KODI
KUBWERA KWA YESU Ambiri a ife takakamizika kufufuza za m'tsogolo. Tikufuna kudziwa zomwe ziri tsidya linalo, kutsogoloko. Koma chindunji chake cheni-cheni sichinapezekebe ayi. Tiri ndi nthawi yovuta ngakhale kudziwa kuti nyengo ya mawa ikhala yotani. Koma alipo wina amene ulosi wake umachitikadi. Mwachindunji, Yesu Khristu, kupyolera m'Mawu ake, atha kutionetsera ife kutsogolo; ndi wotitsogolera wodalirika. Mu phunziro iri, tiona zomwe Iye adanenapo za kubweranso kwake kwachiwiri. Ndiponso,ndani akadadziwa za kutsogolo kwadziko koposa Iye amene analilenga dzikolo. 1. ZIZINDIKIRO ZA M'MASIKU ATHU ZOSONYEZA KUTI YESU ADZABWERANSO Kodi Yesu atatha kuwatsimikizira ophunzira ake kuti adzabweranso kachiwiri ku dziko lapansi, (Mateyu 23:39), ophunzirawa adamufunsa kuti chiyani? "Mutiuza ife zija zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro cha kufika kwanu n'chiyani, ndi cha mathedwe a nthawi ya pansi pano?" - Mateyu 24:3. Yesu anawayankha momveka ndi mwachilimbikitso mu Mateyu mutu 24 ndi mutu 21 wa Luka. Iye akupereka yekha mwini "zizindikiro," kapena umboni umene ife tingadziwire kuti kudza kwake kwayandikira. Maulosi ena a m'Baibulo amathandizanso kukwaniritsa, ndi kutipatsa chinthunzi-thunzi cha m'mene tionere, maulosi amenewa akukwaniritsidwa tikuona ndi maso athu; kutitsogolera kuti kudza kwake kwa Yesu kwayandikira. Tiyeni tione zikwangwani khumi za ulosi wa m'Baibulo zapanjira yathu yopita kumwamba, ndipo tifufuza ndi mafunso omwe munthu paulendo angadzifunse poona zikwangwani zapamsewuzo. CHIKWANGWANI CHOYAMBA - ZOWAWA! CHISOKONEZO! MANTHA A AKURU! Kuposera zaka 1900 zapitazo, Yesu anapereka za ulosi wa khalidwe la moyo wakale ngati wotengedwa mu nkhani za madzulo:- "Ndipo kudzakhala ZIZINDIKIRO pa dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi padziko lapansi CHISAUKO CHA MTUNDU WA ANTHU, ALI NKUTHEDWA NZERU pa mkokomo wa nyanja ndi mafunde ache, ANTHU AKUKOMOKA NDI MANTHA, NDI KUYEMBEKEZERA ZINTHU ZIRI NKUDZA KU DZIKO LAPANSI; pakuti mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka. NDIPO PAMENEPO ADZAAONA MWANA WAMUNTHU ALINKUDZA mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemelero waukuru. Koma poyamba kuchitika izi, weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiomboledwe chanu chayandikira." - Luka 21:25-28. Palibe dongosolo linanso lomwe likanatha kulembedwa la dziko lapansi la lero loposa loti. "Amuna adzakomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza pa dziko lino." Zida zambiri zosonkhanitsidwa zitha kuononga dziko lapansi. Nanga kuli bwanji kuti achifwamba atsogolere nkhondo yomenyera zida zamankhwala owopsa. Yesu akutipatsa ife chiyambi cheni-cheni cha chiyembekezo mu nthawi ya matsoka ngati imeneyi. Nthawi yadziko imeneyi "ya chisauko ndi kuthedwa nzeru" zikungochitira umboni kuti kudzadi kwa Khristu "kwayandikira kwambiri." Anthu masiku ano akhudzidwa m'madandaulo, akukhumudwa. "Taonani m'mene dziko liliri tsopano! Koma ophunzira a ulosi wa