ZA TSOGOLO LANU

Madotolo awa, Patricia ndi David Mrazeki anaona zoswetsa mtima zambiri mu ntchito yawo. Monga wotswirika pa nkhani ya matenda a ana, anachita ndi ana ambiri ovutika. Koma anazizwa poona kuti ana ena amachira pamene ena amapsinjika ndi mavuto amodzimodzi omwewo. Chifukwa chiyani? ndichifukwa chiyani ana ena mwachitsanzo, amamwa mankhwala osokoneza bongo pamene wina apita ku sukulu ya ukachenjede? Nanga bwanji ana ena ozunzidwa amakula nkudzakhalanso ozunza anzawo, pamene ena amadzakhala makolo abwino?

A Mrazeki awa anapanga kafukufuku wakuya kuti apeze mayankho a mafunsowa. Mu ku phunzira kwao khalidwe lina limapezeka mwa anawa omwe anadutsa muzoopsa zomwe anakumanapo nazo, koma nakhala ndi moyo wabwino ndi wathanzi. Chinsinsi chake chinali chiyani? "Mayang'anidwe abwino a moyo ndichiyembekezo."

Chiyembekezo chinabweretsa kusintha. Chiyembekezo, koposa zonse, chimathandiza ife kumenyana ndi kugonjetsa zovuta zomwe zakhala zikuzunza m'miyoyo yathu.

Anthu amafunitsitsa chiyembekezo. Koma nanga timachipeza bwanji? Chiyembekezo ndichovuta kuchipeza m'dziko lathu lapansili mpaka titayang'ana molunjika ku bukhu lopatulika ndi maulosi ake. Phunziro ili likutithandizanso kufufuza ulosi wopatsa chidwi umene watakasa anthu ambiri ndi chiyembekezo chakuya.

1. ULOSI WOZIZWITSA WA MU BAIBULO

Pafupifupi zaka mazana asanu asanabadwe Yesu Khristu, Mulungu anaonetsera za tsogolo la dziko kupyolera mwa mneneri Daniel.

Mulungu anaperekeratu ndondomeko ya mbiri ya dziko lapansi ya zaka zikwi ziwiri mazana asanu zamtsogolo, kuyambira mu nthawi ya Danieli mpaka nthawi yathu ino.

Ulosi uwu unachokera mu loto la mfumu Nebukadinezara, wa dziko la Babulo zaka zikwi ziwiri mazana asanu zapitazo. Lotoli linazunza mfumuyu koma sanathenso kulikumbukira ngakhale atadzuka! Anzeru onse a ku Babulo atalephera kuthandiza kumukumbutsa mfumuyu loto lake kuti limasuliridwe, Mu Heberi wang'ono wogwidwa ukapolo dzina lake Daniel anaonekera akulengeza kuti Mulungu wakumwamba angathe kuvumbuuitsa zinsinsi zonse.

Ataima pamaso pa mfumu, Daniel molimba mtima ananena! "Inu mfumu munapenya ndi kuona FANO LALIKURU Fanoli linali lalikuru, ndi kunyezimira kwache kunaposa; linali kuima popenyana ndi inu, ndi maonekedwe ache anali oposa. Fano ili tsono, mutu wache unali wagolidi wabwino, chifukwa chache ndi manja ache zasiliva, mimba yache ndi chiuno chache zamkuwa, miyendo yache yachitsulo, mapazi ache mwina chitsulo mwina dongo. Munali chipenyere kufikira mwala unasemedwa popanda manja, umene unagunda fanoli pa mapazi ache okhala chitsulo ndi dongo."

"Pamenepo chitsulo, dongo, mkuwa, siliva, ndi golidi, zinapereka pamodzi, nizisanduka ngati nungu wa pa madwale a malimwe; ndi mphepo inaziluza osapezekanso malo awo; ndi MWALA UDAGUNDA DZIKO LONSE LAPANSI." - Daniel 2:31-35.

Fano ili, poliona koyamba, lingathe kuoneka ngati liribe zambiri zokhudzana ndi chiyembekezo cha moyo wathu mu nthawi yathuyi koma khalani cheru muone.

2. ULOSI UMASULIRIDWA

Atatha kunena mwazonse zomwe analota mfumuzo mopanda kuchotsa kapena kuonjezera, mneneri Daniel analongosola motere:

"Ili ndi loto; kumasulira kwache tsono tikufotokozerani mfumu." - Daniel 2:36.

