TINGATHE KUKHULUPIRIRA MWA MULUNGU Nthawi ina Jim anafunsa munthu wosakhulupirira kuti kodi kuli Mulungu? Ngati anayamba waganiza mozama ngati kunjakuno kuli Mulungu kapena ai. 'Mwachuchuchu', munthuyu anati kwa Jim "zaka za m'mbuyomu pamene mwana wathu woyamba anabadwa; ndinatsala pang'ono kukhulupirira kuti Mulungu aliko; poona kanthu kakang'ono kangwiro mu kama wake; tizala take tikugwedera ndi timaso take tikuphethira. kwa miyezi ingapo ndinali pafupi kusintha maganizo anga akuti kumwamba kulibe Mulungu" Izi zinamudabwitsa Jim. "Pokaona kamwanako, ndinatsala pang'ono kukwanitsidwa kuti kuyenera kukhala Mulungu". Anapitiriza motero. 1.
CHOPANGIDWA CHIRICHONSE CHIRI NDI OCHIPANGA WACHE Makina a kompyuta amagwira ntchito yonga iyi komabe zimatengera maganizo a munthu kupanga makina ngati amenewa. Nzosadabwitsa
kuti wolemba masalimo anafika ponena kuti thupi la munthu limanena momveka
bwino komanso mofuula za mlengi wozizwitsa:- "Ndikuyamikani cifukwa kuti cipangidwe changa nchoopsa ndi chodabwitsa: Ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu." - Masalimo 139:14. Sitiyenera kupita kutali kuti tipeze ntchito za Mulungu Mmene ubongo wa munthu ndi ziwalo zina za thupi lake zinapangidwira zimalozera kunzeru zosafikirika za luso za ntchito ya Mulungu. Palibe chopopera chiri chonse chopangidwa ndi munthu chingayerekezedwe ndi mtima wa munthu. Palibe mgwirizano wa mauthenga odzera mu makina a kompyuta womwe ungapose ngwirizano wa bongo ndi ziwalo zonse za thupi. Palibe ngwirizano wa mmene wailesi ya kanema igwirira ntchito yake womwe ungapose mmene munthu ayankhulira kumvera ndi kuona. Palibe makina obweretsa mphepo yabwino kapena kutentha Munthawi yozizira omwe angapose ntchito ya mphuno ndi khungu. Mmene thupi lamunthu liliri malukidwe ake ndikugwirizana kwake zimasonyeza kuti wina wake analipanga motero; ndipo wolipangayo ndiye Mulungu. Thupi lamunthu ndi lathunthu zochitika za ziwalo zonse ndi zogwirizana mu ntchito zawo ndiponso zinapangidwa mosamalitsa. Mapapo ndi mtima; minofu ndi zotenga mauthenga kuchoka ndi kupita kuubongo; zonse ndi zogwirizana pa ntchito zofunika zosokonezeka kuzimvetsetsa kwake; zomwe zifunikanso zipangizo zofanana nazo. Mutatenga ndalama zachitsulo khumi ndikuika chizindikiro pa iri yonse ndi kuziika mthumba lanu ndikuzisakaniza mmenemo; ndipo nimuziturutsa, komanso nimuyamba kuzibwezeramo iriyonse payokhapayokha; kodi mwayi ulipo wotani kuti zibwezeredwemo mwandendende, kufanana ndi mmene zinaikidwira poyamba. Ai ndikwapatali kuti zitero. Potsatira lamulo la masamu, mwina mwayi ulipo umodzi basi pa kuyesa kwa zikwi zikwi kuti zingaikidwe mundondomeko yake. Ndiye inu onani mwayi wa mimba, ubongo, mtima, chiwindi, njira za magazi, impyso, makutu, maso ndi mano zonse kukulira limodzi; kuyamba kugwirira ntchito limodzi; ndi nthawi imodzi. Kutheka kwa zonse ndi chinsinsi cha Mulungu. Ndiye pamenepa, tingalilongosole bwanji momveka thupi la munthu ndi mapangidwe ake? "Ndipo anati Mulungu, tipange munthu mchifanizo chathu monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pa nsomba za m'nyanja, ndi pa mbalame za m'mlengalenga, ndi pa zonse zakukwawa pa dziko lapansi. Mulungu ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adalenga iwo mwamuna ndi mkazi." - Genesis 1:26, 27. Mwamuna ndi mkazi woyamba sanakhale mwatsoka ayi koma mwa chilinganizo. Bukhu Lopatulika likutsimikizira kuti Mulungu anawapanga iwo muchifanizo chake. Anatiganizira natipanga kuti tikhaleko. 