mu Baibulo atha kufuula ndi mau a chiyembekezo, "Taonani Iye amene akubwera kudziko lapansi." CHIKWANGWANI CHACHIWIRI - MATSOKA A M'DZIKO Kodi zochitika zoononga zinthu m'dziko zikugwirizana bwanji ndi masiku otsiriza? "Ndipo kudzakhala zivomezi zazikuru, ndi njala ndi miliri m'malo akuti akuti, ndipo kudzakhala zoopsya ndi zizindikiro zakumwamba pakuona zinthu izi ziri kuchitika, zindikirani kuti ufumu wa Mulungu uli pafupi." - Luka 21:11, 31. Tangoganizani za njala kwa kanthawi. Zithunzi-thunzi za ana omwe akufa ndi njala, mimba zawo zitalowa mkati. Sizozizwitsa kuona kuti anthu a nzeru zopitira kumwezi akusowa nzeru zodyetsera anthu onse? Yesu anadziwa kuti njala idzapitilira ndi kuti anthu odzikonda okha adzapitilira kutero munthawi ya kumapeto kwa dziko. Nanga bwanji za zibvomezi? Monga mwa kulemba kwa World Almanac" mu chaka cha 1999, akunena kuti nthawi ya zaka 100 ziri zonse ya nyengo yakukhala akhristu, kwakhala kukuchitika zivomezi zikuru-zikuru: Mu zaka za zana chikwi ndi mphambu zisanu ndi zitatu (18th century), kunachitika zivomezi zisanu ndi chimodzi; muzaka zina za zana lotsatira apa (19th century) munachitika zivomerezi zisanu ndi ziwiri; ndipo m'zaka zina zana zotsatirazo (20th century), munachitika zivomezi zoposera zana limodzi. Choncho umboni wa izi ukunka nukula pamene tikufika m'masiku athu ano. Chiwerengerochi chikukwaniritsa ulosi wa Yesu. Njala ndi zivomezi zazikulu zikufika pa chikati chawo cheni-cheni. "Ufumu wa Mulungu wayandikira." Kodi nanga m'badwo wathu uno udzabweretsa mazana ambiri a zivomezi zazikuru kapena kubwera kumene kwa Mfumu ya Mafumu? CHIKWANGWANI CHACHITATU - KUCHULUKA KWA CHUMA. Kodi zitanthauzanji tikati chuma chidzakhala ndi anthu ochepa pamene ambiri adzakhala mu umphawi woopya. "Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza." - Yakobo 5:3. Ngakhale dziko lonse lapansi liri pa vuto lachuma, olemera akunka nalemelerabe pamene osauka akunka nawonso nasaukirabe. Mipikisano ya mwayi ya ndalama zambiri yomwe imachitika irinso zizindikiro zotionetsera ife kuti "kudza kwa Ambuye kwayandikira." (vesi 8). CHIKWANGWANI CHACHINAYI - KUSAKHUTITSIDWA PANTCHITO Ndichifukwa chiyani kusakwanitsidwa ndi kuukira pa ntchito kwakula mofulumira kwambiri? "Taonani; mphotho ya antchitowo anasenga m'minda yanu yozunguliridwa ndi inu powanyenga, ifuula, NDIPO MAFUULO A OSENGAWO (ANTCHITO) adalowa m'makutu a Mbuye wa Makamu. Lezani mitima inunso, limbitsani mitima yanu, pakuti kudza kwake kwa Ambuye kuyandikira." - Yakobo 5:4, 8. Atalosera za kudzikundikira chuma kwa mu nthawi yathu ino, Yakobo anaoneratu kusakhutira pa ntchito pakati pa olembedwa chifukwa chosakhutitsidwa. Chizindikiro chinanso choti "Yesu Ambuye ali pafupi kudza" ndicho kusagwirizana ndi kukokana-kokana pakati pa osauka ndi olemela. CHIKWANGWANI CHA CHISANU - KUSWEKA KWA CHIKHALIDWE Ndichifukwa chiyani chikhalidwe cha umunthu mudziko chikuoneka kuti chikuonongekerabe? "Koma zindikirani ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma, olimbilira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu osati okonda Mulungu; akukhala nawo maonekedwe a chipembedzo koma mphamvu yache adaikana Koma anthu oipa ndi onyenga adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa." - 2 Timoteo 3:1-5, 13. Kodi winanso angayembekeze dongosolo lina loposa apa? Lozetsani makina ojambula kulikonse padziko lino masiku ano ndipo mujambuleko zambiri. Mupezanso zambiri zovuta kudzimvetsa zokhudza kuzunza ana. Mupezanso zochita za ana zambiri zosathandizika, kupha ndi kuphana mwachisawawa ali ndi zaka zochepa. Zonsezi zikutipatsa chithunzi-thunzi choonetseratu poyera kuti kudza kwa Yesu kwayandikira. CHIKWANGWANI CHACHISANU NDI CHIMODZI - KUFALIKIRA KWA MATSENGA Kodi ndi chifukwa chiyani kukhulupilira matsenga kwakula modabwitsa? "Chifukwa akhristu onama adzakula, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikuru ndi zozizwa kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka osankhidwa omwe." - Mateyu 24:24. Ndime izi zikulosera kuti munthawi yakumapeto kudzaonekera zozizwa ndi zizindikiro zambiri zoonetsera ngati zochokera kumphamvu yodabwitsayo. Mfiti ndi anyanga adzaonekera paliponse, kugulitsa zithumwa zawo, kulumikizana polankhula ndi mizimu. Zizindikiro zofanana ngati zoona ndi zozwizwa zidzauka. Zonsezi zikuchitikira umboni monga Khristu analosera, kuti, tikukhala mu nthawi ya "kudza kwa mwana wa munthu." (vesi 27). CHIKWANGWANI CHA CHISANU NDI CHIWIRI - KUDZIDZIMUTSIKA KWA DZIKO Kodi zikutanthauzanji tikati kudzidzimutsika kwa kudziko - kutsitsimuka kwa Africa, kwa maiko a kum'mawa, pakati kum'mawa kwa Ulaya ndi maiko a kutali uko kum'mawa? "AGALAMUKE AMITUNDU; Longani zenga, pakuti dzinthu dzacha Pakuti zoipa zao nzazikuru. Aunyinji, aunyinji m'chigwa chotsiriza mlandu! Pakuti layandikira TSIKU LA YEHOVA M'chigwa chotsiriza mlandu." - Yoweri 3:12-13. Lero ku Asiya ndi ku Afrika, kum'mawa kwa Ulaya ndi komwe kale kumatchedwa Soviet Union, komanso maiko a pakati ku m'mawa, tonse tikuchitira umboni izi za kudzidzimutsika kwa maiko aliwonse paokha-paokha zonse monga mwa ndondomeko ya momwe mbiri yakale ikunenera, "pakuti tsiku la Ambuye layandikira." CHIKWANGWANI CHA CHISANU NDI CHITATU - ZILINGANIZO ZA MTENDERE NDI KUKONZEKERA NKHONDO Tikukhala ife m'dziko la chilendo. Aliyense akuvomereza kuti payenera pabwere mtendere. Timanena za mtendere; koma ziwawa zilipo zambiri ndipo zinayamba kale-kale. Aneneri monga Mika ndi Yoweri analosera kuti munthawi yomwe maiko adzakambirana za mtendere (Mika 4:-31), kusakhulupilirana kwa maiko kudzabuka koma kudzanso nkhondo pakati pa maiko oyandikana (Yoweri 3:9-13). Kalelo Baibulo limaonetsera momwe dziko latsopanoli lomwe tikukhalali lidzakhalira lofuna mtendere - komanso lankhondo, ndikuonetsa kuti mtendere sudzatheka mpaka pamene Yesu adzabwere. CHIKWANGWANI CHA CHISANU NDI CHINAYI - KUCHULUKA KWA NZERU Ndichifukwa chiyani, patatha zaka zambiri mumbiri ya dziko lapansi, kuti mtenga-tenga ndi