CHIKONZERO CHA MOYO WANU

Mlaliki wina atatha kulalikira pa mutu wotchedwa "CHIFUKWA CHOMWE NDIKHULUPIRIRA MWA YESU", munthu wina wovala mooneka bwino, wamwamuna anamuyendera wolalikirayu kukamuchezera mukuwerenga ndi kuphunzira kwake, ndipo anapereka ndemanga yakuti, "Uthenga wanu usiku uja unali wopatsa chidwi, koma zonse zomwe mumanena zimachokera mu baibulo lanu, zokhuza Yesu khirisitu, Ndiuzeni ine ngati Yesu anadzakhaladi mdziko lino lapansi? Nanga chifukwa chiyani mbiri iriyonse siyinena za Iye?"

"Funso labwino limenelo," Anatero wolalikirayu yemwe anatembenuka natenga mabukhu angapo, nati, "Kunena, zoona mbiri ikunenapo za Yesu Khristu".

M'nyamatayu anayankhanso nati, "Izi ndikufuna nditaziona ndekha".

(Chabwino, tenga iyi yomwe iri kalata ya panambala makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi ziwiri (97) ya mubukhu la chachikhumi la Pliny wang'ono, woyambirira wachiroma ku Bithynia, dela lina la ku Asia Minor. Pliny analembera kwa mfumu wa Roma, Trajan, kumuuza za zomwe zichitike m'derali: Onani, apa akufunsa nzeru za mmene angachitire ndi kagulu katsopano, ka a khristu akunena za mmene kagulu kameneka kakuchulukirira mofulumira ndi momwe akuyimbira nyimbo zao mwanthenthemya zophunzitsidwa ndi atsogoleri awo. Kalatayi ikuonetsa mbiri yonse ya umboni wa mbiri ya munthu, Khristu ndi kulalikira kwa chikhulupiriro chake mnthawi ya masiku atumwi ake".

Modabwa m'nyamatayu anati, "ndiuzenibe Zambiri!" Pamene mbusayu amaloza ndi chala chake mizere ya mau yomwe amawerenga m'bukhu linanso, anaonjezera kunena yomwe amawerenga m'bukhu linanso, anaonjezera kunena kuti; " Wolemba za mbiri yakale winanso, mogwirizana ndi Pihiny, anali Tacitus, mtimabukhu take ting'onoting'ono, ( Bukhu la chikhumi ndi chisanu, (15), mutu wa makumi anayi mphambu zinayi (44) akunena za udani wa mfumu Nero womwe anali nawo pa akhristu omwe adaphetsa akhristu nthawi yomwe Roma anadya moto. Tacitus kuti liwu loti "mkhristu" likuchokera ku dzina la "khristu". Akunenaponso kuti Yesu Khristu, yemwe adayambitsa chipembedzo cha chikhristu, anaphedwa ndi mfumu Pilato, wolamulira woweruza wa mu Yudeya, munthawi ya mfumu Pilato, wolamulira woweruza wa mu Yudeya, munthawi ya mfumu Tiberius. Zonsezitu Zomwe Tasita akutipatsa m'bukhuli zikugwirizana ndendende ndi zonse zochitika , maina ndi malo omwe apatsidwa mu Baibulo".

"Abusa, ndinali ndisanamvepo kuti zinthu ngati zimenezi zikupezeka mu mbiri yakale ya dziko lapansi!" Mlendoyu adafuula.

Mbusayu adapitiriza nati, "ndikufuna uwone kuti pafupifupi mu AD 180, Celsus analemba bukhu lotsutsa akhrisitu, kuonetsera kuti chikhristu munthawiyo chinali ngati chokakamiza kuchitsata". "Ngati ukukayikabe, kumbukira kuti mabukhu amauthenga abwino anayi aja a m'chipangano chatsopano ali ndi mbiri yakale ngati bukhu lina liri lonse la mbiri yakale".

Pamene mnyamatayu anazindikira kuti bukhu lopatulika ndi mbali zake komanso mabukhu wamba akugwirizana kuti Yesu anakhalapo monga munthu pa dziko lapansi, anapita wokhutitsidwa kuti Yesu Khristu alipodi weniweni, woonetsedwa mu mbiri yakale.

1. KHRISTU ANAYAMBA KUKHALAKO KUYAMBIRA KALE LOSAONEKALO

Yesu sanangokhala kokha munthu wabwino ayi, analinso Mulungu. Kodi Yesu adapanga chiyani yekha chokhudzana ndi Umulungu?

"Mukadazindikira Ine mukadadziwa Atate wanganso, kuyambira tsopano mumzindikira Iye, ndipo mwamuna Iye,... Iye amene wandiona Ine waona Atate." - Yohane 14:7-9.

