MPULUMUTSI WOPEZEKERATU
NTHAWI IRI YONSE

Pamene kam'nyamata kena kake ka mdziko la Scotland kochedwa Petro kanasowa usiku wina wamdima waukuru ku chire lina lake kumeneko lochedwa Wasteland, Mulungu anamuitana dzina lake; "Petro". Pamene mau akumwambawa adaitananso Petro anaima mukanjira kena kake, nayang'ana pansi, napeza kuti anatsala pang'ono kuti agwere mu ngalande yaikuru yomwe inakumbidwa ndi oswa miyala.

Kodi sizikadakhala zabwino kwambiri kuti aliyense wa ife amve kuitana kwa Mulungupa dzina lake? Sizikanakhala zabwino kuti Mulungu akhale bwenzi lathu lapafupi - ife titangoti tikhale pansi naye pamodzi ndi kucheza naye nthawi yaitali pa za mavuto ndi maloto athu?

1. MWAYI WOPANDA MALIRE WOLUMIKIZANA NDI YESU

Kaya mufuna kuti mukhulupirira, kaya ayi, koma dziwani kuti titha kudza chifupi ndi Yesu panopa koposa mmene zinaliri nthawi yomwe Iye anali m'dziko lapansi nafe, wooneka mwa umunthu. Kukhala ndi Yesu mwa thupi mdera lathu, ndi chinthu chopambana ndithu, koma tangoganizirani khamu limene lingamutsatire nthawi zonse kuti limuonetsetse. Nanganso nthawi yomuonera? Tikanatha ife kungokhala nayo mphindi yochepa basi kucheza naye m'moyo wathu wonse.

Yesu akufuna kukhazikitsa ubale weniweni ndi wina aliyense wa ife. Ichi ndi chimodzi mwa zifukwa zomwe Iye anachoka kudziko lino lapansi pa utumiki wapadera kumwamba umene ungampange Iye kudza chifupi nafe aliyense wa ife tsiku liri lonse. Popeza kuti Yesu siali malo amodzi okha ayi monga mmene zinaliri pamene anali m'dziko lapansi pano, mwa mzimu woyera, ali paliponse kutsogolera munthu aliyense ndi moyo wake payekhapayekha, ngati munthuyo ali wofuna kutsogoleredwako.

Kodi ndi lonjezo la chilimbikitso lotani lomwe Yesu anapereka asanakwere kunka kumwamba?

"Ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano." - Mateyu 28:20.

Kodi kristu akuchita chiyani kumwamba chomwe chingapangitse kuti "akhale nanu masiku onse".

"Popeza tsono TIRI NAYE MKULU WA NSEMBE WOTHA kumva chifundo ndi zofooka zathu, koma woyesedwa m'zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo. Yesu mwana wa Mulungu Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wachifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi yakusowa." - Aheberi 4:14-16.

Onani inu chitsimikizo cha chilimbikitso chotilonjeza kukhala naye Yesu ngati wotiimirira wathu wathu kumwamba; " Woyesedwa munjira zonse, monga mmene ifenso tiriri". "Womva chisoni nafe mu zofooka zathu". "Wotithandiza mnthawi ya kusoweka kwathu", ndi Yesu monga mkulu wansembe, ife sitiri otsekeredwa kapena okhala kutali ndi kumwamba ayi. Yesu atha kutilowetsa ife kumwamba pamaso pa Mulunguyo. Ndi chosadabwitsa kuti ife tikupemphedwa "kudza ku mpando wa chisomo molimba mtima".

Kodi Yesu akukhala malo ati kumwambako?

"Koma Iye (Yesu), mmene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala PA DZANJA LAMANJA LA MULUNGU," - Aheberi 10:12.

Khristu wamoyo - amene amamvetsetsa - ndiye wotiimira ku mpando wachifumu " kudzanja lamanja la Mulungu".

Kodi moyo wa Yesu udali bwanji kuti afike pokhala mkulu wathu wansembe?

"Potero kudamuyenera kufafanizidwa ndi ABALE mzonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wa chifundo ndi wokhulupirika mzinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu. Pakuti popeza adamva zowawa poyesedwa yekha, AKHOZA KUTHANDIZA iwo amene ayesedwa." - Aheberi 2:17, 18.