2. CHIRICHONSE CHOPANGIDWA CHIRI NDI WOCHIPANGA Chotsimikizira kuti kuli Mulumgu sithupi la munthu lokha ayi. Zafalikira mpaka pa za kumwamba. Onani m'mene mlengalenga mumaonekera usiku. Mitambo yowundana pamwamba pa nyenyezi ndi njira zake zopangidwa ndi gulu la nyenyezi zikwi zikwi zowala ndi dzuwa lofanana ndi lathu lomwe tilidziwali. Dzuwa lathu ndi maiko ake lizungulira ndi mbali imodzi miyanda miyanda ya nyenyezi zowala kwambiri zomwe zingaonedwe pansi pano ndi makina otchedwa "Telescope" amphamvu kwambiri, kapena " Hubble Telescope" Mumlengalenga. Nzosadabwitsa kuti wolemba masalimo anafika ponena kuti, nyenyezi zimanena za ulemelero wa Mulungu. "Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetse ntchito ya manja ache." - Masalimo 19:1-3. Nanga tingabwere ndi maganizo anji poona mapangidwe odabwitsa ndi kukula kwake kwa dziko lapansi? "Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi." - Genesis 1:1. "(Mulungu) ali woyamba wa zonse, ndipo zonse zigwirizana pamodzi mwa iye." - Akolose 1:17. Zolengedwa zonse zichitira umboni Mulungu mwini wakuzipangayo. Mu mawu ena. "Pachiyambi Mulungu" tingawatanthauzire mosabvuta kuti tipezamo mayankho a zodabwitsa za m'moyo. Pali Mulungu amene analenga zonse. Maganizo ambiri a akatswiri a zofufuza lero amakhulupiriranso kuti kuli Mulungu. Dr. Arthur Compton, yemwe anapeza mphotho pa zaukatswiri wake; ponenapo za vesi la m'bukhu lopatulikali anati; Kwa ine ndimakhulupira kuti nzeru zodabwitsa zazikulu ndi zakuya zimabweretsa zinthu zomwe kunalibe, kukhalapo ndizomwezonso zinalenga munthu. Izi sizobvuta kwa ine kukhulupirira podziwa kuti paliponse pali cholengedwa pali Mlengi. Dziko lapangidwa mwa ndondomeko lichitira umboni ku coonadi cha mau oposa awa akuti, (PACHIYAMBI MULUNGU"). Bukhu lopatulika silikufufuza kuti lipeze zoona zake za Mulungu ayi, koma likunena za kukhalako kwake. Dr. Arthur Conklin, katswiri wodziwika pa zamoyo, analemba nthawi ina, kuti, "Maganizo oti pali mwayi woti moyo unachokera kwina kwake mwangozi angayerekezedwe ndi maganizo oti pali mwayinso woti pali bukhu lotanthauzira mawu losokonekera m'matanthauzo ake lomwe linabwera mwangozi pamene nyumba yosindikizira mabukhu inaphulika". Tikudziwa kuti munthu sangapange kanthu popanda zipangizo zirizonse. Titha kumanga zinthu, kupeza zinthu zatsopano zomwe sizinawonedwepo, kulumikiza zinthu; koma sitinabweretsepo ngakhale kanthu kakang'ono popanda kugwiritsa ntchito zipangizo. Ine ngakhale kulenga chule kapena duwa laling'ono munthu sangathe. Zinthu zomwe zitikhudza ife zimaneneranso kuti Mulungu anazipanga, anazirenga, nazipatsa umoyo wake. Yankho lenileni lokhulupirika pa chiyambi cha dziko lino lapansi, ndi anthu ake ndi - Mulungu. 