YESU AKADZABWERERA INU Patatha zaka zambiri zankhanza, Armando Vallades anaonda, kungokhala ngati chithunzi cha momwe analiri kale. Amagwira ukaidi wa zaka makumi atatu mu imodzi ya ndende za Castro chifukwa chopezeka akupemphera m'chalichi pa tsiku la Khrisimasi. Oyang'anira ndende anamukhazika ndi njala, kumuzunza ndi kumunyoza komabe sanalole kusiya chikhulupiriro chake. China chake chinampanga iye kupitabe chitsogolo: lonjezo lomwe anapanga kwa msungwana wina wotchedwa Martha. Anakomana nafunsirana ubwenzi iye adakali m'ndende. Msungwanayu anakhudzidwa kwambiri ndi chikhulupiriro cha Armadochi. Atakwatitsidwa m'ndende momwemo pa mwambo womwe unachitikira mchipinda china momwemo, Martha anakakamizika kupita ku Miami. Kulekana kwawo kunali kowawa. Koma Armando anayesetsa kumulonjeza wokondedwa wake polemba, pakapepala kosaoneka bwino kotayidwa pomwe analembapo lonjezano lake lakuti: "Ndidzabwera kwa iwe, ngakhale mavuto adzachulike sindidzawasamala ayi." Wam'ndendeyu anatsimikiza kuti tsiku lina iye ndi Martha adzapanga malumbiro awa a ukwati mu kachisi wa Mulungu pamaso pa Mulungu. Tsiku lina kulumikizana kwawo kudzakhala kwathunthu. "Uli ndi ine nthawi zonse." Anamuuza choncho msungwanayo. Lonjezoli, zinapangitsa Armando kupitirirabe chitsogolo kupyola zaka zonse zozunzidwa zidakampangitsa munthu aliyense kutaya mzimu wake. Ndipo zinampangitsa Martha kupita chitsogolo. Anayesetsa kuwadziwitsa anthu poyera mosatopa zacholinga cha mwamuna wake. Sanataye chiyembekezo chake. 1. LONJEZANO Nthawi zina ungayesedwe kuzizwa kuti kodi Khristu adzatsikadi tsiku lina kuchoka kumwambaku kudzalumikizananso nafe? Modabwitsa talekanitsidwa ndi Iye kwa nthawi yaitali tsopano. Kathedwe kabwino kotere mbiri yaitali, yoopsa ya dziko lapansi kudzaoneka yabwino kwambiri kukhala yoona. Koma pali chinthu chimodzi chomwe chingasunge chikhulupiriro chathu kukhalabe chamoyo m'mitima yathu. Ichi ndicho lonjezano lake la Yesu kuti adzabweranso. Yesu asanachoke kwa ophunzira ake kupita kumwamba, anawalonjeza. "Mtima wanu usabvutike, mukhulupirira Mulungu, Khulupirirani inenso. M'nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri. Ngati sikudali kotero ndikadakuuzani inu; pakuti ndipita kukakukonzerani inu malo, ndipo ngati ndipita kukakukonzerani inu malo NDIDZABWERANSO, ndipo ndidzalandira inu kwa ine ndekha; kuti kumene kuli ineko, mukakhale inunso." - 1 Yohane 14:1-3. Yesu asanakwere kunka kumwamba, anawatsimikizira ophunzira ake, 'Ndidzabweranso!' anawalonjeza kudzawatenga onse omukhulupirira iye kunka nawo ku malo apadera omwe watikonzera. Mawu a Mulungu akunena za kubwera kwake kwa chiwiri pafupifupi nthawi zikwi ziwiri mazana asanu (2,500 times). Nkhani yoti Yesu akubweranso kachiwiri ku dziko lapansi ndi yoona ngati momwe anakhaliradi padziko lapansi zaka zikwi ziwiri zapitazo. M'mbuyomo Mulungu analonjeza za kudza kwa Mesiya, wotimasula yemwe akadadzitengera pa Iye yekha mphulupulu machimo athu ndikutipatsa chikhululukiro cha tchimo la anthu. Lonjezolo