KUCHOKERA KU KUTSUTSIKA NDI CHIMO KUFIKIRA KU WOYERA WOKHULULUKIDWA

Sadapeza malo pomwe panagwira zala. Palibenso chida chomwe chidapezeka. Wakuphanso sanaoneke akusowa mu ofesi ya dotoloyo. Palibenso adamva kulira kwa mfuti. Koma kunapezeka kuti dotolo ali gone pa mpando wake wa muofesi. Zipolopolo za mfuti zisanu zikuonekera kuti zaboola malaya ake ndikulowa m'thupi.

Zinaoneka ngati chinali chiwembu changwiro. Apolisi sanathe kupeza umboni uliwonse pachiyambi koma adapeza waya wina wake wan'gono atamangiliridwa ku nsonga ya choikamo pensulo pa tebulo lantchito la dotoloyo. Wayayo adakafikira ku wailesi yojambula mau yomwe inali muchosungira zinthu chapatebuloyo. Anazindikira kuti, choikamo pensulocho, chinali chitaphimbira chija choyankhulirapo mawu, (microphone) chomwe dotolo ankagwiritsa pojambula zokambirana ndi odwala ake amene anayenera kuwapatsa malangizo.

Ofufuza adaibweza tepi yojambulidwayo, ndipo anadabwa, pamene anamvetsera tepiyo kupeza kuti imakamba zokhudzana ndi chiwembu chomwe chidapha dotoloyo. Mwamuna wotchedwa Anthony adalowa mu ofesiyo nayamba mkangano waukuru ndi dotoloyo. Kenaka kunamveka kulira kwa mfuti ndipo tepiyo inathera ndi kulira kosautsika ndi ululu kwa dotoloyo, akufa kugwera pa nsalu ya muofesiyo.

Choopsa chirichonse chinajambulika. Wakuphayo amaganiza kuti chiwembucho sichidzaululikanso. Anayesetsa kuchita mosamala kuti pasapezeke umboni uliwonse. Koma tepiyo idapereka umboni wonse.

Muchotsogolera cha phunziro ili, tiphunzira za chiweruzo chomaliza cha Mulungu pamene anthu adzaweruzidwa "malinga ndi zomwe iwo adachita, zomwe zalembedwa m'mabukhu" (cibvumbulutso 20:12) kwa; iwo amene sanamulandire khristu ngati Mpulumutsi wawo; kwaiwo kudzakhala nkhani yoipa. Koma chiweruzochi chidzakhala nkhani yabwino kwa iwo amene anapeza kupuma mwa khristu.

1. M'MENE MUNGAFIKIRE KUCHIWERUZO MOPANDA MANTHA

Kodi adzaweruza dziko lapansi ndani?

"Pakuti Atate saweruza munthu aliyense, koma anapereka kuweruza konse kwa Mwana." - Yohane 5:22.

Kodi nanga mtanda unamkonzetsera bwanji Yesu Khristu kuti akhale woweruza wathu?

"Amene Mulungu anaunika poyera (Yesu) akhale cotetezera mwa cikhulupiriro cam'mwazi wace, kuti aonetsere cilungamo cace... kuti Iye akhale WOLUNGAMA, NDI WAKUMUYESA WOLUNGAMA Iye amene akhulupirira Yesu," - Aroma 3:25, 26.

Imfa ya khristu m'malo mwa ife inapangitsa Iye kukhala yekha woweruza komanso wotilungamitsa yemwe angathe kutikhululukira ife tikalapa machimo athu. Pamene dziko lapansili likuonerera zochitika zake ndikhala ndi mafunso ngati awa, "kodi woweruza angathenso bwanji kumupanga wolakwayo kukhala wopanda mlandu?" Khristu atha kuyankha poonetsa zipsera za mabala m'manja mwake,. Analandira dipo lakuyeretsera machimo athu m'thupi lake mwini.

Mabukhu a kumwamba amasungira zochitika zonse za m'moyo wamunthu aliyense, ndipo zochitika zosungidwazo zimagwiritsidwa ntchito pa chiweruziro (Cibvumbulutso 20:12).

Iyi ndi nkhani yowawa kwa iwo omwe amaganiza kuti machimo awo amtseri ndi ziwembu zawo sizidzawapezanso. Koma pali nkhani yabwino yokoma kwa iwo omwe adadzichepetsa kumlandira khristu ngati wowaimirira pa mlandu wawo kumwamba: "mwazi wa Yesu... utiyeretsa ife kumachimo athu" (1 Yohane 1:7).