"M'bale" wathu yemwe anagawana nafe umunthu wathu ndipo wakhala " woyesedwa" monga mmene ife tiri, ali wamkuru wathu wansembe kudzanja la manja la Mulungu. "Wopangidwa monga ife", amadziwa zonse zomwe tikukumana nazo. Iye anakhalaponso wanjala, waludzu, anayesedwa, namva kutopa. Anaona kufunika komveredwa chisoni ndikumvetsetsedwa.

Koma pamwamba pa zonsezi, Yesu anafikira pokhala wansembe wamkuru chifukwa anafa kuti apereke nsembe yotetezera " ku machimo athu. Analipira dipo lonse la machimo athu pofa m'malo mwathu, Uwu ndi uthenga wabwino kwa munthu aliyense, kulikonse ndi kunthawi iri yonse.

Mmodzi wa atsogoleri a masukulu athu ophunzirako za m'bukhu lopatulika akufuna kugawana nafe zomwe adakumana nazo motere: Pamene mwana wathu wamkazi wamng'ono adali ndi zaka zitatu, adapanitsa chala chake ku mpando nathyola fupa. Pamene tinathamangira naye kwa dotolo, kulira kwake kofuula ndi ululu kunadetsa nkhawa mitima yathu ndipo kunamukhuza mwapadera mwana wathu wina wa zaka zisanu. Ndipo sindikuiwala mau omwe adalankhula pamene dotolo adamaliza kumusamalira mbale wake wovulalayu. Mosisima adati. "Oh! Adadi, ndikadalakalaka chikadakhala chala changa!"

Pamene dziko lonse la anthu lidaphwasuka ndi uchimo ndi kuyenera kufa kwamuyaya, Yesu anati; "Oh, Atate, ndikulakalaka ndikadakhala Ine." Ndipo Atate anampatsa Iye, Yesuyo, mongamwa kulakalaka kwake pa mtanda.

Mpulumutsi wathu waona zowawa zonse zomwe ife tikukumana nazo - ndiponso kuposerapo!

2. UTHENGA WA MU CHIPANGONO CHAKALE

Pamene ana a Israyeli adasonkhana mmunsi mwa phiri la Sinayi, Mulungu adawalangiza kupyolera mwa Mose, kuti amange kachisi woyenda naye kuti adzipembedzeramo. "Motsatira momwe Iye adawalangizira iwo kudzera mwa Mose, paphirilo la Sinayi" (Eksodo 25:40). Patangopita pafupifupi zaka Mazana asanu, Mfumu Solomoni Adamanga kachisi wamkulu wolowa mmalo mwa kachisi wonyamulikayu. Ndipo kachisiyu adamangidwa motsatira ndondomeko yomweyo ya kachisi wamng'ono uja yemwe Mose adalangizidwa kumanga pa phiri la Sinayi.

Pamene Mulungu adampatsa Mose ndondomeko ija kamangidwe ka kachisiyu, kodi iye adaona kufunika kwa mtundu wanji mumtima mwake?

"Ndipo andimangire malo opatulika, KUTI NDIKHALE PAKATI PAO." - Eksodo 25:8.

Uchimo udalekanitsa munthu ndi mlengi wake. Kachisi inali njira ya Mulungu yoonetsera mmene iye angalumikizaniranenso ndi kukhala nafe. Kachisi, kapena nyumba ya Yehova, inasandulika chilikati cha moyo wachipembedzo ndi matamando mu nthawi ya chipangano chakale. Mmawa uli wonse, anthu ankasonkhana mozugulira kachisi nalumikizana ndi Mulungu m'mapemphero (Luka 1:9, 10) kuitanitsa lonjezano la Mulungu: "Ndidzakumana nanu" (Eksodo 30:6).

Chipangano chakale tikuphunzitsidwa uthenga womwewo wa chipulumutso mmene ukupezekanso m'chipangano chatsopano. Zonsezi zikuonetsera Yesu wotifera ndi kutitumikira ife ngati wansembe wankuru mu kachisi wa kumwamba.