mtokoma kwapangitsa ngati maiko ali pafupi-pafupi? "MPAKA NTHAWI YA CHIMALIZIRO; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka." - Daniel 12:4. Apa Daniel akusonyezera kuti nzeru za ulosi wake zidzachuluka "mu" kapena "mpaka nthawi ya kumapeto." Koma ulosiwu ukulozeranso chindunji cha nthawi yathu ino ya makina a kompyuta. Nzeru za mtundu wina uli wonse zapita pa tsogolo mwa kuthwanima kwa mphezi m'zaka zochepa zokha zapitazo. Kwakhala kusintha kwakukuru mzaka makumi asanu okha zomwe zapitazo, poyelekeza ndi kusintha komwe kwachitika mu zaka zikwi zikwi zapitazo. "AMBIRI ADZAPITA UKU NDI UKO, kuonjezera nzeru." Chisanafike chaka cha 1850, anthu ankayenda pa ngamira, ndi a bulu ndi nyama zina zomwe anali nazo pa nthawi yawo kuyambira pachiyambi. Koma lero, maulendo akuyendedwa pa ndege zikulu-zikulu mu mlenga-lenga. Kuchuluka kwa maulendo ndi kusefukira kwa kufufuza mwaukatswiri kutipatsa umboni wokwaniritsa kuti tiri kukhala mu "nthawi ya kumapeto." CHIKWANGWANI CHA CHIKHUMI - UTHENGA WABWINO KUDZIKO LONSE LAPANSI Yesu analosera kuti atangotsala pang'ono kuti akubweranso, uthenga wabwino udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi. "Ndipo uthenga uwu wabwino waufumu, udzalalikidwa pa dziko lonse la pansi, ukhale umboni kwa anthu amitundu yonse ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro." - Mateyu 24:14. Kwa zaka zambiri, pafupi-fupi theka la dziko lapansi linatsekeredwa mu mdima, kutari ndi uthenga wabwino. Koma ndithu mwadzidzidzi mukanthawi kochepa, kum'mawa kwa Ulaya kunacha kumasulidwa kwa nsinga za komyunisiti. Khoma la Berlin linanka ligwa ndi ufumu wake unayamba kugawanika mwadzidzidzi pafupi-fupi theka ladziko lapansi linatambasuka m'manja kulandira uthenga wabwino. Uthenga wabwinowu ukupitadi "kudziko lonse lapansi" kuposa momwe sunachitikirenso. Kupyolera pa Kanema, uthenga ukufalitsidwa pafupi-fupi dziko liri lonse. Tikukhala m'masiku awodi omwe Yesu ananena m'mene anati: "Uthenga uwu wabwino udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi" ndipo "pamenepo chimaliziro chidzafika." 2. KODI PAYANDIKIRA BWANJI PAKUDZA PACHE PA YESU Atatha kulongosola zochitika zomwe zidzaonetsere kudzanso kwake, Yesu anamaliza ndi mau oti: "Indetu ndinena kwa inu, m'badwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa." - Mateyu 24:34. Kumalizaku nkodziwikiratu - m'badwo womwe ukunenedwa ndi zizindikirozi za ulosi udzaona Yesu akubweranso kachiwiri ku dziko lapansi. Sipadzakhalitsa, ndipo adzachotsa tchimo lonse, ndi kuzunzika konse, ndikukhazikitsa ufumu wake wamuyaya. Yesu akuchenjeza, "palibe aliyense yemwe adziwa tsikulo kapena nthawi yake - (vesi 36). Ndipo Yesu akupitiliza kunena kuti: "Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa mu nthawi imene simuganizira, Mwana wamunthu adzadza." - Mateyu 24:44. 