MPHAMVU YODABWITSA M'MOYO WANGA

Muchaka cha 1929, munthu wina wotchedwa Frank Morris adakwera nawo Sitima yapanyanja yopita ku Switzerland. Ulendo umenewu ankaudikilira kwa nthawi yaitali. Koma unali ulendo wosautsa. Yemwe anali womutumikira mu sitimayo ankamutsekera iye mukachipinda usiku uli wonse. Atatha kudya chakudya cham'mawa mofulumira, Frank ankatha kuchita masewera olimbitsa thupi pang'ono, koma samamva kumasuka kuti adzichitidwa monga ngati chiweto kuti adzitsogoleredwa kuzungulira sitimayo. Kenaka womuyang'anirayo anamukhazika iye pa mpando wa mu sitimayo. Nthawi zonse pamene adakumana ndi wokwera sitima wina yemwe anali ngati bwenzi namuitanira kukayenda woyang'anirayu adamukaniza nanena kuti iye waikidwa kumuyang'anira iye mosamalitsa.

Frank anali wamkulu, wachidwi ndi zofuna ngati munthu wamkulu. Komanso anali wosaona, ndipo womutumikirayu adaona kuti Frank sangadzitumikire yekha. Frank anali ngati katundu wopangidwa ndi kutumizidwa mopanda iye kunenapo kanthu.

Koma atafika ku Switzerland, moyo wa Frank udasintha modabwitsa. Ali komweko adaphunzira kuti panali galu ophunzitsidwa bwino kutsogolera anthu akhungu. Pomubweretsa m'busa wina wa ziweto wa ku German wotchedwa Buddy ku America kunapangitsa Frank kuyambitsa bungwe lalikulu pa dziko lonse lapansi loona za maso.

Ndi Buddy, pambali pake, Frank anatha kupita pali ponse, nthawi iri yonse ndi ali yense. Ndipo anali womasuka tsopano. Nthawi ina, ali pachionetsero kwa atolankhani pa msewu wina wodutsa magalimoto ndi zokwera zambiri mu mzinda wa New York , Buddy adamutsogolera mbuye wake mwa luso kuchoka mu msewu wina kupita msewu winanso, pamenepo magalimoto ambiri akudutsanso mwaliwiro. Chifukwa chomudalira ndi kumukhulupirira Buddy kwambiri, Frank adadutsa misewu mosavuta. Atolankhani adavutika kudutsa mpaka wina wa iwo adapeza galimoto ndikukwera kuti apite mbali ina.

Mu ndime zotsatirazi, tiphunzira za Mzimu woyera, wotsogolera amene amafuna ife kuti tiike miyoyo yathu m'manja mwake. Tonsefe ndife wolumala mwa umunthu, khungu tiri nalo ku zinthu zomwe ziri zofunika. Ndipo nthawi ya moyo wathu iri yofulumira kwambiri moti tinangopezeka kuti tikungotsatira zinthu zina, m'malo mopita chitsogolo. Ndipobe, tiri okaikira kuti tikhulupilire miyoyo yathu kwa wina wake kuti atitsogolere. Koma chofufuzidwa chopezeka chenicheni chikutidikirira ife ndi ichi: tidzapeza ufulu weni-weni ndi mphamvu pozamitsa chidaliro chathu pa Mzimu woyera kuti atitsogolere ife moyo wathu wonse.

1. WOIMIRA KHRISTU M'DZIKO LAPANSI

Pamene Yesu anali pafupi kukwera kunka kumwamba, anawalonjeza ophunzira ake mphatso yaulere:

"Koma ndinena Ine choonnadi ndi inu, kuyenera kwa inu kuti ndichoke Ine; pakuti ngati sindichoka, NKHOSWEYO sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma Iye kwa inu… Koma atadza Iyeyo, MZIMU WA CHOONADI, adzatsogolera inu m'choonadi chonse… IYEYO ADZALEMEKEZA INE; chifukwa adzatenga za mwa Ine nadzalalikira kwa inu." - Yohane 16:7, 13, 14.