3. UTUMIKI WA YESU KWA IFE UNAONETSEDWA MKACHISI WA CHIPANGANO CHA KALE

Kachisi ndi atumiki ake onse amavumbulitsira ife zomwe Yesu akuchita panopa kumwamba mkachisi wa kumeneko; ndiponso zomwe akuchita panopa m'dziko lino lapansi kuti akatidzadza ndi kutitsogolera ife m'moyo wathu wa tsiku ndi tsiku.

Mu mitu ya 25 mpaka 40 ya bukhu la Eksodo, muli dongosolo la utumiki ndi miyambo ya kachisi wa mchipululu mwatsatanetsatane. Chidule chake cha kamangidwe ndi zopezeka mkachisimo chikuonetsedwa mu chipangano chatsopano.

"Ndipo lingakhale chipangano choyamba chinali nazo zoikika zakulambira, ndi malo opatulika apadziko lapansi…. M'menemo munali choikapo nyali, ndi gome, ndi mkate woonekera, apa panali pa malo opatulika. Koma mkati mwa chophimba chachiwiri, chihema chonenedwa malo opatulikitsa, okhala nayo mbale ya zofukiza ya golidi ndi likasa la chipangano, lokuta ponsepo ndi golidi momwemo munali mbiya ya golidi yosungamo mana. Mulikasamo munali…. Magome a miyala a chipangano (Pomwe Mulungu adalembapo Malamulo khumi (Denteronomo 10:1-5). Ndipamwamba pa che pa Likasa Akerubi a ulemerero akuchititsa mthunzi pachotetezerapo (mpando wachisomo)." - Aheberi 9:1-5.

Kachisiyu adali ndi zipinda ziwiri, malo opatulika ndi malo opatulikitsa. Kutsogolo kwa kachisiyi kunakonzedwa bwalo. Pabwaloli panali guwa la nsembe la mkuwa pomwe wansembe amaotchera nsembe, ndi mbiya yomwe amasambiramo m'manja.

Nsembe zoperekedwa pa guwa lamkuwali zimaimira Yesu, Yemwe kupyolera mu imfa yake ya pamtanda anasandulika. "Mwana wankhosa wa Mulungu, yemwe achotsa chimo lake la dziko lapansi" (Yohane 1:29) pamene wochimwa analapadi kusiya machimo ake paguwa amalandira chikhululukiro ndi chiyeretso. Mwa njira yomweyonso, wochimwa wa lero amalandira chikhululukiro ndi chiyeretso kupyolera m'mwazi wa Yesu (1 Yohane 1:9).

M' chipinda choyambachi, malo opatulika choikapo nyali zisanu ndi ziwiri mu nthambi zake zisanu ndi ziwiri zinali kuyaka nthawi zonse, kuonetsera kuti Yesu wosalepherayo "Kuunika kwa dziko lonse lapansi" (Yohane 8:12). Gome lokhala ndi mkate wopatulidwa limaimira Yesu wopezekeratu nthawi iri yonse pamene tiri ndi njala yauzimu, natikhutitsanso mu njala yathu yakuthupi. "Mkate wamoyo" (Yohane 6:35).

Guwa la golidi la zonunkhira linaimira moyo wa Yesu wapemphero lakwa ife pamaso pa Mulungu mwini (Chibvumbulutso 8:3, 4).

Chipinda chachiwiri, malo opatulikitsa, munali likasa lachipangano lokuta ndi golidi. Iloli limaimira mpando wachifumu wa Mulungu chokhalirapo chaka cha chisomo, kapena chotetezera chimaimira mapemphero otetezera a Yesu, Wansembe wathu wamkuru, kupemphera mmalo mwa mtundu wa anthu wochimwa, omwe aswa malamulo a Mulungu a chikhwalidwe. Magome awiri a miyala pomwe padalembedwa malamulo khumi anali pansi pa mpando wachisomo. Akerubi a golidi aulemerero anazungulira mokuta mpandowu mmapeto aliwonse a likasali. Nyali yowala mwaulemerero inaikidwa pakati pa Akerubi awiri, chizindikiro choti Mulungu mwini anali pomwepo.

Chinsalu chinaphimba malo opatulika kuti anthu asathe kuonako pamene wansembe anali kuwapempherera pabwalopo. Nsalu yachiwili inali kutsogolo kwa malo opatulikitsa kumphimbira kuti wansembeyu yemwe anali mchipinda choyambachi cha malo opatulika.