MUTU WA GOLIDI:
Kodi ndi ufumu uti wa dziko womwe Daniel adauza mfumu kuti ukuimiliridwa ndi mutu wa golidi.
"Inu mfumu ndinu mfumu ya mafumu, pakuti Mulungu wakumwamba anakupatsani ufumu, ndi mphamvu yaikuri, ndi ulemu... INU NDINU MUTUWO WAGOLIDI." - Daniel 2:37, 38.

Daniel amuuza wolamulira wa dziko dera lalikulu kwambiri ndi lamphamvu pa dziko lonse lapansi. "Nebukadinezara, Mulungu akukuuzani kuti ufumu wanuwu wa Babulo ukufanizidwa ndi mutu wa Golidi wafanolo".

CHIFUWA NDI MANJA ZA SILIVA
Mukuona kwa umunthu, zinali kuoneka kuti Babulo adzalamulira nthawi zonse. Koma kodi ulosi ukunena kuti chidzachitika ndi chiyani pambuyo pake?

"Ndipambuyo pa inu padzauka ufumu wina wochepa ndi wanu." - Daniel 2:39.

Pokwaniritsa ulosi wa Mulunguwu, ufumu wa Nebukadinezara unagonjetsedwa ndi ufumu wa a Medi ndi Apelezi motsogozedwa ndi mfumu Sairasi m'chaka cha 539 B.C. Choncho chifuwa ndi manja zasiliva zikuimira a Medi ndi a Perezi, ufumu winanso wamphamvu.

MIMBA NDI CHIUNO ZA MKUWA
Kodi mbali imeneyi ikuimira chiyani pa chifano chachikuluchi?

"Ndi ufumu wina wachitatu wamkuwa wakuchita ufumu pa dziko lonse lapansi." -
Daniel 2:39.

Mimba ndi chiuno zamkuwa zimaimira ufumu wa Chihelene womwe motsogozedwa ndi Alexander, anagonjetsa a Medi ndi a Perezi, kusandulika ufumu waukulu wachitatu padziko lonse lapansi womwe unalamulira kuyambira m'chaka cha 331 mpaka 168 BC.

MIYENDO YA CHITSULO
"Ndi ufumu wachinayi (anatero mneneri) udzakhala ngati chitsulo, popeza chitsulo chiphwanya ndi kufooketsa zonse; ndipo monga chitsulo chiswa zonsezi, uwu udzaphwanya ndi kuswa." - Daniel 2:40.

Atafa Alexander, ufumu wake unafooka ndikugawika m'magulu odana mpaka pamene, m'chaka cha 168 BC, pa nkhondo ya ku Pydna, "ufumu wa chitsulo" wa Roma una phwanya Ahelene.

Augustus Caesar (Kaisala) anali kulamulira ufumu wa boma pamene Yesu anabadwa pafupifupi zaka zikwi ziwiri zapitazo (Luka 2:1). Khristu ndi atumwi ake anakhala munthawi imeneyi ya ulamuliro woyimiridwa ndi miyendo ya chitsulo. Gibbon, wolemba wa mbiri yakale wa mu zaka za m'mazana khumi ndi asanu ndi mphambu zitatu (18th Century), analemba za nthawi imeneyi, popanda kukaika anali ndi ulosi Daniel mmaganizo pamene analemba kuti "Zifanizo za golidi, kapena siliva, kapena mkuwa, zomwe zimathandizira kuimirira maiko ndi mafumu awo, anaphwanyidwadi ndi ufumu wa chitsulo wa Roma. Edward Gibbon. Mbiri ya kugwa ndi kudzukanso kwa ufumu wa Roma, tsamba 89, vol. 4 (John D. Morris and company).

Taganizirani inu kwa kamphindi za ulosiwu mwa umunthu Daniel akanatha bwanji kukhala ndi m'ndandanda wa maufumu anayi akutsogolo molondola pamene iye anali kukhala munthawi ya ufumu woyambirirawo wa Baibulo? Tiri ndi vuto lodziwa za momwe malonda akhalire Sabata yamawa! Koma Babulo, Medi ndi Perezi, Aherene, ndi Roma anakhaladi maufumu otsatana kulamulira monga mmene ulosi unaliri ngati ana omvera a sukulu pamzere.

Kodi Mulungu akulamulira pa za mtsogolo? Tingakhale ndi chiyembekezo pa chikonzero chake? Yankho ndi loti, "Eya."

MAPAZI NDI ZALA ZA DONGO KUSAKANIZANA NDI CHITSULO
Kodi ufumu wachisanu udzabwera pambuyo pa ufumuwu wa Roma?