Kodi Yesu amausinthanitsa moyo wathu wa uchimo ndi chiyani?

"Ameneyo sanadziwa ucimo anamyesera ucimo m'malo mwathu kuti ife tikhale cilungamo ca Mulungu mwa Iye." - 2 Akorinto 5:21.

Moyo wathu wa uchimo umasinthanitsidwa ndi moyo wangwiro wachilungamo wa khristu chifukwa chakufa kwa Yesu wosachimwa, Mulungu atha kutikhulukira ife ndikutitenga monga ngati sitidachimweko cikhalire. Kodi chamuyenera Yesu kukhala wotiimira ndi wotiweruza pa mlandu wathu ndi chiyani?

2. YESU ANABWERA PANTHAWI YAKE

Pa ubatizo wake, Yesu anazunzidwa ndi mzimu woyera.

"Ndipo Yesu pamene anabatizidwa , pomwepo anaturuka m'madzi: ndipo onani, miyamba inatsegukira Iye, ndipo anapenya mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye: ndipo onani, mau akucokera kumiyamba akuti "Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera." - Mateyu 3:16, 17.

Potsatira bwino kudzodzedwa kwa Yesu ndi Mzimu woyera pa ubatizo wake, ophunzira ake analengeza:

"Tapeza ife Mesaya" (ndiko kusandulika Kristu)."- Yohane 1:41.

Ophunzirawa ankadziwa liwu lachiHebri loti "Mesiya" ndi lina lachiherene loti "khristu" onsewa atanthauza "amene ali wodzozedwa."

Wophunzira wina wa Yesu dzina lake Luka, analemba zatsiku lomwe Yesu anadzozedwa ngati Mesiya kuti chinali chaka chachisanu kulamulira kwa Kaisara. Tiberiyu (Luka 3:1) kwa ife nthawi imeneyo idali chaka cha A.D. 27.

Kupyolera zaka mazana asanu Yesu asanabwere, m'neneri Danieli analosera kuti Yesu adzadzodzedwa monga Mesiya m'chaka cha A.D.27.
"kuyambira kuturuka lamulo lakukonzanso, ndi kumanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo... kudzakhala masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri makwalala ndi chemba zidzamangidwanso." - Daniel 9:25.

Masabata asanu ndi awiri ndi masabata makumi asanu ndi chimodzi mphambu ziwiri, zonsezi pamodzi zitipatsa masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu ndi zinayi, kapena masiku mazana anayi makumi asanu ndi atatu ndi mphambu zitatu (483 days).

Muzizindikiro za m'baibulo ndi ulosi wake, tsiku limodzi limaimira chaka chimodzi (Ezekieli 4:6, Numeri 14:34), ndiyeno masiku tachulawo akuimira zaka mazana anayi makumi asanu ndi atatu mphambu zitatu (483 years).

Danieli adalosera kuti ulamuliro udzaperekedwa kubwezera ndi kumanganso Yerusalemu, ndipo patapita zaka zimene tatchulazi chiikire ulamuliro Mesiya adzaonekera.

Kodi Yesu adaonekera ngati Mesiya nthawi yoikikayi? Aritasasta, mfumu adapereka lamulo kumanganso Yerusalemu m'chaka cha 457 B.C. (Ezara 7:7-26). Ndipo zaka izi mazana anayi makumi asanu ndi atatu mphambu zitatu zinathera m'chaka cha A.D. 27 (457 B.C + A.D. 27 = 484). Lamuloli lidapitirirabe m'chaka cha 457 ndipo khristu anadzodzedwa m'nthawiyi ya chaka cha A.D.27, kupangitsa zakazi kukhala mbali imodzi kuti nthawi yake yeniyeni ikakhale zaka mazana anayi makumi asanu ndi atatu mphambu zitatu.)

Munthawi yake yoikikayo, m'chaka cha A.D. 27, Yesu anaonekera ndi uthenga: "nthawi yafika" (Marico 1:15). Kukwaniritsidwa kwenikweni kwa ulosi wa m'baibulo ndi kokwanira kutsimikizira kuti Yesu waku nazareti ndiyedi Mesiya, Mulungu muthupi la umunthu.

Kodi panayenera kutenga nthawi yaitali bwanji kuti Yesu akwaniritse lonjezo?

"Ndipo adzapangana cipangano colimba (lonjezo) ndi ambiri sabata limodzi." - Danieli 9:27, mbali yoyambirira.

