyo wachikristu. Ndipo akutionetsera chinsinsi cha moyo wa chikhristu wokondwa. Zikuthandizaninso inu kumanga ubale wamphamvu ndi khristu, mmene udzathera mu moyo weniweni wapadera wa chikhristu. Chotero yang'anitsitsani pa Yesu lero ndipo mudzatha kukhala mbali imodzi ya chigonjetso chomaliza chachikondwerero pamene mtendere wa khristu udzalamulira popanda woutsutsa.

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.