"Mulungu ndi ndani? nanga amaoneka bwanji?" Yang'anani kwa Yesu basi, yemwe ananena,

"Ine ndi Atate ndife amodzi." - Yohane 10:30.

Mulungu Atate ndi, Mulungu Mwana, akhala aliko limodzi kuyambira kalekale (Aheberi 1:8). Palibe nthawi yomwe Yesu anakhala yekha wopanda Atate. Mulungu Atate amachita mwa chikondi ndi chisamaliro chimodzimodzi monga chomwe Yesu anaonetsera mu moyo wake wonse pa dziko lapansi.

2. KHRISTU, MTIMA WA MBIRI YAKALE NDI ULOSI

Pakuti mbiri ya moyo wa Khristu imakwaniritsa ulosi, mbiri yakeyinso inalembedwa Iye asanabadwe. Ulosi wa mu chipangano chakale umaonetseratu ndondomeko yonse ya moyo, imfa ndi kuuka kwa Yesu. Chipangano chatsopano ndiye moyo wakewo mokwanirirtsa zomwe zinaloseredwazo.

Aneneri a chipangano chakale omwe adakhalako zaka pafupifupi kuyambira mazana asanu mpaka chikwi ndi mazana asanu Yesu Khristu asanabadwe, amaonetseratu molosera za moyo wonse wa Mesiya. Ndipo pachiyambi penipeni pa utumiki wa Yesu Khristu pa dziko lapansi, pamene anthu amafananitsa moyo wake ndi ulosi womwe udalipo wa Iye, kodi adafika pa mfundo yomaliza yamtundu wanji?

"Iye amene Mose analembera za Iye m 'chilamulo, ndi aneneri, tampeza, ndiye Yesu mwana wa Yosefe wa ku Nazarete." - Yohane 1:45.

Mpulumutsi wathu anaonetsa momwe Iye aliri ndi ntchito yake kupyolera mu ulosi wokwaniritsidwawo.

"Ndipo anayamba ndi Mose, ndi kwa aneneri onse, nawatanthauzira iwo m 'malembo onse (chipangano chakale) zinthu za Iye yekha". - Luke 24:25-27.

3. MOYO WA KRISTU, KUKWANIRITSA ULOSI

Tiyeni tiwone angapo a maulosiwa momwe aliri mu chipangano chakale, ndi mmene akwaniritsidwira mu chipangano chatsopano.

MALO AKE OBADWIRA
Ulosi wa m 'chipangano chakale:
"Koma iwe, BETELEHEMU Efrata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda. Mwa iwe mudzanditurukira wina wakudzakhala woweruza m'Israyeli; maturukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba." - Mika 5:2.
Kukwaniritsidwa kwa ulosiwu m'chipangano chatsopano:
Kukwaniritsidwa kwa ulosiwu m'Betelehemu wa Yudeya." - Mateyu 2:1.

KUBADWA KWAKE MWA NAMWALI
Ulosi wa m'chipangano chakale: "Taonani Namwali adzaima, nadzabala mwana wa mwamuna, nadzamucha dzina lake Imanueli? (Mulungu Nafe)." - Yesaya 7:14.
Kukwaniritsidwa kwa ulosiwu m'chipangano chatsopano:
"Yosefe, Mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti ICHO CHOLANDIRIDWA MWA IYE CHIRI CHA MZIMU WOYERA. Ndipo adzabala mwana wamwamuna ndipo adzamucha dzina lache Yesu (Ambuye anapulumutsa)" - Mateyu 1:20-23.

KUMENE IYE ANACHOKERA MU PFUKO LA YUDA
Ulosi wa m 'chipangano chatsopano:
"Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda,… kufikira atadza Silo, ndipo anthu adzamumvera iye." - Genesis 49:10.
Kukwaniritsidwa kwa ulosiwu m'chipangano chatsopano:
"Pakuti kwadziwikadi kuti, Ambuye wathu anatuluka mwa Yuda." - Aheberi 7:14.

KUKANIDWA KWAKE
Ulosi wa m'chipangano chakale:
"Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu." - Yesaya 53:3. Kukwaniritsidwa kwa ulosiwu m'chipangano chatsopano:
"Anadza kwa zake za Iye yekha, ndipo ake amwini yekha sanamlandira Iye." - Yohane 1:11.

KUPEREKEDWA KWAKE NDI MTENGO WA MALIPIRO APATSIDWA
Ulosi wa m'chipango chakale.
"Ngakhale Bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira , ndiye amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidende chake." - Masalimo 41:9.