Tikatengera chiwerengero cha tsiku kuimira chaka, "sabata" iyi ikhala zaka zisanu ndi ziwiri. Ndiye kwazaka zisanu ndi ziwiri-kuyambira m'chaka cha A.D. 27 kufikira A.D. 34. Yesu akada "kwaniritsa chipangano, "kapena lonjezo lomwe adapanga kwa Adamu ndi Hava atangochimwa. Mulungu adapanga pangano, lonjezano, kuti adayenera kupulumutsa mtundu wa anthu kuchokera ku tchimo kupyolera mu imfa ya wina wake yemwe akadamtuma kudzafera machimo athu (Genesis 3:15).

Chinayenera kuchitika n'chiyani mkatikati mwa sabata ya makumi asanu ndi awiriyi?

"Ndi pakati pa sabata adzaleketsa nsembe yophera ndi nsembe ya ufa." - Daniel 9:27.

Yesu anapachikidwa m'chaka cha A.D. 31 "mkatikati mwa sabatayi" pa nthawi yomwe khristu anafa, Mulungu "anang'amba nsaru ya m'kachisi... pakati kuyambira kumwamba mpaka pansi (Mateyu) 27:51). Nsembe yopsereza yoperekedwa kuti iphedwe (yoimira Yesu "Mwana wa nkhosa wa Mulungu" idathawa m'manja mwa wansembe. Ichi chinali chizindikiro kuti Mulungu safunanso munthu kuti adzipereka nsembe ya nyama. Uku kukwaniritsa ulosi wakuti Yesu "anathetsa" kufunika kumaperekabe nsembe yodzera muimfa ya Yesu, anthu akupezeramo mwayi wofika kwa Mulungu mowaperekanso nsembe kupyolera mwa akuru ansembe, koma kupyolera mwa Mesiya, mwana wa nkhosa wa Mulungu.

3. CHITSIMIKIZO KUTI MACHIMO AKHULULUKIDWA

Monga mwa ulosi wa Danieli, ndi chifukwa chiyani Yesu anafa?

"Wokozedwayo adzalikhidwa, nadzakhala wopanda kanthu."
- Danieli 9:26.

Paimfa yake pamtanda, Yesu "analekanitsa." Anafa, "osati kudzifera yekha" osatinso kulipira dipo la tchimo lake, koma kulipira dipo la machimo a dziko lonse lapansi kodi tingadziwe bwanji kuti Mulungu wakhulukira machimo athu?

"Ndipo cilungamo ca Mulungu cimene cicokera mwa cikhulupiriro capa Yesu Khristu kwa onse amene akhulupirira... pakuti ONSE ANACHIMWA..., ndipo ayesedwa olungama kwaulere, ndi cisomo cace, mwa ciombolo ca mwa khristu Yesu... mwa cikhulupiriro ca mwazi wace." - Aroma 3:22-25.

Mfundo zenizeni mu mavesiwa ndi awa: Ife "tonse tinachimwa," koma cifukwa cha chisomo cha Mulungu, tonse "tidalungamitsidwa" amene ali "ndi chikhulupiriro" mu mphamvu yakuyeretsa ya "Mwazi" wa khristu. Pamene tilungamitsidwa, Mulungu amaticha ife wopanda tchimo, nafafaniza mphulupulu zathu zonse zakale. Ndipo amatitcha ife wolungama, "chilungamo cha kwa Mulungu chichokera mu chikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu."

Tonse amene tatunduzidwa pofuna kuyesetsa kukhala wolungama mwatokha, titha kupeza mpumulo weniweni mu chisomo chakutilandira cha khristu. Akutilonjeza kuti, "idzani kwa Ine, inu nonse akulema ndi akuthodwa, ndipo ndidzakupumulitsani" (Mateyu 11:28). Tonse amene talemedwa ndi zipsera za ukali wathu ndikumva kuperewera kwathu ndi manyazi, titha kupeza mtendere ndi umphumbu mwa khristu.

4. NTHAWI YA CHIWERUZIRO KUFUNA KUYAMBIKA

Mu mutu wakhumi ndi chisanu ndi chitatu cha Danieli muli m'ngelo yemwe akuonetsa Daniel zinthu zazikuru zodzachitika kutsogolo. Daniel adaona:

(1) Nkhosa yamphongo, (2) mbuzi yamphongo ndi (3) nyanga imodzi yomwe mbuzi yamphongoyi idali nayo " munatuluka nyanga ina yomwe inayamba ngati yaing'ono, naikula mu mphamvu" (Daniel 8:1-12, 20:26).

Kodi mbali yachinayi ya ulosiwu ndi yotani?