"Ndipo umo mudaonera mapazi ndi zala zache, mwina dongo la woumba, mwina chitsulo, UFUMUWU UDZAKHALA WOGAWANIKANA; Koma momwemo mudzakhala mphamvu ya chitsulo; popeza mudaona chitsulo cosanganizika ndi dongo ndi zala za mapazi, mwina chitsulo ndi mwina dongo, momwemo ufumuwo mwina wolimba mwina wogamphuka." - Daniel 2:41, 42.

Mneneri analosera, osati ufumu wachisanu wa dziko, koma kugawikana kwa ufumu wa chitsulo wa Roma. Roma ayenera kuthyoka nkupangika timaufumu tina khumi ting'onoting'ono, tomwe tiimiriridwa ndi mapazi ndi zala za kumapazi za chifanocho.

Kodi izi zidachitikadi? Inde zinachitika. Mu zaka za zana lachinayi ndi la chisanu za mbiri ya Chikhristu, anthu ankhanza ochokera ku mpoto anadzasokoneza Roma yemwe anataya mphamvu yake, namugonjetsa pompatsa mavuto ndi nkhondo yomugonjetsa pafupi pafupi. Posakhalitsa Madera khumi amitundu ya mu ufumuwo anapeza nawo ulamuliro wa mbali zina za kumadzulo kwa Roma, ndi maboma khumi anakhala odziimira paokha mmalire a Ulaya. Izi ndizo zimene zala khumi zikuimirira, maiko atsopano khumi a ku Ulaya lero.

3. TSIKU LATHU MU ULOSI

Kodi ulosi wa Danieli ukuonetsa kuti kuyesa kudzachitika masiku athu ano mu ulosi kogwirizanitsa maiko a ku ulayawa pansi pa mtsogoleri mmodzi?

"Ndi umo mudaonera chitsulo chosanganiza ndi dongo, iwo adzadzisokoneza ndi ana a anthu wamba; koma SADZAPHATIKIZANA, monga umo chitsulo sichimasanganizika ndi dongo." - Daniel 2:43.

Nthawi ndi nthawi, amuna amphamvu ayesetsa kugwirizanitsa maiko a ku Ulaya, koma nthawi zonsezi alephera. Napoliyoni anakhala ngati angathe kuposa ena onse, koma mwina poganizira za ulosiwu, pomwe ankathawa atagonjetsedwa ku nkhondo ya ku Waterloo, analira, "Mulungu wamphamvu zonse wandikulira."

Kaiser Wilhelm wachiwiri ndi Adolf Hitler anadza ndimagulu ankhondo oopsa ndi amphamvu kwambiri pa nthawi yawo. Koma aliyense analephera kugwirizanitsa maiko a ku Ulaya pansi pa utsogoleri wawo. Nanga ndi chifukwa chiyani? Ndichifukwa choti mawu a Mulungu anali kukwaniritsidwa. "Anthu adzasanganikira ndipo sadzagwirizanitsika." Zotsatira zake za nkhondo zonse ziwiri za dziko lonse lapansi zotsimikizira kuti Mulungu amagwiriziza tsogolo la dziko lapansi m'dzanja lake; Iye ndiye amene akulamulira zonse. Izi ndi zokwana kutipatsa ife chiyembekezo, mtendere wa mumtima, ndi kulimba mtima mu chikonzero chake pa miyoyo yathu.

4. KUONANSO ZA KUTSOGOLO

Mbali imodzi yokha ya ulosi wa Daniel ndi yomwe siinakwaniritsidwe. Kodi tanthauzo la mwala umene ukuphwanya fanoli kumapazi, napela fanolo, nusandulika phiri lalikulo lodzaza pa dziko lonse, ndi chiyani?

"NDIPO MASIKU A MAFUMU AJA (MAIKO ATSOPANO AKU ULAYA), MULUNGU WA KUMWAMBA ADZAIKA UFUMU woti sudzaonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wace sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse. NDIDZAKHALA CHIKHALIRE." - Daniel 2:44.

"Mafumu aja" angalozere maufumu okhawo a mapazi ndi zala za fanolo - Atsogoleri a maiko atsopano a ku ulaya, kulozera kunthawi yathu ino ya lero. Mwala umene unapangidwa wopanda manja uli kufuna kuphwanya fano ndi kuliswa kulipera, ndipo iwo udzadzaza dziko lonse lapansi (ndime ya 34, 35, 45). Posachedwa Yesu atsika kuchokera kumwamba "Kudzakhazikitsa Ufumu," Ufumu wake wa chisangalalo ndi mtendere. Pomwepo, Khristu, thanthwe la mibadwo ndi mfumu ya mafumu, adzalamulira dziko lapansi kwa muyaya!