Pamene Yesu anafa pamtanda, chidachitika ndi chiyani ku nsaluyi?

"Ndipo onani chinsalu chochinga ca mkachisi chinang'ambika pakati, kuchokera kumwamba kufikira pansi," - Mateyu 27:51.

Malo opatulikitsa anaonekera pamene Yesu anafa. Itatha imfa ya Yesu, panalibenso chochingira pakati pa Mulungu woyera ndi wokhulupirira moona, Yesu, wansembe wathu wamkuru, akutiitanira ife kwa Mulungu (Aheberi 10:19-22).

Tiri ndi mwayi ife wopita kumpando mchipindacho chachifumuncho kumwamba chifukwa choti Yesu ndiye wansembe wathu wankuru kudzanja lamanja la Mulungu. Yesu akutiyenereza ife kufika pamaso pa Mulungu ndi pa mtima wa chikondi wa Mulungu. Choncho " tiyeni tidze chifupi ndi Iye".

4. CHIVUMBULUTSO CHA KHRISTU KUTIFERA KUTI TIPULUMUKE

Monga momwe kachisi woyambayo adali ngati nyumba ya Mulungu yaing'ono momwe Yesu anali kutumikira mmalo mwaife, Zochitika zake mmenemo zinali "Zofanana ndi Kapena chithunzithunzi cha zomwe ziri kumwamba" (Aheberi 8:5). Koma pali kusiyana kwina kwake koonekeratu: Ansembe omwe amatumikira mukachisimo samatha iwo kukhululukira chimo, koma pamtanda Yesu, " anaonekera kamodzi kokha nthawi yonse yadziko lapansi mkuchotseratu chimo kupyolera mu nsembe yodzipereka Iye mwini" (Aheberi 9:26).

Chipangano chakale, m'bukhu la Levitiko, tikumva mwatsatanetsatane dongosolo la utumiki omwe umachitika mukachisiyo. Miyambo ndi mautumiki ake zinagawidwa pawiri. Utumiki wa tsiku ndi tsiku, ndi mwambo wa utumiki wa pachaka (monga tidzaphunzira mu phunziro lotsogolera la khumi ndi chitatu).

Mu utumiki watsiku ndi tsiku, wansembe amapereka nsembe ya munthu aliyense mumpingo wonse. Pamene munthu anachimwa, amabweretsa nyama yamoyo yopanda banga kapena chilema monga ngati chopereka kuti chimo likhulukidwe, " naika manja ake pamutu panyamayo ndikuiphera pa malo operekera nsembe" (Levitiko 4:29). Uchimo wa munthuyo umalowa mwa nyamayo yosalakwa ponena machimo ake otaika manja ake pa nyamayo. Izi zinaimira khristu wosenza machimo anthu onse pa Karivala, iye wosachimwa "nakhala chimo m'malo mwathu" (2 Akorinto 5:21). Nyama yansembeyo inayenera kuphedwa ndi mwazi wake nukhetsedwa chifukwa zimalosera ku dipo lalikuru lomwe Khristu analizunzikira pa mtanda.

5. CHIFUKWA CHIYANI MWAZI?

"Popanda kukhetsa mwazi, palibe chikhululukiro" (Aheberi 9:22). Zomwe zinachitika mu kachisi wa m'chipangano chakale zimaonetsera Khristu ndi ntchito yake yopulumutsa. Atatha kutifera ife ku machimo athu, adalowa malo opatulika "kamodzi kokhako kokwanira ndi mwazi wake, atapeza chiombolo chosatha" cha ife (vesi 12). Pamene mwazi wa Yesu unakhetsedwa pa mtanda chifukwa cha machimo athu "Chinsaru cha mkachisi (Mu Yerusalemu) chinang'ambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi" (Mateyu 27:51) chifukwa cha Yesu kudzipereka nsembe pa mtanda, nsembe za nyama sizinali ndipo sizili zofunikanso ayi.