Mu chikonzetsero choyeracho, Yesu anayenera kubwerera kumwamba ngati wotiimilira kwa Mulungu, naonekera m'malo mwa ife pamaso pa mpando wake wa Mulungu" (Ahebri 9:24). Pamene Ambuye wathu wopachikidwayo akutiimilira kumwamba, tirinso ndi NKHOSWE ndi WOTITSOGOLERA, ndiye Mzimu woyera, pansi pompano. Iye ndiye woimilira Yesu Khristu.

Ali padziko lapansi pano, Yesu adatumikira mbali zonse za thupi la munthu, ngakhale sanathe kupezeka pali ponse. Koma mzimu woyera alibe malire; atha kutumikira ngati nkhoswe ndi mtsogoleri kwa anthu osawerengeka ku malo ambiri nthawi imodzi. Khristu amathetsa zosowa zathu kupyolera mwa mzimu woyera.

2. KODI MZIMU WOYERA NDI NDANI?

Ambiri aife tingathe kulumikizana ndi Mulungu Atate ngati titathanso kuganizira, chisamaliro chomwe Iye amatipatsa chomwe sichinaonekenso ndi kale lonse, Iye ngati kholo lathu. Ndipo titha kuona Yesu Mwana Wake, chifukwa anakhalanso Iye monga munthu ngati ife mudziko lomwe lino. Koma Mzimu woyera, ndikovuta kuika pa chithunzi-thunzi chake ndi kuyerekeza kwake. Tiribe chamunthu chomwe tingayerekezere ndi mzimu woyera, komabe Bukhu lopatulika limatipatsa ife dongosolo leni-leni la Mzimu woyera.

KHALIDWE: Yesu anayerekeza Mzimu woyera monga munthu m'modzi wa atatuwo mu uMulungu, wokhala nawo pamodzi ndi Mulungu Atate ndi Mulungu Mwana.

"Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, ndikuwabatiza iwo m'dzina la ATATE, ndi la MWANA, ndi la MZIMU WOYERA." - Mateyu 28:19.

Mzimu uli ndi khalidwe lake-lake: maganizo (Aroma 8:27); nzeru (1 Akorinto 2:10); chikondi cha kwa ife (Aroma 15:30); kutha kutiphunzitsa (Nehemiya 9:20); kumva chisoni pamene tichimwa (Aefeso 4:30); ndi mphamvu yakutsogolera.

KUKHALA NAWO PA CHILENGEDWE: Mzimu woyera anali nawo pachilengedwe cha dziko lapansi pamodzi ndi Atate ndi Mwana.

"PACHIYAMBI Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi… ndipo MZIMU WA MULUNGU unalinkufungatira pamwamba pa madzi." - Genesis 1:1, 2.

3. NTCHITO ZA MZIMU WOYERA

(1) Kusintha mtima wa munthu. Pamene adakumana ndi Nikodimo, Yesu adatsimikizira mbali yomwe Mzimu woyera amachita pakusintha mtima wa munthu.

"Yesu anayankha nati, 'indetu, indetu ndinena ndi iwe, ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi mzimu, sakhoza kuona ufumu wa Mulungu.'" - Yohane 3:5.

Kubadwa "mwa Mzimu" zitanthauza kuti Mzimuyo amatiyambitsa moyo watsopano. Sikungosintha makhalidwe athu kokha ayi, koma kusinthika kwa mkati ndi kunja komwe, kukwaniritsa malonjezo oti: "Ndidzakupatsani inu mtima watsopano (Ezekiel 36:26).

(2) Kutidziwitsa ife zoipa zomwe tachita ndikutipatsa chikhumbo-khumbo cha chiyero.

"Ndipo atadza Iyeyo (Mzimu Woyera) ADZATSUTSA DZIKO LAPANSI za machimo, ndi za chilungamo, ndi za chiweruzo." - Yohane 16:8.

Mukamva za nthano za wina yemwe adasinthika modabwitsa kuchoka ku moyo watchimo kupita kwa Mulungu nakhala m'banja wokhulupirika ndi kholo losamala, kumbukirani kuti khwerero liri lonse adatenga, lidadza ndi kudandaulira kwa Mzimu woyera.

(3) Kutitsogolera ife m'moyo wathu wachikhristu. Yesu analankhula nafe mwachindunji kupyolera m'mawu aang'ono "akachete-chete" a Mzimu.