"Ndipo ndinanena nao, 'Chikakomera inu ndipatseni mphoto yanga; ngati iai, lekani. Ndipo anayesa mphoto yanga, kulemera kwake NDARAMA ZASILIVA MAKUMI ATATU." - Zakariya 11:12.
Kukwanitsidwa kwa ulosiwu m'chipangano chatsopano:
"Pomwepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo, dzina lake Yudase Isikariote, anamuka kwa ansembe akuru, nati, mufuna kundipatsa chiani, ndipo ine ndidzampereka Iye kwa inu? Ndipo iwo anawerengera Iye NDARAMA ZASILIVA makumi atatu." - Mateyu 26:14, 15.

IMFA YAKE PAMTANDA
Ulosi wa m'chipangano cha kale:
"Andi boola m'manja anga ndi m'mapazi anga." - Masalimo 22:16.

Kukwaniritsidwa kwa ulosiwu m'chipangano chatsopano:
"Ndipo pamene anafika ku malo dzina lake Bade, Anampachika Iye." - Luka 23:33 (onaninso pa Yohane 20:25).


KUCHOKA KWAKE M'MANDA
Ulosi wa m'chipangano chakale:
"Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda; simudzalola wokondedwa wanu abvunde." - Masalimo 16:10.
Kukwaniritsidwa kwa Ulosiwu m'chipangano chatsopano:
"Iye pakuona ichi kale, analankhula za kuuka kwa Kristu, kuti sanasiyidwa m'hade, ndipo thupi lake silinaone chibvundi. Yesu ameneyo, Mulungu anumuukitsa, za ichi tiri mboni ife tonse." - Machitidwe 2:31, 32.

Umboni wokwanira ndi wamphamvu woti Yesu sanangopezekamo m'maulosiwa ayi. Mbiri ya moyo wake inalembedwadi kale kale chisanakhazikitsidwe chiri chonse. Zoona, Yesu ndi mwana wa Mulungu.

Titatha kuona umboniwu, tiyenera kupemphera popanga chisankho cha amene ayenera kukhala Ambuye wa moyo wathu. Ngati simunachite izi, kodi mungatero, kuika moyo wanu m'manja mwake?


4. MOYO WOKONZEDWERATU NDI MULUNGU

Yesu anakhala moyo womwe udali wokonzedweratu ndi Mulungu Zaka zambiri mbuyomo ye asanabadwe. Pokhudzidwa ndi izi, Iye anakhala woganizira mwakuya pochita momwe Mulunguyo adamutsogolerera. Khristu anati:

"Ndipo sindicita kanthu kwa Ine ndekha, koma monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi,... chifukwa ndichita Ine zimene zimukondweretsa Iye nthawi zonse." - Yohane 8:28-29.

Mulungu adakonzeratu moyo wa umunthu wa Yesu Khristu iye asanabadwe, ndi amakonzeratunso chimodzimodzi moyo wamunthu ali yense. Amadziwa mmene aliyense waife angakwanitsire zilakolako zake zakuya ndi kupeza moyo wathunthu.

Ray sanafike podziwa motsimikiza kwenikweni kuti apereke moyo wake kwa Mulungu. Koma atafika posankha za sukulu ya ukachenjede yomwe adayenera kupita, adafunsa chitsogozo cha Mulungu kwa nthawi yoyamba. Anapemphera kwa masiku angapo kudikira yankho. Patapita nthawi adafika pa chitsimikizo kuti ali ndi zifukwa zokwanira kusankha mbali B ya zomwe adayenera kusankhazo. Mbaliyi inali kunena za sukulu yochipa koma yaikulu kwambiri. Atapita ndipo atangoyamba kumene maphunziro ake adazolowerana kwambiri ndi a khrisitu ena ozizwitsa omwe anali a bungwe lina la pa sukulupo lotchedwa 'Ankhondo A Khristu'. Zomwe anapeza pokhala nawo kwa zaka ziwiri zinasintha moyo wake modabwitsa.

Pamene Ray ankayang'ana moyo wake wambuyo, anapeza kuti nthawi zonse ankapezana ndi chisankho chachikulu choti apange mwachitsimikizo napempha mphamvu za umulungu kuti zimutsogolere, "Mulungu anatsegula zonse zatsopano za m'moyo wanga".

Kodi mungadziwe bwanji chikonzero cha Mulungu pa moyo wanu? Mulungu akutitsogolera mu njira zingapo:

(1) BAIBULO
"Mau anu ndiwo nyali ya kumapazi anga ndi kuunika kwa panjira panga." - Masalimo 119:105.

Wolemba masalimoyu wapeza choncho kuti bukhu lopatulika ndiye chitsogozo.

Mawu a Mulungu amakonzanso mwatsopano maganizo athu ndi kutipatsa chidziwitso (Aroma 12:12, Masalimo 119:99). Kuwerenga mauwa ndi kupemphera nthawi zonse ndiye njira yoposa zonse popezera zofunika zenizeni m'moyo wathu.