Pamene Yesu anakhetsa mwazi wake pamtanda, amapereka moyo wake wangwiro ndi womvera ngati cholowa m'malo mwa zolephera zathu. Pamene atate ndi mwana analekanitsidwa pa karivali, atate anatembenukira kumbali ndikumva kupweteka ndipo mwanayo anafa chifukwa chosweka mtima. Mulungu mwana analowa mu mbiri yodzitengera Iye yekha mphoto yake ya uchimo ndi kuonetsera m'mene tchimo limaonongera. Tsono akanatha kukhululukira wochimwa aliyense mopanda kulichepetsa vuto la chimolo. Kristu anapanga " mtendere m'mwazi wake,wokhetsedwa pa mtanda" (Akolose 1:20).

6. BVUMBULUTSO LA YESU YEMWE ALIPO KUTIPULUMUTSA IFE

Kodi ntchito ya Yesu tsiku ndi tsiku ndiyotani mu kachisi wa kumwamba?

"Kuchokera komweko akhoza kupulumutsa konsekonse iwo akuyandikira kwa Mulungu mwa Iye, popeza ali nawo moyo wace chikhalire wa kuwapembedzera iwo." - Aheberi 7:25.

Panopa Yesu "akukhala" kupereka moonetsera mwazi wake, nsembe yake, m'malo mwa ife. Panopa akugwira ntchito molimbika kupulumutsa munthu aliyense kuchoka ku tsoka lobwera ndi chimo. Anthu ena molakwitsa amaganiza kuti, Yesu, monga wotiimira potipempherera, ali kumwamba kupempha Mulungu wosafuna kukhululukayo, kuti atikhululukire. Koma choti tidziwe ndi choti, ndi Mulungu yemweyo yemwe mokondwa analola kulandira nsembe ya mwana wake yochitikira chifukwa cha ife.

Monga wansembe wathu wamkuru, Yesu kumwambako, akudandaulira mtundu wa anthu. Akugwira ntchito yobweretsa maganizo ena a chisomo kwa anthu osiyana maganizo, komanso chiyembekezo kwa iwo amene akusowa chochita ndi zobvuta zamoyo, kupyolera onse kupeza chuma choposa mu mawu a Mulungu ndim'mphamvu ya pemphero. Yesu akuiumbanso miyoyo yathu kuti igwirizane ndi Malamulo a Mulungu ndi kutithandiza kukula mu makhalidwe athu kuti tikathe kudzaima nji pa Iye munthawi ya msautso ndi mayesero.

Mulungu anataya moyo wake chifukwa cha munthu wina aliyense wokhala pa dziko lapansi. Ndipo panopa, monga wansembe wamkuru ndi m'khalapakati, "alipo nthawi zonse" kutitsogolera ife anthu ake kuti tikailandire imfa yake kuti ndiyo yachifukwa cha machimo athu.

Ngakhale anayesetsa kuliyanjanitsanso dziko lapansi lakugwalo ku chiyanjano chatsopano ndi Iye pamtanda, sangathebe kutipulumutsa pokhapokha titalandira ndi kuvomereza chisomo chake. Anthu sadzataika chifukwa choti iwo ndi wochimwa ayi, koma chifukwa chakuti akana kuvomereza chikhululukiro chamachimo chimene Yesu wapereka.

Chimo lidaononga ubale weniweni womwe udalipo pakati pa Adamu ndi Hava ndi Mulungu wawo, womwe amasangalala nawo. Koma Yesu, monga mwana wa nkhosa wa Mulungu, anafera mtundu wonse, kumchotsa ku chimo mwaulere; ndi kubwezeranso ubale uwo womwe udasokonezekawo. Kodi inunso mwapeza kuti Iye ali mkulu wanu wansembe, amene akhala ku nthawi zonse kubweretsa ubalewo pafupi ndi kumpanga weniweni?

Imfa yodzipereka nsembe ya Khristu ndi yapayokha. Utumiki wa Yesu Khristu kumwamba ndiyosayerekezeka ndi china chilichonse. Ndi Khristu yekha yemwe amamubweretsa Mulungu pafupi pathu. Ndi Khristu yekha amene amapanga zotheka kuti mzimu woyera wopatulika akhala m'mitima yathu. Anadzikhuthula Iye ngati wopanda kanthu kuti ife tikakhale athunthu. Iyenso akuyenera kuti ife tikadzipereke kwa Iye chomwecho. Tiyeni timulandire kwanthunthu Iye ngati Mpulumutsi ndi mbuye wa miyoyo yathu.

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.