"Ndipo makutu ako adzamva mawu kumbuyo kwa iwe akuti, 'njira ndi iyi, yendani inu m'menemo.' Potembenukira inu ku lamanja, ndipo potembenukira ku la manzere." - Yesaya 30:21.

Kupyolera pa Kanema, zinthu zambiri zakutali ku dziko lonse lapansi taziona pafupi ndi maso athu. Mzimu woyera amakhala ngati uthenga wa pakanema wa Mulungu, kumubweretsa Yesu pafupi kuchokera kumwamba kudza kudziko lapansi, ndikumupanga Iye wopezekeratu panthawi iri yonse imene timufunitsitsa (Yohane 14:15-20).

(4) Kutsogolera moyo wa mapemphero.
"Ndipo momwemo MZIMU ATHANDIZA KUFOOKA KWATHU pakuti chimene tizipempha monga chiyero; sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka… monga chifundo cha Mulungu." - Aroma 8:26, 27.

Pamene tivutika kupeza mawu, Mzimu amapemphera m'malo mwathu. Pamene takhumudwitsidwa, tingathe kulilira kwa Mulungu kokha, ndipo Mzimu amakulitsa chikhulupiliro cha kulira kwathu kuchoka mukuchepa kwake kufikira ku pemphero lamphamvu lofikiratu pa mpando wake wachifumu wa Mulungu kumene Yesu ali kutumukira.

(5) Kukuza makhalidwe ndi maonekedwe a Chikhristu. Mzimu amapangitsa anthu opanda chipembedzo kukhala obala zipatso zauzimu.

"KOMA CHIPATSO CHA MZIMU ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiliro, chifatso, chiletso, pokana zonsezi palibe lamulo." - Agalatiya 5:22, 23.

Kukhala ndi mphatso za Mzimu zimaonetsera kuti ife tiri m'nthawi yolumikizidwa ku mpesa weni-weni, Yesu (Yohane 15:5). Yesu atha kukhala moyo wake wonse mwa ife kupyolera mwa Mzimu woyera ndi mphamvu zake.

(6) Kutikonzetsera ife kukhala mboni. Yesu akulonjeza:

"KOMATU MUDZALANDIRA MPHAMVU, Mzimu woyera atadza pa inu, ndipo mudzakhala MBONI… kufikira malekezero ache a dziko." - Machitidwe 1:8.

Onse omwe ali olola, angathe kukhala mboni motsogozedwa ndi Mzimu. Sitingathe ife kukhala ndi mayankho, koma Mzimu adzatipatsa mayankho ndi nthano zomwe zidzatha kusintha mitima ndi maganizo a anthu. Atumwi anali ndi vuto kuti amvane pa tsiku la Pentekosite, koma Mzimu woyera atabwera, adanena ndi mphamvu, za Yesu Khristu mpaka "adalitembenuza dziko chadodolido. (Machitidwe 17:6).

4. MPHATSO ZA MZIMU WOYERA

Mawu a Mulungu akulekanitsa momveka bwino pakati pa Mphatso ya Mulungu ya Mzimu woyera kwa aliyense kuti akhale MKHRISTU wopambana m'moyo; ndi mphatso zosiyana-siyana zomwe Mzimu anapereka kwa wokhulupilira kuti atumikire mwapadera mwa njira zosiyanasiyana.

"Chifukwa chake ananena, m'mene anakwera (Khristu) kumwamba, anamanga ndende undende, namuika za ufulu kwa anthu…. Ndipo Iye anapatsa ena akhale ATUMWI, ndi ena ANENERI, ndi ena ALALIKI, ndi ena ABUSA, ndi ena APHUNZITSI, kuti akonzere oyera mtima ku ntchito ya utumiki kumangilira thupi la Khristu." - Aefeso 4:8, 11-12.

Mkhristu m'modzi salandira mphatso zonsezi ayi. Ena atha kulandira zingapo kuposera anzawo. Mzimu Woyera "amapereka kwa iwo molingana ndi m'mene Iye Mzimuyo akuonera" (1 Akorinto 12:11). Mzimu woyera amamuzamitsa wokhulupilira aliyense mu ntchito yake malinga ndi chikonzetsero cha Mulungu. Mulungu amadziwa nthawi ndi malo kumene kufunikira mphatso iri yonse kuti zikadalitse anthu ake ndi Mpingo wake.