lidaoneka labwino kulikhulupirira kwa anthu ambiri m'nthawi yakaleyo omwe anavutika m'moyo wawo. Koma Yesu anabweradi nafa pa mtanda. Lonjezano lija linakwaniritsidwa mokondweretsa koposa momwe anthu amaganizira. Lonjezo lake lakubweranso lidzakwaniritsidwa. Tingathe kudalira pa Iye wotikondayo, kuti adzabwera ndi kusonkhanitsa iwo womwe Iye adawalipirira mtengo wapatali . Kupyolera mu undende wake wonse, Armarndo anapitirira kulemba ndakatulo, mauthenga ndi zojambula kwa Martha mozembetsa. Ndipo msungwanayu anazisindikizitsa zolembedwazi. Luso ndi uthenga wa zolembadwazi zinachititsa chidwi padziko. Maboma anayamba kuumiriza Castro kuti atulutse andende achikumbumtima. Purezidenti wa Faransa analowereraponso ndipo pamapeto pake m;chaka cha 1982 Armando anatulutsidwa natumizidwa ku Parisi pa ndege. Zinamuvuta kukhulupirira kuti ali mfulu tsopano ngakhale pamene ndege yomwe anakwera inatera. Koma tsopano patatha zaka makumi awiri akuzunzika, ndi kudikirira,ndi kukhumba, Amarndo anathamangira napezekanso m'manja a Martha. Patapita miyezi yochepa, anthu awiriwa ali wokondwa anaima pamaso pa mpingo wa St Kiera ku Miami kupanga malumbiro awo a ukwati. Kulunzanitsidwa kwawo kunatheka tsopano. Lonjezano linakwaniritsidwa. "Ndidzabweranso kwa iwe." Kodi
mungathe inu kuganizira chisangalalo chomwe chidzakhale panthawiyi yolumikizanayi
pamene tidzamuona Yesu Khristu wathu maso ndi maso? Kuonekera kwake
kwa ulemerero kudzakwirira zisoni ndi zokhumudwitsa zathu zonse, kudzapukuta
zowawa zomwe zakhala zobisika m'mitima yathu. Kubweranso kwa Yesu kudzakwaniritsa
khumbo lathu ndi chiyembekezo chathu cha pansi pa mtima. Ndipo tidzakhala
pa mgwirizano wosatha ndi munthu wozizwitsa wa dziko lonse. 2. YESU ADZABWERA BWANJI (1)
Kodi Yesu adzabwera mwa chinsinsi? (2)
Kodi Yesu adzabweranso ngati munthu weniweni? Patsiku lake lonyamuka kuchoka pa dziko lathuli angelo anawatsimikizira ophunzira kuti, "Yesu yemweyo" watengedwa kukwera kumwamba osati wina ayi - adzabweranso yekha ngati mfumu ya mafumu. Yesu yemwe anachiritsa odwala ndi kupenyetsa akhungu. Yesu yemweyo adalankhula mofatsa kwa mayi wogwidwa m'chigololo. Yesu yemweyo yemwe adapukuta misozi ya wolira nalandira ana m'chifukato chake. Yesu yemwe adafa pa mtanda wa Karavali, napuma m'manda naukanso kwa akufa pa tsiku lachitatu. (3)
Kodi Yesu adzabwera moti tidzamuona? Onse
amoyo pamene Yesu adzabweranso, olungama ndi ochimwa omwe pamodzi, adzachitira
umboni kudza kwake. Kodi Yesu adanena kuti ndi anthu angati omwe adzaone
kudza kwake? "Ndipo
pomwepo padzaoneka m'thambo chizindikiro cha mwana wa munthu; ndipo
mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pa chifuwa, nidzapenya
mwana wa munthu alinkudza pa mitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemelero
waukuru." - Mateyu 24:30. Munthu aliyense, munthu wamoyo padziko lathuli lapansi adzaona Yesu akubweranso. (4)
Kodi omwe adzabwere naye Yesu pamodzi ndani? (5)