3. YESU, CHIYEMBEKEZO CHOKHALA CHA DZIKO LAPANSI Yesu ndiye chiyembekezo chomaliza chopambana ku dziko lathuli lapansi, chifukwa ndi Iye yekha yemwe angaononge tchimo lomwe lasautsa dziko lapansi. Yesu anafa pa Karavali kuti kukakhale kotheka kugonjetsa choipa ndi kumasula onse amene avomera chipulumutso chomwe Iye wachipereka. "Iye wochita tchimo ali wochokera mwa m'dierekezi, chifukwa m'dierekezi anachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za m'dierekezi." - 1 Yohane 3:8. Mpulumutsi wathu anakonza njira kuti dziko likamasukire podzipereka thupi lake lomwe ndi mwazi wake nsembe, Ndipo Yesu yemweyo, yemwe tsiku lina adzachiritsa dziko lonse ku tchimo ndi zotsatira zake, akuperekanso mwayi wochiritsa miyoyo yathu ya tchimolo. Simuyenera inu kudikira kuti abwerenso kachiwiri kuti muyeretsedwe ku tchimo, kapena kuti musiye makhalidwe achionongeko ayi. Yesu ali wolola kukupatsani mtendere wake pompano. Msungwana wina wake, ankachita nawo msonkhano wauzimu. Anakhudzidwa ndi uthenga womwe umalalikidwawo. Pamene anamva nthano ya kubweranso kwachiwiri kwa Mpulumutsi ikuvumbulutsidwa, anaona kuti zizindikiro zonse zikugwirizana. Anaona kuti zikupanga zinthu kukhala zomveka bwino. Kenaka adapeza kuti iye ankafuna-funa chikondi, kukondwa ndi mtendere ku malo olakwika. Yesu ndi wolola kutipatsa mtendere pompano. Tsiku linzakelo pamene wolalikirayo ndi gulu lake adamuyendera, adawauza bwino lomwe za moyo wake wosautsa umene adakhala nawo. Anawauza kuti adali chidakwa, ndipo ankachita zachiwere-were kuti apeze zosowa zake. Atatha kulongosola mavuto ake adayamba kukhetsa misozi, nanena, 'usiku uja mumalalika za m'mene ine ndiriri ndithu." Koma mawu omwe adamukhudza iye adali mawu a Mulungu, ndipo amamuyankhula mofatsa. Ndipo iye adafika poganiza zosiya zonse namuitana Khristu kulowa mumtima mwake monga Ambuye ndi Mpulumutsi wake, nagwiritsitsa ku chiyembekezo cha kubweranso kwachiwiri kwa Yesu Khristuyo. Mu masabata otsatira apo,iye adayamba kuona kuti mantha ndi kusowa chitetezo kwake kwakukulu komwe amakubisalira mukuledzera, kunamasulidwa pamene nthawi yambiri tsopano ankalumikizana ndi Yesu. Yesuyo adayamba kumumasula iye kuzonse zomwe zimasautsa moyo wake. Adachita iye zambiri zomwe sanathe kuti angazinyadire koma chifundo ndi chisomo komanso chikhulupiliro cha Khrisu chinaonetsera mphamvu zazikuru koposera manyazi ake. Omwe adaona mbava ya pamtanda zinali ndi tanthauzo lalikuru kwa iye. Mu nthawi yake yazowawa yakumapeto, adatembenukira kwa wolangidwa wosalakwayo yemwe anali pambali pake napempha, "Yesu, mundikumbukire ine pamene mudzadza mu ufumu wanu" (Luka 23:42). Yesu anamuyankha pomwepo namulonjeza iye malo kukhala naye ku Paradizo (Vesi 43). Yesu yemweyo anakhululukira mwa chisomo kwa mbava ija yomwe inafa, akuperekanso tsopano kwa inu chipulumutso, kukhulukira konse,ndi mtendere mumtima. Dzipezereni inu nokha lero zinthu zimenezi. Inunso mungathe kupemphera ngati mbava yophedwa pamtanda ija kuti: "Yesu, mundikumbukire ine pamene mudzadza mu ufumu wanu." Ndipo Yesu adzayankha, "Ndidzabweranso, ndipo udzakhala ndi Ine ku Paradizo."
© 2003 The
Voice of Prophecy Radio Broadcast |
|