Chirichonse cha mu ulosi wa Daniel 2 chachitika kupatulapo mwalawu kuphwanya fanoli. Mchikonzero cha nthawi ya Mulungu, tatsala pang'ono kufika pa mapeto penipeni, kuti Yesu abwere padziko lapansi. Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, ali pafupi kutsiriza kulimbana kwamwazi komwe kwatenga nthawi yaitali mu mbiri ya munthu ndi kudzakhazikitsa ufumu wosatha wa chikondi ndi chisomo.

5. LOTO LA MFUMU NDI INU

Ulosi uwu ukuulula dzanja lotsogolera la Mulungu mu nthawi ya kudza ndi kugwa kwa mafuko. Mulungu amadziwa zammbuyo, ndipo ulosi uwu wa m'Baibulo ukuonetsera poyera kuti Iye akudziwanso zam'tsogolo.

Ngati Mulungu amatsogolera mmene maufumu akuyendera mwandondomeko yotereyi, ndithudi, atha kutsogolera moyo uliwonse. Yesu anatitsimikizira ife: "Ngakhale tsitsi la mmutu mwanu liwerengedwa ndi ine. Chotero musaope" (Mateyu 10:30-31).

Mphatso ya Mulungu ya chikhulupiriro itha kukhala mankhwala a mavuto, madandaulo ndi mantha athu. Chiyembekezo chomwe amachitakasa chitha kukhala mzati wa mitima yathu (Ahebri 6:19).

Wophunzira wa mzaka zamazana khumi mphambu zisanu ndi limodzi (16th Century), Erasmus analongosola zomwe zinachitika pa ulendo wa panyanja zomwe sadaziiwale moyo wake wonse. Sitima yake inavutika ndi kuonongeka ndi mafunde. Pamene mafunde a ukali anamenya pa Sitima yake niyamba kuphwanyika, ngakhale oyendetsa sitimayo anaopa okwera nawo anali pafupi kuyamba kukomoka Ena nafuula kufuna chithandizo kwa owayendetsa, poimba nyimbo zotamanda za uzimu, ndi kupemphera mofuula.

Erasmus anaona munthu mmodzi woyenda nawo m'sitimayo, yemwe anachita mosiyana ndi ena onse. "Mwa ife tonse," Erasmus analemba, "mmodzi yemwe sanaonetse kugwedezeka anali mkazi wachisungwana yemwe anali ndi mwana yemwe amamusamalira. Ndiyekhayo yemwe sanafuule nafe, kapena kulira, kapena kukambirana ndi kumwamba. Sanachite kena kalikonse koma kupemphera mwachete kwa iye yekha uku akumugwira mwana wake momufungata pa chifuwa pake."

Pemphero iri, Erasmus anazindikira, kuti linali kupitiriza mapemphero omwe mayiyu anali kuchita nthawi zonse m'moyo wake. Anaonetsa wodzipereka mwa iye yekha kwa Mulungu.

M'mene Sitima inayamba kumira, msungwanayu anaikidwa pa thabwa, atapatsidwa chopalasira kuti agwiritse ntchito, natengedwa ndi mafundewo. Anamgwiritsabe mwana wake ndi dzanja limodzi ndi kusambira ndi dzanja linali. Ndi anthu ochepa omwe anaganiza kuti msungwanayu apulumuka ku mafunde woopsawo.

Koma chikhulupiro chake ndi kusagwedezeka kwake kunampanga kukhala tcheru. Iye ndi mwana wake ndiwo adali oyamba kufika ku gombe.

Chiyembekezo mwa Mulungu wodalirikayo chingabweretse kusintha konse ngakhale pamene dziko likuoneka ngati likuphwasuka motizungulira. Sitiri tokha kupalasa ngalawa ayi, pali dzanja lamphamvu likutitsogolera ndi kutigwira dzanja.

Mukabwera kwa Yesu athunthu modzipereka adzakupatsani chikhulupiriro chimene chidzakudutsitsani m'mafunde. Pezani inu mtendere wodabwitsawu umene Yesu amalonjeza.

"Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani inu… Mtima wanu usabvutike, kapena usacite mantha." - Yohane 14:27.

Kodi muli ndi mtendere umenewu? Ngati ndi choncho, thokozani Yesu Mpulumutsi wanu. Ngati sichoncho, bwanji osamuitana iye m'moyo wanu lero?

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.