Tingathe ife kuneneratu nthawi yeniyeni yomwe Yesu adzabwerere? Aliyense adzaona Yesu ndi kufika kwake kwa ulemelero. Koma ambiri adzakhala asanakonzekere. Inu mwakonzekera panokha kuti Yesu abwere? 3. KODI YESU ADZACHITA CHIYANI AKADZABWERANSO (1)
Yesu adzasonkhanitsa opulumutsidwa (osankhika) onse Pamodzi. (2)
Yesu adzaukitsa akufa olungama. (3) Yesu adzasintha oyera onse pakubweranso kwake - osati akufa olungama okha ayi, koma ngakhalenso olungama amoyo. "Pamenepo
ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo
kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye
nthawi zonse." - 1 Atesalonika 4:17. Potikonzetsera
ife moyo muyaya, Yesu akusintha matupi athu a kufawa kuwapanga okongola
ndi wosafa. "Taonani ndikuuzani chinsinsi; sitidzagona tonse, koma tonse tidzasandulika, m'kamphindi, m'kuthwanima kwa diso, pa LIPENGA LOTSIRIZA; ndipo ife TIDZASANDULIKA. Pakuti chovunda ichi chiyenera kuvala chisavundi, ndi cha imfa ichi kuvala chosafa." - 1 Akorinto 15:51-53. Yesu podzabwera tonse tidzasinthika. Tangoganizani kopandanso kufa ziwalo, kopanda matenda. Zipatala kutsekedwa ndi malo osungira maliro kutsekedwa. Khristu wabwera! (4)
Yesu adzatenga olungama onse kupita nawo Kumwamba. (5)
Yesu adzathetsa choipa ndi masautso onse kunthawi zonse. Akudziwa kuti mawu amene akufuula ndi omwe aja adawaitana iwo nthawi ina kuti alandira chisomo chake. Iwo amene adaziipsa ndi chuma ndi zokondweretsa za moyo, kapena maudindo tsopano adziwa kuti anakana chinthu chokhacho chopambana m'moyo. Ndi chibvumbulutso chopweteka. Komatu palibe ndi mmodzi yemwe anayenera kutaika. Mulungu mwini "Sakondwera nayo imfa ya ochimwa" (Ezakiel 33:11). Iye, safuna kuti wina akaonongeke, koma kuti adze ku kulapa (2 Petro 3:9). Yesu akutidandaulira ife, "Idzani kuno inu nonse akulema ndi akuthodwa, ndipo ndidzakupumulitsani" (Mateyu 11:28). Koma chodabwitsa ndi chomvetsa chisoni, ena amakana kuitanira kwake kwa chisomo. 4. KODI INU MWAKONZEKA PAKUBWERA YESU Zinamutengera Yesu mtengo waukulu kutipatsa ife tsogolo la ulemelero ndi iye. "M'nyumba ya Atate anga." Zinamutengera moyo wake! "Kotero KHRISTUNSO ATAPEREKEDWA NSEMBE KAMODZI, ku kasenza machimo a anthu ambiri, adzaonekera pa nthawi yachiwiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amulandira kufikira chipulumutso." - Ahebri 9:28. Mpulunutsi yemwe anafa pa mtanda kuchotsa machimo ako adzaonekera kachiwiri ndipo adzabweretsa chipulumutso kwa iwo omwe akumuyembekezera. Yesu anadzipereka yekha nsembe ndicholinga chotipatsa aliyense wa ife chipulumutso. Koma popanda kubweranso kachiwiri, ntchito ya mtanda ikanakhala yopanda pake. Khristu akufuna kutipatsa ife kwathu kwamuyaya ndi kotetezedwa ndi Iye, kuti izi zitheke, tiyenera ife kumulola Iye kulamulira mitima yathu ngati mpulumutsi ndi Ambuye kuyambira tsopano. M'mawa wa pa August 16, 1945, mwana wina wam'ngono anathamanga kudutsa nyumba za a Shantung kumpoto kwa dziko la China akufuula kuti waona ndege mlengalenga. Onse amene anali ndi mphamvu pa mudzipo anatuluka panja nayang'ana kumwamba. Anthuwatu anali atakhala zaka zambiri mosalidwa, kukanidwa