(2) NJIRA ZA ZOCHITIKA MOTIPATSA
Mulungu amatitsogoleranso potionetsera zochitika zoyera zotitsogolera. Masalimo 23 akumuonetsera Iye ngati mbusa wabwino. Mbusa amatsogolera nkhosa zake mzigwa zoopsa ngakhalenso mmatanthwe ovuta. Amatha kuthandiza mntchito zake kuti zipindule ndi kuphunzitsa. Tiri ndi m'busa ife amene amakhala pafupi nafe nthawi zonse.

(3) KULANKHULANA KWACHINDUNJI NDI MTIMA KOMWE
MULUNGU AMACHITA

Mulungu amatitsogoleranso poyankhula ndi maganizo athu a umunthu. Mzimu utha kutionetsera "maso athu a mumtima" (Aefeso 1:18). Nthawi zonse pamene tilumikizana ndi Mulungu, ndipamenenso amatha nayenso kutitsogolera. Anaumba zonse zathu, maganizo a mkati mwamtima wathu kuti tiwone choyenera chenicheni kuti tingachite nthawi zonse.

5. ZITSOGOZO ZIYENERA KUGWIRIZANITSA

Ndizotheka, ndithu, kuona ngati ukuyenda mmoyo wotsogozedwa ndi Mulungu pamene ukungotsatira za iwe mwini (Miyambo 16:25). Zofuna zathu ziyenera kugwirizana ndi ziphunzitso za mu baibulo. Sichanzeru kungoganiza Mulungu akutsogolera pokhapokha titaona kuti mitu itatu iri mwambayo ikuyendera limodzi.

Tamuoneni, mwachitsanzo, munthu uyu wotchedwa Jake. Anali ndi mkazi wake wokondeka ndi ana awiri, koma analinso ndi mkazi wina kumbali. Anawauza anzake: "Ndapemphera kwa Mulungu za izi ndipo ndikuona kuti ichi ndi chifuniro chake".

Maganizo a Jake ndi "Kumva kwake kwa mumtima" kumamutsogoza kunjira yolakwika. Iye anaona ndi kuganizira kuti chinali "chopatsidwa" kuti iye akumane ndi mkazi winayu ndipo sanabwererenso kukawerenga zomwe baibulo likunena ayi, pa za chigololo. Ndipo Baibulo, "ku chilamulo ndi umboni , ndilo bukhu lololedwa kutitsogolera, loyenera kutiuza choyenera chenicheni kuti tichichite (Yesaya 8:20).

Tisalole maganizo ena aliwonse kapena choperekedwa kwa Iye chiri chonse kutitsogolera kuntchito motsutsana ndi mawu a Mulungu.

6. KUDZIPEREKA KU CHIKONZERO CHA MULUNGU

Yesu atalandira satana kuti amuyese m'chipululu, anamuonetsera izi, "ngati ungachite modzipereka podzipereka nsembe yopweteka yomwe Atate wakukonzera Iwe, ndidzakupatsa dziko lonse lapansi m'dzanja lako udzachuka, udzakhala wamwayi, ndi moyo wofewa udzakhala ndi Iwe". Satanayo anapereka umboni ndi mawu a m'bukhu lopatulika kuyesetsa kuti amusocheretse Yesu. Koma nthawi zonse Yesu anamugonjetsa ndi mawu akuti " kwalembedwa" (Mateyu 4:1-11).

Phunziro lalikuru ndi lamphamvu lomwe tikuphunzira apa ndi moyo wa Yesu Khristu ndi lodzipereka ku chifuniro cha Atate. Ngakhale mkati mwa zowawa za Getsemane, iye analira nati, "Atate ngati nkotheka, chikho ichi chindipitirire, osati mwa kufuna kwanga ayi, koma mwa kufuna kwanu" (Mateyu 26:39). Patapita zaka zitatu za utumiki wake pokhala tsiku ndi tsiku mu mgwirizano ndi chikonzero cha Atate wake, Mawu omwe adayankhula pakufa anati, "Kwatha" (Yohane 19:30). Yesu apa amanena kuti, Chikonzero cha Atate pa moyo chafika kumapeto ndipo chakwaniritsidwa".

Pamene muyamba kumva liu la Mulungu kuyankhula nanu mosalekeza ndi mogwirizana m'mawu ake, zomwe watipatsa, ndi zokwaniritsa zake, mutha inu kuphunzira kumulandira ndi mtima wanu wonse mu ziphunzitso zake. Inunso mutha kupeza chisangalalo cha chikonzero ndi chitsogozo cha Mulungu pa moyo wanu.

Nthano zonse zanenedwazi zikupezeka mu zolemba za mpingo wa khristu momwe muli nthano za mbiri ya mpingo wakale.

 

© 2003 The Voice of Prophecy Radio Broadcast
Los Angeles, California, U.S.A.