"Masomphenya a nsembe yopsereza yachikhalire, ndi cholakwa chakupulumutsa ca kupereka malo opatulika ndi khamulo ziponderezedwe, adzakhala mpaka liti? Nati kwa ine, mpaka masiku zikwi ziwiri mphambu mazana atatu usana ndi usiku; pamenepo malo opatulika adzayesedwa olungama." - Daniel 8:13, 14.

Daniel adakomoka m'ngelo asadayambe kulongosola za mbali ya masiku zikwi ziwiri mphambu mazana atatu ya ulosi, ndipo mutu wachisanu ndi chitatu ukutha usanamasulire ulosiwu. Koma nthawi inanso mngeloyu anabweranso nanena:

"Ndaturuka tsopano ine kukuzindikiritsa mwa luntha. Pakuyamba iwe mapembedzero ako, linaturuka lamulo, ndipo ndadza ine kukufotokozera. Masabata makumi asanu ndi awiri olamulidwira anthu a mtundu wako ndi mudzi wako wopatulika, kumariza colakwa, ndi kutetezera mphulupulu." - Daniel 9:22-24.

Masiku zikwi ziwiri mphambu mazana atatu, indedi ndi zaka zimenezo, tsiku limodzi liimira chaka chimodzi (Ezekieli 4:6). Masabata makumi asanu ndi awiri, kapena masiku mazana anayi mphambu makumi asanu ndi anayi, ziri mbali imodzi yaitali kwambiri yoyambirira ya Zaka zikwi ziwiri mphambu mazana atatu. Nthawi zonsezi zinayamba m'chaka cha 457BC pamene Perezi adapereka lamulo "lobwezera ndi kumanganso Yerusalemu." Kuchotsera zaka zobwezera ndi kumanganso Yerusalemu." Kuchotsera zaka mazana anayi mphambu makumi asanu ndi anayi ku zaka izi zikwi ziwiri mphambu mazana atatu, titsala ndi chikwi chimodzi, mphambu mazana asanu ndi zitatu ndikhumi kuphatikizira zaka zotsalazi ku chaka cha A.D. 34, pamene zaka mazana anayi mphambu makuni asanu ndi anayi zidathera, zikutipatsa chaka cha A.D. 1844.

5. KUYERETSEDWA KWA KACHISI WA KUMWAMBA- CHIWERUZIRO

Mngelo adamuuza Daniel kuti m'chaka cha 1844, kumapeto kwa zaka zikwi
ziwiri mphambu makumi atatu, "kachisi adzayeretsedwa" (Daniel 8:14). Koma nanga izi zikutanthauza chiyani? Kuyambira m'chaka cha A.D. 70 pamene Aroma adaononga kachisi wa Yerusalemu, anthu a Mulungu adakhala opanda kachisi pa dziko lapansi. Kachisi woti ayeretsedwe, kuyambira mu 1844, anayenera kukhala wakumwamba yemwe amafanana ndi yemwe adali pansi pano.

Nanga, zitanthauzanji kuyeretsa kachisi wakumwamba? Israeli wakale ankalitcha tsiku loyeretsa kachisi wa pansi pano kuti yomu kipuru, tsiku lachitetezero. Linalidi tsiku la chiweruziro.

Monga mmene tidaonera mu phunziro lakhumi ndi chiwiri lija, ntchito yakhristu kwa ife mu kachisi yagawidwa pawiri:
(1) Nsembe yatsiku ndi tsiku imaonetsera utumiki wa wansembe muchipinda choyamba cha kachisiyo, malo opatulika.

(2) Nsembe ya pachaka imaonetsera ntchito yapamwamba ya utumiki wa unsembe m'chipinda chachiwiri, malo opatulikitsa (Revitiko 16).

Mukachisi wa dziko lapansi, pamene anthu ankalapa machimo awo tsiku ndi tsiku, mwazi wa nyama yophedwa umawazidwa pambali pamapeto a guwa lansembe, ndipo umasamutsidwa ku malo opatulika (Levitiko 4 ndi 6). Kusonyeza kuti, mzoimirira, tipeza kuti tsiku ndi tsiku, machimo amaperekedwa ku kachisi kudasiidwa kumeneko anthu okalapa.