ndi kumanidwa, ndi chikhumbokhumbo, andende omwe anasungidwa ndi dziko la Japani ngati akaidi am'maiko odana nawo. Kwambiri chinthu chimodzi chokha, chomwe chinawapanga kukhalabe amoyo muuzimu, ndicho chiyembekezo chakuti tsiku lina nkhondoyi idzatha. Nyesi ya magetsi inawadutsa gulu la anthu chikwi ndi mazana asanu am'ndende omwe anali ndi moyobe. Pamene anazindikira kuti nkutheka ndegeyo imadzera iwo. Pamene phokoso la ndegeyo linakulirakulirabe, wina wa iwo anafuula, "TAONANI, pandegeyo pali mbendera ya dziko la AMERIKA! Yopetedwa mmbali mwake akutikwezela mikono Akutidziwa, akubwera kudzatitenga." Panthawiyi chisangalalo chimakulirakulirabe koposa mwa anthu ovutika ofooka, ofuna kwawo wa. Chisokonekero chachikuru chinabuka. Anthu ankathamanga mutimagulu mozungulira, akufuula mokweza ndi manja awo m'mwamba ndi kulira. Mwadzidzidzi kunagwa bata pa gululi pamene onse anapenya kunsi kwa ndegeyi kukutseguka ndipo anthu akutsika mundegeyo pogwiritsa ntchito matumba otsikira ndege idakali m'mwamba aja. Owapulumutsa awo samangobwera kokha tsiku lina ayi, amabwera lero, PANOPA kuti akhale pakati pawo. Gululi linakhamukira kuchipata cha mudziwo. Palibe anaganiziranso za mfuti zoopsa zomwe zinawaloza kuchokera pa chinyumba chachitali cha owayang'anila ayi. Atakhala zaka zambiri zogwetsedwa mphwayi, kusowa abwenzi, anaswa chipatacho nathamangira komwe owapulumutsawa amatera. Posakhalitsa anthuwa anatembenuka nalowanso mmudziwo atawanyamula asirikali owapulumutsa aja. Wolamulira ku malo awa anawapereka iwo wopanda nkhondo. Nkhondo inathadi. Ufulu unabwera. Dziko linakhalanso latsopano zedi. Posachedwa Mulungu wathu, nthano yaitali yoopsa ya munthu Mpulumutsi wathu, adzatsika kuchokera m'mitambo kudzatipulumutsa. Kuchitira nkhanza munthu nzake kudzatha. Kudzakhala kukondwa pa tsikuli, kufuula kwa chimwemwe podzamvetsetsa komaliza; akubwera pafupi; ndikutha kuona angelo akuimba malipenga awo." Mawu a lipenga akumveka mopfuula, kumwamba kukuwalirawalirabe, mpaka pamene sitingathe kupirira. Koma sitingasiye kuyang'ana pamenenso tizindikira; "Akundiona ine. Akundidziwa ine kuti ndine yani." Ndidzazindikira ndi chimwemwe chachikuru "Uyu ndi Mulungu wanga akudzera ine, osatinso tsiku lina, koma panopa, lero." Kodi mwakonzeka kudzamulandira mfumu mu ulemelero wake wonse? Ngati sichoncho, chonde, muitaneni Yesu panokha m'moyo mwanu tsopano lino. Monga kudza kwa Yesu kudzathetsa mavuto onse a padziko lapansi, kumulola iye kudza mumtima mwanu kudzakuthandizani kuthana nawo mavuto anu a tsiku ndi tsiku m'moyo uno. Uyu wamkulu wothetsa mavuto athu angakumasuleni inu ku chitsutso ndi katundu wa tchimo ndi kukupatsani moyo wosatha. Kubwera kwa Yesu m'moyo wa munthu kumasinthiratu kwakukuru ndi kwamuyaya, monga m'menenso kudza kwake kudzasinthire miyoyo yathu pa dziko lapansi. Inu mutha kumudalira Yesu. Adzakukonzetserani yekha pa zakubwera kwake ndi kukupatsani chitsimikizo chodabwitsa cha moyo wokondwa kwa muyaya.
© 2003 The
Voice of Prophecy Radio Broadcast |
|