Mum'ndandanda wina wa mphatso za mzimu woyera ukupezeka pa 1 Akorinto 12:8-10 ndipo zina za izo ndizo nzeru , chidziwitso, chikhulupiliro machiritso, ulosi, kulankhula malilime osiyana-siyana (manenedwe, zilankhulo), ndi kutanthauzira kwa malirimewa (vesi 8-10).

Paulo akutiumiriza ife kuti "tikhumbe modzipereka ndi mofunitsitsa mphatso zimenezi," ndipo akunenanso kuti, "ndipo tsopano ndidzakuonetserani inu njira yopambana zonse" (1 Akorinto 12:31).

Mutu wonena za chikondi (1 Akorinto 13) umene ukubwera patsogolo pa vesili umatsimikizira kuti, "njira yopambana zonse," ndiyo njira ya chikondi. Ndipo chikondi ndi mphatso ya Mzimu (Agalatiya 5:22).

Ife tiyenera kukhudzidwa ndi kufuna-funa mphatso za Mzimu ndi kulola Mzimuyo kutigawira ife mphatsozo monga momwe "Iye afunira" (1 Akorinto 12:11).

5. KUKWANIRA KWA MZIMU PA PENTEKOSITE

Pa tsiku la Pentekosite, Mzimu woyera adatsanulidwa mopanda malire, kukwaniritsa lonjezo la Yesu:

"Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu woyera atadza pa inu; ndipo mudzakhala mboni zanga… kufikira malekezero ake adziko." - Machitidwe 1:8.

Pa Pentekosite, Mzimu anapangitsa atumwi kufalitsa uthenga momveka bwino mu ziyankhulo za mtundu wina uli wonse wa anthu "a dziko liri lonse la pansi pa thambo" (Machitidwe 2:3-6).

Ophunzira a Bukhu lopatulikali ambiri amayerekeza kudza kwa Mzimu woyera kumeneku ndi mvula yoyambilira ya nyundo ndi mvula yotsiliza ya masika ya ku Palestina (Yoweli 2:23).

Mzimu yemwe adabwera pa Pentekosite anali ngati "Mvula yoyambilira" ya nyundo yomwe imameretsa mbeu naipereka chakudya chofunikira ku mpingo wa Khristu mu Chiyambi chake.

6. MVULA YOTSIRIZA YAMASIKA YA MZIMU WOYERA

Ulosi wa m'Bukhu lopatulika umatiuza za tsiku likubwera pamene Mzimu wa Mulungu udzatsanulidwa ku mpingo wake ngati mvula, kuwapatsa anthuwo mphamvu, kuti akachitire umboni (Yoweli 2:23).

Zaka zambiri zadutsa ndithu pamene nthano ya chipulumutso yafalitsidwa ku mbali yaikulu ya dziko lapansi. Ndi nthawi ino tsopano kuti "mvula ya Masika" ichetse mbewu, kuzikhwimitsa, kuti zikathe kukololedwa.

Pamene mbiri ya dziko lapansi ikufika pachimake peni-peni, Yesu asanabwere, Mulungu adzakonzetsera wokhulupilira aliyense, kupyolera mu mphanvu yaikulu ya Mzimu woyera, kuti akalowe kumwamba. Kodi inu mutha kuona mphamvuyi ya "mvula yoyamba" yokonzetsera mpingo ku "mvula yamasika" ya Mzimu woyera? Kodi mukukhala inu m'moyo wodzadzidwa ndi Mzimu? Pamene mulimbikitsidwa inu ndi Mzimu, mungalole kodi Mulungu kukugwiritsani ntchito yofalitsa za chikondi chake choposa ndi kudza kwake kwa posachedwa?

7. ZOYENEREZA MUNTHU KULANDIRA MZIMU WOYERA

Pa Pentekosite, Mzimu woyera anakhudza iwo amene anamva Mawu a Mulungu, nadzifunsa molira kuti, "kodi abale, tidzachita chiyani?" (Machitidwe 2:37).