3. MULUNGU AMABWERA M'CHIYANJANO NDI ANTHU Mulungu yemwe anakhazikitsa nyenyezi m'mwamba, natenga dziko lapansi, amafuna kuyanjana ndi ife. Anali m'chiyanjano chomwecho ndi Mose: (Ndipo Yehova ananena ndi Mose... monga munthu alankhula ndi bwenzi lake" (Eksodo 33:11). Ndipo Mulungu akufuna kukhala m'chiyanjano ndi inu kuti akhale bwenzi lanu. Yesu anawalonjeza omutsatira ake: "Muli abwenzi anga inu" (Yohane 15:14). Takhala tikulingalira tonse pa maganizo a za Mulungu, Pakuona munthu ndi waumulungu m'chibadwidwe. palibe nyama yomwe imanga guwa lopembedzerapo. Koma kuli konse mukapeza munthu (amuna ndi akazi) akupembedza. Mumtima mwa munthu ali yense muli chibadwidwe chakufuna kupembedza; kusonyeza kuzindikira kuti Mulungu aliko, ndi kufuna kukhala bwenzi lake. Tikafunafuna motere ndi kumupeza Mulunguyo, sitikayikanso zakuti aliko ndi kumufuna kwathu. Mu zaka za mu ma 1990, zikwi zikwi za anthu osakhulupira kuti kuli Mulungu m'dziko la Russia anasiya kusakhulupirira kwawo natembenukira kwa Mulungu. Mphunzitsi wina wamkulu wa pa sukulu ina ya ukachenjede, St. Petersburg, ananena mau omwe anasonyeza anagwirizana ndi ganizo loti kunja kuno kuli Mulungu. Iye anati "Ndafufuza tanthauzo la moyo mu ntchito yanga ya zofufuza, koma ndapeza zonse zosadalirika.. Anzanganso muntchitoyi sanapeze kanthu. Poyang'ana ukulu wa dziko lapansi ndi mmwamba ndi kuyerekeza ndi kuperewera kwa mzimu wanga; ndinamva china chake chosonyeza kuti payenera kukhala chinthu china cake chatanthauzo, ndipo nditalandira bukhu lopatulika ndikuwerenga, kuperewera kwanga kunakwanitsidwa tsopano m'moyo mwanga. Ndapeza kuti Bukhu lopatulika ndiye muli chilimbikitso cha moyo wanga. Ndamulandira Yesu kukhala mpulumutsi wanga ndipo ndapeza mtendere weni weni ndipo ndakhutitsidwa mu moyo wanga". Mkhrisitu amakhulupirira mwa Mulungu chifukwa iyeyo wakumana naye ndikupeza kuti iyeyo amakwaniritsa zofuna za mtima wa munthu zenizeni. Mulungu, yemwe okhulupirira amupeza mokondwera kuti aliko, amatipatsa ife maganizo atsopano, matanthauzo atsopano, zolinga zatsopano ndi zisangalalo zatsopano. Mulungu salonjeza moyo wopanda mavuto ndi zipsinjo ayi; koma alonjeza motitsimikizira kuti atsogolera ndi kutisungabe ife tikakhala naye m'chiyanjano. Miyanda miyanda ya akhirisitu idzachitira umboni kuti kuli bwino kusiya zonse ndi kukhala m'chiyanjano ndi Mulungu koposa kubwerera njira zakale zopanda Mulungu m'moyo. Chodabwitsa
chachikulu cha zonse ndi chakuti Mulungu wathu ndi Mlengi wathu amene
amasunga ndi kuyang'anira dzikoli amafunanso kukhala m'chiyanjano ndi
munthu aliyense, wamwamuna kaya wamkazi; mnyamata kapena mtsikana. Davide
anakondwa ndi mawu awa pomwe analemba kuti:- Mlengi wathu "amakumbukira" wina aliyense waife. Amakhala ndi chidwi ndi munthu aliyense payekhapayekha ngati kuti munthuyo alipo yekhayo basi yemwe anamulenga. Choncho
titha kukhulupirira mwa Mulungu:- 4.