Ndipo chaka chiri chonse, pa tsiku lachitetezero, kachisi amayeretsedwa kumachimo onse olapidwa chaka chonse (Levitiko 16). Kuti kuyeretsa uku kutheke, mkulu wansembe amapereka nsembe yapadera ya mbuzi yopanda banga yopatulidwa. Ndipo mwazi wa mbuziyo amautenga kukalowa nawo ku chipinda chopatulikitsa nawaza mwaziwu pa chofundira cha chitetezero kuchipindako kusonyeza kuti mwazi wa Yesu, mombolo alikudzayo, adzalipira dipo la zochimwa zonse. Wamkuru wansembeyu woyerekezera amakhala ngati wachotsa machimo onse omwe anthu adalapa mkachisimo kuwatula pa mutu pa mbuzi ina, yomwe imasiyidwa kupita kuchipululu kuti ikafe (Levitiko 16:20:22).

Mwambo uwu wachitetezero wa tsiku lapachaka umayeretsa kachisi ku tchimo. Anthu ankalitenga tsikuli ngati lachiweruziro, chifukwa omwe adakana kulapa machimo awo amatchedwa wosayera ndipo "amachotsedwa m'gulu la anthu a Mulungu" (23:29).

Chomwe anayerekeza wansembe dziko lonse lapansi (cibvumbulutso 14:6-7). Mtsogolomu, m'maphunziro athu omwewa tidzaphunzira za uthenga umenewu.

6. KUDZAPEZANA NDI ZOMWE MUNACHITA M'MOYO PA CHIWERUZIRO

Kuyambira mu 1844, Khristu, monga woweruza, wakhala akufufuza mu 1844, khristu, monga woweruza, wakhala akufufuza mabukhu a munthu aliyense wokhala pa dziko lapansi kuti otsimikizira za iwo amene ali woyera kukakhala opulumutsidwa pamene Yesu adzabwera. Monga woweruza wathu, Yesu "akufufuta" machimo onse a anthu oyera kuchokera mu mabuku awo a moyo kumwamba (Macitidwe 3:19).

Dzina lanu likadzafika pachiweruziro, zidzakhala zosavuta kukumana ndi ntchito zathu zomwe zinalembedwa-koma pokhapokha ngati mwamulandira Yesu khristu monga wolowa m'malo wanu, ndipo pamene chiweruziro cha olungama chatha, Yesu adzabwerera ku dziko lapansi kudzapereka mphotho kwa iwo (Cibvumbulutso 22:12,14).

Kodi inu mwakonzekera kubwera kwa Yesu? Kapena pali china chake chomwe mwakhala mukumubisira Iye? Kodi muli pa ubale woongoka ndi woona womasuka ndi yemwe walonjeza kuti:

"Ngati tibvomereza macimo athu, ali wokhulupirika ndi wolungama Iye, kuti atikhululukire machimo athu, ndikutisambitsa kuticotsera cosalungama ciri conse." - 1 Yohane 1:9.

Kulapa kutanthauza mosavuta kuti tavomera kukumana ndi machimo athu, ndi kuvomereza chikhululukiro cha Mulungu komanso kuzindikira kufunika kwa mphamvu yake ndi chisomo chake kwa ife.

Mfumu ina yotchedwa Fredrick William woyamba adamvetsera madandaulo a kufuna chikhululukiro kundende ina yomwe adakachezako ya ku Potsdam. Am'ndende onse adalumbira nati oweruza okondera, mboni zonama, ndi oyimirira milandu yawo osadziwa ntchito, adachititsa kuti iwowa apezeke mundende chomwechi. Kuchokera chipinda china chandende kufikira china, onse ankanena chimodzimodzi mopitiriza kuonetsa kuti anali wosachimwa.

Koma m'chipinda china wandende mmodzi adalibe chonena. Modabwitsika, Fredrick adaseleula motere naye, "ndiyesa inunso ndinu wosalakwa."
"Ayi mfumu yanga," munthuyo adayankha, "ine ndine wolakwa ndithu ndipo chilangochi ndichondiyenera." Ndipo mfumu idatembenukira kwa woyang'anira m'ndende naitana mofuula, "Idzani ndi kumtulutsa munthuyu mwachangu, asanafike poononga gulu la anthu osalakwali."

Kodi ife timakonzekera bwanji chiweruziro? nanga timamukonzekera bwanji Yesu khristu pakubwera kwache? Pongolapa moona mtima wachikhulupiriro kunena kuti: Inedi ndiyenera dipo la imfa chifukwa cha machimo anga, koma wina walowa m'malo mwanga ndikundipatsa ine chikhululukiro chozizwitsa.

Pangani chitsimikizo tsopano ndi kunena kuti kaya zivute bwanji kaya, mudzasunga ubale wanu maso ndi maso ndi Yesu kuti ukakhale woona wa pansidi pamtima.

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.