"Koma Petro anati kwa iwo, 'LAPANI, BATIZIDWANI yense wa inu m'dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu, ndipo MUDZALANDIRA MPHATSO YA MZIMU WOYERA.'" - Machitidwe 2:38.

Kulapa - kuchoka ku njira za uchimo ndi kubwelera kwa Khristu, ndiyo njira imodzi yoyenera kulandira mphatso za Mzimu woyera. Kuti Mzimu atsanuliridwe pa ife, tiyenera kuyamba talapa ndi kuipereka miyoyo yathu kwa khristu. Yesu anatsimikiziraponso pa za kufunitsitsa kum'tsatira Iye ndi kumumvera Iye ngati njira ina yotiyenereza ife kulandira mphatso za Mzimu woyera (Yohane 14:15-17).

8. MOYO WODZADZIDWA NDI MZIMU

Yesu asanachoke pa dziko lapansi, anawalangiza ophunzira ndi omutsatira ake motere:

"Musachoke mu Yerusalem, komatu mulindire lonjezano la Atate, limene anati, munalimva kwa Ine… pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu woyera, asanapite masiku ambiri." - Machitidwe 1:4, 5.

Posanthula-santhula m'Bukhu lopatulika tisonyezedwa kuti Mkhristu ayenera "kudzadzidwa ndi Mzimu woyera" (Machitidwe 2:4; 4:8; 4:31; 6:3; 6:5; 7:55; 9:17; 13:9; 13:52; 19:6). Mzimu woyera umapangitsa moyo wamunthu kukhala wokwaniritsa ndi wabwino chifukwa moyo wodzadzidwa ndi Mzimu umafikiritsa mbendera zonse zomwe Khristu ali nazo pa ife.

Pamene tikulongosola za moyo wodzadzidwa ndi Mzimu wa chikhristu, Paulo akupereka pemphero iri loti likanenedwe ndi wokhulupilira aliyense:

"Kuti monga mwa chuma cha ulemelero wake akulimbikitseni inu ndi mphamvu mwa Mzimu wake, m'kati mwanu, kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiliro m'mitima yanu,… Ndipo kwa iye amene angathe kuchita koposa -posatu zonse zimene tizipempha, kapena tiziganiza, monga mwa mphamvu ya kuchita mwa ife." - Aefeso 3:16, 17, 20.

Monga Frank Morris ndi galu wake wokhulupirika pomutsogolera, Buddy, ifenso motsogozedwa ndi Mzimu woyera mkati mwathu, titha kuchita zinthu zambiri zosawerengeka zomwe sitinachitepo ndi kale lomwe. Ndi zikhumbo zatsopano ndi mphamvu zatsopano, ife titha kupita chitsogolo molimba mtima m'malo mongoyesa kuti tithane ndi zovuta za m'moyo.

Machita-chita odzadzidwa ndi Mzimu amapangidwanso mwatsopano tsiku ndi tsiku kupyolera mupemphero ndi kuphunzira mawu a m'Bukhu lopatulika. Pemphero limatiika ife pafupi zedi ndi Khristu pamene kuphunzira mawu a m'Bukhu lopatulika kumatipanga ife kuyang'ana kwambiri kwa Iye munjira zathu zonse. Izi zimaphwanya malinga onse otitchingira ife ndi Yesu Khristu kuti asatitsanulire mphatso zathu zaulele za Mzimu. Umu ndimo m'mene tikhalira, ndikuchotsa makhalidwe akale oipa ndikuikamo maonekedwe aukhondo a khalidwe lathu.

Aroma 8 amatilongosolera ife bwino maonekedwe a moyo wodzadzidwa ndi Mzimu. Pezani nthawi yanu muwerenge pamene mungathe, ndipo muwerenge kuti ndi nthawi zingati zomwe Paulo akulozera ku "Mzimu" monga mphamvu yokhayo ya moyo wachikhristu.

Kodi inu mwafufuza zozizwa zopezeka mu moyo wodzadzidwa ndi Mzimu? Ndinu wofunitsitsa kuti Mzimuyu akhale m'moyo mwanu? Kodi mwayamba kale kuona mphamvu yake yopatsa moyo? Tsegulani mitima yanu kumphamvu yaikuru iyi yomwe iri m'dziko lonse.

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.