KODI IYEYU NDI MULUNGU WA MTUNDU WANJI Kodi Mulungu adagwiritsa ndondomeko yanji polenga amuna ndi akazi? "Mulungu
ndipo adalenga munthu m'chifanizo chake, m'chifanizo cha Mulungu adalenga
ife; adalenga iwo mwamuna ndi nkazi." - Genesis 1:27. Pokhala olengedwa m'chifanizo cha Mulungu, mwayi wathu wakuganizira, kumva, kukumbukira ndi chiyembekezo, kuona ndi kutanthauzira - zonse zichokera kwa Iye. Kodi khalidwe lenileni la Mulungu ndilo liti? "Mulungu ndiye chikondi." - 1 Yohane 4:8. Mulungu amadzilunzitsa ndi anthu achikondi, palibe chomwe anachita kapena adzachita choposa icho chosonyezera chikondi chake chodzipereka. 5. MMENE YESU AONETSERA MMENE MULUNGU ALIRI Mubukhu lopatulika, Mulungu ananena za iye yekha ngati atate. "Kodi
sitili naye atate mmodzi ife tonse? Sanatilenga kodi Mulungu Zifanizo
zina za utate wake zomwe tiziona lero nzoyenera kuzisirira Atate wathu wokonda ankafuna kuchita moposera kudziulula yekha mu mawu ake oyera. Ankadziwa Iye kuti munthu yemwe tikhala naye ali weniweni osati wongomumva kapena kumuwerenga mu bukhu ayi. Ndiye anadza ku dziko lino ngati munthu weniweni - munthu mwa Yesu. "(Yesu) ali fanizo la Mulungu wosaonekayo." - Akolose 1:15. Ndiye ngati mwaona Yesu, mwaona Mulungu. Anadza mooneka ngati ife - nakhala monga ife - kuti atiphunzitse mmene tiyenera kukhalira ndi kukhala okondwa; kuti tikathe ife kuona momwe aliri Mulungu. Yesu ndi Mulungu wopangidwa woonekayo. Iye anati, "Iye amene wandiona Ine waona Atate" (Yohane 14:9). Pamene muwerenga mbiri ya Yesu mu mauthenga abwino anayi, omwe ndi mabukhu oyambirira anayi a chipangano chatsopano, mupeza maonekedwe oonetsa kuti Mulungu ali Atate wathu wakumwamba. Asodzi aukali anasiya maukonde awo namutsata Yesu Khrisitu; ena anamuthamangira kuti akalandire madalitso. Atatha kusangalatsa wochimwitsitsa ndi kumuchepetsa uyo wodziyesa wolungama monyenga. Anachiza matenda ali wonse kuyambira ku khungu mpaka ku khate. Muntchito zake zonse, Yesu anaonetsa kuti Mulungu ndi chikondi ndipo wakhala ali chikondi chaulemerero, Yesu anafika pachimake poonetsa chikondi cheni cheni cha Mulungu pa mtanda. "Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa mwana wake wobadwa yekha kuti yense okhulupirira iye asatayike koma akhale nawo moyo wosatha." - Yohane 3:16. Yesu anafa osati kuti atipatse moyo wokondwa wa nthawi ino yokha ayi, komanso moyo wosatha. Kwa nthawi yaitali anthu akhala akuzizwa, kuyembekezera ndi kuganizira za Mulungu. Akaona chilengedwe chake padziko ndi kumwamba chiri chokongola. Koma pamtanda, Yesu anaphwanya zonsezi, nawapanga anthu kumuona Mulungu ndi chikondi chake chosatha maso ndi maso. Mutha kumupeza Mulungu panopa pamene Yesu akumuvumbulutsa. Kupeza uku kukupangitsani kunena motsimikiza kuti "Atate, ndikukondani".
© 2003 The
Voice of Prophecy Radio Broadcast |
|